ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 19)

 1. 1. Yehova ntchito zanu n’zambiri,

  Zakumwamba zitamanda inu.

  Chilengedwe chinena za inu;

  Ngakhale sichitulutsa mawu.

  Chilengedwe chinena za inu;

  Ngakhale sichitulutsa mawu.

 2. 2. Nzeru yeniyeni ndi yabwino,

  Imateteza okuopani.

  Mfundo zanu zoposa golide​—

  N’zothandiza ana ndi akulu.

  Mfundo zanu zoposa golide​—

  N’zothandiza ana ndi akulu.

 3. 3. Kudziwa inu n’kothandizadi,

  Mawu anu, amapatsa moyo.

  Oyeretsa dzina lanu onse,

  Mudzawapatsatu madalitso.

  Oyeretsa dzina lanu onse,

  Mudzawapatsatu madalitso.