ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Yohane 14:27)

 1. 1. Tamandani Yehova,

  Wamtendereyo.

  Nkhondo adzazithetsa,

  Mwa Mwana wake.

  Adzapambana nkhondo,

  Yachilungamo.

  Mtendere udzabwera,

  Padziko lonse.

 2. 2. Tasiya kulankhula

  Zokhumudwitsa.

  Malupanga, mikondo,

  Zonse tataya.

  Tisungabe mtendere

  Tikhululuke.

  Monga nkhosa za Yesu,

  Zamtenderedi.

 3. 3. Mtendere ndi umboni

  wa madalitso.

  Tasunga malamulo

  a M’lungu wathu.

  Timakonda mtendere,

  Tiusonyeza

  Mpaka M’paradaiso

  Wamtendereyo.