ONANI

(Ekisodo 34:6, 7)

 1. 1. Inu Yehova, M’lungu Wamkulu,

  Wabwino m’zinthu zonse,

  Tidzakutamandani.

  Muli ndi mphamvu, chikondi, nzeru.

  Mulungu wathu ndinu.

 2. 2. Timaonanso chifundo chanu.

  Ngakhale ndife fumbi,

  Tikapempha mumamva.

  Mumatidyetsa, kutiphunzitsa,

  Mumatithandizadi.

 3. 3. Tikutamanda inu Yehova.

  Tikukuimbirani

  Mosangalala ndithu.

  Muyeneradi kutamandidwa.

  Kuchokera mumtima.