Kodi Ayuda omwe anapita ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E., analidi ochokera ‘mu mtundu uliwonse wa pansi pa thambo’?

Anthu ali ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E.

Kuwonjezera pa zimene Baibulo limanena pa Machitidwe 2:5-11, wolemba mabuku wina wa m’nthawi ya atumwi, dzina lake Philo, analemba zinthu zina zomwe zingatithandize kudziwa zambiri za anthu omwe anapita ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E.

Philo analemba kuti: “Anthu osawerengeka ochokera m’mizinda yakutali, ankabwera ku Yerusalemu. Ena ankachokera m’mayiko a kum’mawa, kumadzulo, kumpoto, kum’mwera ndipo ena ankachita kuwoloka nyanja zikuluzikulu kuti akachite zikondwerero ku Yerusalemu.” Philo anafotokozanso zimene Mfumu Agiripa Woyamba, yemwe anali mdzukulu wa Herode Wamkulu analemba m’kalata yake yopita kwa mfumu ya Roma, dzina lake Kaligula. M’kalatayi Mfumuyi inanena kuti Yerusalemu, “Ndi Mzinda Woyera . . . ndipo Ayuda ambiri ochokera m’mayiko osiyanasiyana, omwe ali pansi pa ulamuliro wa Roma, amapita ku Yerusalemu kukalambira Mulungu.”

Mfumu Agiripa inatchula madera ena amene Ayuda ankakhala. Inatchula madera monga Mesopotamiya, mayiko a kumpoto kwa Africa, Asia Minor, Girisi komanso zilumba za m’nyanja ya Mediterranean. Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Joachim Jeremias, anati: “Ngakhale kuti zimene Agiripa ananena sizikunena za maulendo opita ku Yerusalemu, zikutithandiza kudziwa kuti anthu ambiri ankapita ku Yerusalemu kukalambira Mulungu. Izi zili choncho chifukwa chaka chilichonse, Myuda aliyense ankayenera kupita ku Yerusalemu kukachita zikondwerero zikuluzikulu.”—Deuteronomo 16:16.

Kodi anthu amene ankapita ku zikondwerero ku Yerusalemu ankagona kuti?

Malo ena omwe anthu ankasamba asanalowe m’kachisi ku Yerusalemu

Chaka chilichonse, ku Yerusalemu kunkachitika zikondwerero zitatu. Zikondwererozi zinali Pasika, Pentekosite komanso Chikondwerero cha Misasa. M’nthawi ya atumwi, Ayuda masauzande ambiri ankapita ku Yerusalemu kukachita zikondwererozi ndipo ena ankachokera m’mayiko akutali kwambiri. (Luka 2:41, 42; Machitidwe 2:1, 5-11) Anthu onsewa ankafunika kupeza malo oti agone.

Ndiye kodi ankapeza kuti malo ogona? Ena ankagona kwa anzawo pomwe ena ankagona m’nyumba zogona alendo. Anthu enanso ankamanga matenti m’mbali mwa mipanda, mumzinda wa Yerusalemu. Panalinso ena omwe ankagona m’matauni oyandikira mzinda wa Yerusalemu. Mwachitsanzo, pamene Yesu anapita komaliza ku Yerusalemu, anakagona m’tauni ina yapafupi yotchedwa Betaniya.Mateyu 21:17.

Akatswiri ena anapeza malo enaake pafupi ndi kachisi, pomwe panali madamu. Akatswiriwa akuganiza kuti n’kutheka kuti pamalowa panali mabafa omwe alendo obwera ku Yerusalemu ankasambako asanalowe m’kachisi. Anapezanso mawu ena omwe analembedwa pakhoma la bafa lina. Mawuwo amanena zoti Theodotus, yemwe anali wansembe komanso mtsogoleri wa sunagoge, “anamanga sunagoge kuti anthu azikawerengerako Torah . . . Anamanganso malo ogona komanso zitsime zoti alendo osauka azigwiritsa ntchito.”