ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(1 Petulo 1:22)

 1. 1. Tikakhala ndi chikondi,

  Timasangalatsa M’lungu.

  Mulungu ndiye chikondi,

  N’zosangalatsadi.

  Nafe timakonda ena,

  Timapezadi mabwenzi.

  Chikondi chenichenidi,

  Tizichisonyeza.

  Ena akavutika,

  Tidzawathandiza mwamsanga.

  Tidzakhalatu bwenzi,

  Lomwe limamvetsadi.

  Yesu anatisonyeza,

  Chikondi cha M’lungu wathu,

  Chimatikhudzadi mtima.

  Tizikonda anzathu,

  Kuchokera mumtima.