Pa nthawiyi n’kuti asilikali a Roma akubwerera kwawo ndipo sanawononge mzinda wa Yerusalemu. Ndiyeno panali mabanja awiri Achikhristu amene anafunika kusankha zinthu mwanzeru. Kodi iwo anamvera mawu a Yesu n’kuthawira kudziko lachilendo kusiya zinthu zawo zonse? Inali nkhani yosankha moyo kapena imfa. Zochitika zimene zikusonyezedwa m’vidiyoyi zinalembedwa m’Baibulo, ndipo ngakhale mabuku a mbiri yakale amatsimikizira kuti zinachitikadi. Pofuna kusonyeza mmene zinthu zinachitikira, malo ena ndi ena akusonyeza anthu akumenyana, komabe cholinga chathu si kungosangalatsa anthu ayi koma kusonyeza mmene moyo wa Akhristu unalili pa nthawi imeneyo.