Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

NSANJA YA OLONDA Na. 1 2017 | Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikusangalatsani?

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi Baibulo ndi lachikale kapena ndi lothandizabe masiku ano? Baibulo limati: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.”2 Timoteyo 3:16, 17.

Nsanja ya Olonda iyi ikusonyeza kuti m’Baibulo muli malangizo anzeru komanso ikufotokoza zimene mungachite kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo.

 

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Ubwino Wowerenga Baibulo Ndi Wotani?

Kodi anthu ambiri apindula bwanji ndi kuwerenga Baibulo?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Ndingayambe Bwanji?

Pali zinthu 5 zimene zingakuthandizeni kusangalala powerenga Baibulo.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kukhale Kosangalatsa?

Kuwerenga Baibulo kungakhale kosangalatsa mukamawerenga Baibulo labwino, mukamagwiritsa ntchito zipangizo zamakono ndiponso zinthu zothandiza kuphunzira komanso mukamatsatira njira zosiyanasiyana.

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

Buku lakaleli lili ndi malangizo anzeru kwambiri.

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Sindinkafuna Kufa

Yvonne Quarrie ankafuna kudziwa cholinga chimene Mulungu anamulengera. Yankho la funsoli linamuthandiza kuti asinthe moyo wake.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

‘Mulungu Anakondwera Naye’

Ngati mumasamalira banja kapena zimakuvutani kuti muzichita zinthu molimba mtima, mukhoza kuphunzira zambiri pa chitsanzo cha Inoki.

Kusamvetsa Zinthu Kukhoza Kutipweteketsa

Uthenga wa m’Baibulo ndi wofunika kwambiri ndipo tiyenera kuumvetsa. Koma kodi tingaumvetse bwanji?

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Baibulo limafotokoza chifukwa chake timavutika komanso zimene Mulungu adzachite pothetsa kuvutika.

Zina zimene zili pawebusaiti

Kodi Nkhani za M’Baibulo Zimatsutsana?

Onani nkhani zina za m’Baibulo zimene zimaoneka ngati zimatsutsana komanso mfundo zimene zingakuthandizeni kuti mumvetse nkhanizo.