Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  December 2015

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi n’zotheka kumudziwadi Mulungu?

N’chifukwa chiyani mulungu amafuna kuti timudziwe bwino? werengani Yohane 17:3

Mulungu amafuna kuti timudziwe. N’chifukwa chake anagwiritsa ntchito mphamvu yake ya mzimu woyera pothandiza anthu kuti alembe Baibulo. (2 Petulo 1:20, 21) Choncho tikhoza kumudziwa bwino Mulungu tikamawerenga Baibulo.—Werengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16.

Baibulo limatithandiza kudziwa makhalidwe a Mulungu komanso zimene amafuna. Limafotokoza chifukwa chimene Mulungu anatilengera, zimene wakonza kuti adzatichitire mtsogolomu komanso zimene amafuna kuti tizichita. (Machitidwe 17:24-27) Choncho tinganene kuti Yehova Mulungu amafuna kuti timudziwe bwino.—Werengani 1 Timoteyo 2:3, 4.

Kodi ndi anthu otani amene Mulungu amafuna kuti akhale anzake?

Yehova amafuna kuti anthu amudziwe bwino ndipo n’chifukwa chake anatumiza Mwana wake kuti adzaphunzitse anthu zokhudza iyeyo. Choncho amathandiza anthu amene amafunitsitsa kudziwa zolondola kuti akhale otsatira a Yesu. (Yohane 18:37) Ndipo amafuna kuti anthu oterewa akhale anzake komanso azimulambira.—Werengani Yohane 4:23, 24.

Satana Mdyerekezi amaphimba anthu m’maso kuti asamudziwe bwino Mulungu. Amachita zimenezi pofalitsa mabodza. (2 Akorinto 4:3, 4) Anthu amene safuna kudziwa zolondola zokhudza Mulungu, amakhulupirira mabodza amenewa. (Aroma 1:25) Komabe pali anthu ena ambiri omwe amaphunzira Baibulo ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asapusitsidwe ndi mabodza a Satana.—Werengani Machitidwe 17:11.

 

Onaninso

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Kodi Zoona Zenizeni za Mulungu N’zotani?

Kodi inuyo mumaona kuti Mulungu amakuganizirani? Werengani nkhaniyi kuti mudziwe makhalidwe a Mulungu komanso zimene mungachite kuti mumuyandikire.

PHUNZIRO LA BAIBULO

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?

Baibulo likuthandiza anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri. Kodi inunso mukufuna kuthandizidwa?