ONANI
Kukula kwa Zilembo
Chithunzi

(Chivumbulutso 4:11)

 1. 1. Yehova ndinu M’lungu wamphamvu,

  Moyo, kuwala zichoka kwa inu.

  Chilengedwe chanu chilengeza;

  Za mphamvu zanu zazikulu.

 2. 2. Mumaweruza mwachilungamo.

  Malamulo anu ndi olungama.

  Tikamawerenga Mawu anu

  Timaona nzeru zakuya.

 3. 3. Chikondi chanu ndi chachikulu.

  Mumatipatsa mphatso zapamwamba.

  Za dzina ndi makhalidwe anu,

  Tilengeza mosangalala.