ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Yesaya 55:1-3)

 1. 1. M’lungu ndi chikondi.

  Amatikonda kwambiri.

  Anaperekatu Yesu

  N’kuwombola anthu tonse,

  Timayembekezeranso

  Moyo wosangalatsadi.

  (KOLASI)

  Inu nonse a ludzu,

  Dzamweni kwaulere.

  Madzi opatsa moyo;

  Mulungu n’chikondi.

 2. 2. M’lungu ndi chikondi.

  Ntchito zake ndi umboni.

  Wasonyezanso chikondi,

  Popatsa Yesu Ufumu.

  Ufumu wa Yesu pano.

  Wayamba kulamulira.

  (KOLASI)

  Inu nonse a ludzu,

  Dzamweni kwaulere.

  Madzi opatsa moyo;

  Mulungu n’chikondi.

 3.  3. M’lungu ndi chikondi.

  Nafenso tichisonyeze.

  Pothandiza ’nthu ofatsa,

  Kusungatu malamulo.

  Timamvera M’lungu wathu,

  Tilalikira konseko.

  (KOLASI)

  Inu nonse a ludzu,

  Dzamweni kwaulere.

  Madzi opatsa moyo;

  Mulungu n’chikondi.