Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

MITU YA NKHANI

Mboni za Yehova

Chichewa

Imbirani Yehova Mosangalala

 NYIMBO 10

Tamandani Yehova Mulungu Wathu

Sankhani Zoti Mumvetsere
Tamandani Yehova Mulungu Wathu
ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Salimo 145:12)

 1. 1. Tamanda Yehova M’lungu!

  Dzina lakelo lengeza.

  Chenjeza! Anthu adziwe,

  Tsiku lake layandikira.

  Walamula kuti Mwana wake,

  Akhale Mfumu padziko.

  Kauzeni anthu uthengawu,

  Ndi madalitso akenso!

  (KOLASI)

  Tamanda Yehova M’lungu!

  Lengeza kuti ndi wamkulu!

 2. 2. Tamanda, Imba mokweza!

  Mosangalala Imbani!

  Ndi mtima, woyamikira

  Tilengeza ulemerero.

  Ngakhale Mulungu ndi wamkulu,

  Koma amadzichepetsa.

  Ndi wachifundo chachikuludi;

  Amayankha mapemphero.

  (KOLASI)

  Tamanda Yehova M’lungu!

  Lengeza kuti ndi wamkulu!