Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  Na. 3 2017

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi zidzatheka kuti padzikoli pakhaledi chilungamo?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

“Ndikudziwa bwino kwambiri kuti Yehova adzazengera mlandu anthu osautsika. Iye adzachitira chilungamo anthu osauka.” (Salimo 140:12) Ufumu wa Mulungu udzabweretsa chilungamo padzikoli.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mulungu amaona zinthu zopanda chilungamo zimene zikuchitika padzikoli, ndipo adzazithetsa.Mlaliki 5:8.

  • Chilungamo chochokera kwa Mulungu chidzachititsa kuti anthu padzikoli azikhala mwamtendere komanso motetezeka.Yesaya 32:16-18.

Kodi Yehova amakonda kwambiri mtundu wina wa anthu kuposa wina?

Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu anadalitsa kapena kutemberera mtundu winawake wa anthu, pomwe ena amakhulupirira kuti Mulungu sakondera mtundu uliwonse wa anthu. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

“Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Mulungu amaona kuti anthu onse ndi ofanana.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • M’Baibulo muli “uthenga wabwino” wopita “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse.”Chivumbulutso 14:6.

 

Onaninso

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Kuti Tizivutika?

N’chifukwa chiyani munthu aliyense amavutika, ngakhale amene Mulungu amamukonda?

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Kodi Mulungu Analenga Dziko Lapansili Chifukwa Chiyani?

Kodi zimene Yehova Mulungu ankafuna, zoti anthu azikhala m’paradaiso, zidzachitikadi? Ngati ndi choncho, zidzachitika liti?