ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Machitidwe 17:7)

 1. 1. Yehova ndi M’lungu wopanda tsankho.

  Amasamalira mosakondera.

  Amapatsa mvula,

  Ngakhalenso dzuwa;

  Amatisangalatsa mtima.

  Osauka tikamawathandiza,

  Mulungu wathu tidzamutsanzira.

  Adzatidalitsa

  tikamachitira,

  Ena zinthu mokoma mtima.

 2. 2. Pothandiza ena sitingadziwe

  Madalitso omwe tingalandire.

  Angakhale anthu

  achilendo ndithu,

  Tiwapatse zosowa zawo.

  Monga Lidiya wa m’nthawi yakale,

  Akabwera kwathu tiwalandire.

  M’lungu amadziwa

  onse om’tsanzira,

  Pochitira ena chifundo.