ONANI

(Afilipi 4:9)

 1. 1. M’lungu wachikondi,

  Mwalonjeza mtendere.

  Mutipatse mzimu wanu;

  Zipatso tisonyeze.

  Chikhulupiriro,

  Chimatithandizadi,

  Kukhala mabwenzi anu;

  Tili pamtenderedi.

 2. 2. Timamvetsa zinthu

  Timaona kuwala.

  Timatsogoleredwa

  Mudziko lamdima ili.

  Nthawi idzafika

  Pomwe nkhondo zidzatha,

  Dalitsani khama lathu

  Tikhale amtendere.

 3. 3. Mulitu ndi gulu,

  Kumwamba ndi padziko,

  Lomwe ndi logwirizana

  Lolengeza Ufumu.

  Mu Ufumu wanu

  Nkhondo mudzazithetsa.

  Tidzakhala mwamtendere

  Padziko kwamuyaya.