Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  November 2015

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinkaona Ngati Zinthu Zikundiyendera

Ndinkaona Ngati Zinthu Zikundiyendera
  • CHAKA CHOBADWA: 1982

  • DZIKO: POLAND

  • POYAMBA: NDINALI NDI MAKHALIDWE OIPA KOMANSO NDINKAFUNA NTCHITO YAPAMWAMBA

KALE LANGA:

Ndinabadwira m’tauni inayake yaing’ono ya ku Poland. Tauniyi ili pafupi ndi malire a dziko la Germany. Ndinkakhala moyo wa phee, chifukwa m’tauniyi munali mafamu komanso nkhalango zambiri. Makolo anga ankandiuza kuti ndikhale mwana womvera komanso kuti ndizilimbikira sukulu n’cholinga choti ndidzapeze ntchito yabwino.

Ndinkalimbikiradi sukulu kwambiri, moti ndinapita ku yunivesite ina mumzinda wa Wrocław kuti ndikaphunzire zamalamulo. Ndili kumeneko, moyo wanga unasintha kwambiri. Ndinayamba kucheza ndi anthu osalongosoka ndipo anandisokoneza kwambiri. Poyamba ndinkakonda kuonera mpira, koma ndinayamba kuukonda kwambiri chifukwa chocheza ndi anzangawa, moti unasanduka mulungu wanga. Ndinkasapotera timu ina ya ku Warsaw, ndipo ndinkailondola kulikonse komwe inkapita. Zoti timuyo ikasewera kutali, ndinalibe nazo ntchito. Ndinkaona kuti kuchita zimenezi kunkandithandiza kuti ndipitidweko mphepo ina. Koma kumpirako tinkakonda kumwa mowa, kuledzera komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Nthawi zambiri tinkamenyana ndi masapota a timu inayo. Komatu zomwe ndinkachitazi zikanachititsa kuti ndimangidwe ndipo ngati ndikanamangidwa, tsogolo langa likanasokonekera. Pajatu ntchito ya zamalamulo imafuna kuti munthu akhale ndi mbiri yabwino.

Tinkakonda kupita kumadansi ndi kumalo azisangalalo. Nthawi zambiri tikapita kumeneko, tinkamenyana ndi anthu. Ndinamangidwapo ndi apolisi kangapo, koma ndinkangowapatsa kenakake kuti andimasule. Pa nthawiyi ndinkaganiza kuti zinthu zikundiyendera, koma pansi pa mtima ndinkadziwa kuti ndikuchita zoipa. Kuti ndisamadziimbe mlandu, Lamlungu lililonse ndinkapita kutchalitchi kuti ndikalape machimo anga.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Tsiku lina mu 2004, kunyumba kwanga kunabwera a Mboni za Yehova awiri. Atandipempha kuti ndiziphunzira nawo Baibulo, ndinavomera. A Mboniwo anandiphunzitsa zimene Akhristu enieni amayenera kuchita. Nditaona kuti si zimene ineyo ndinkachita, ndinayamba kudziimba mlandu kwambiri. Ndinkadziwa kuti ndikufunika kusiya kumwa mwauchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso kucheza ndi anthu oipa. Ndinkaonanso kuti zingakhale bwino nditasiya kuchita ndewu. Komabe, zinkandikanika kusiya makhalidwe oipawa.

Tsiku lina ndinamenyana ndi anthu ena ndipo anthuwa anandionetsa polekera. Anthuwo analipo 8 ndipo anandimenya kwambiri n’kundisiya ndili thapsa. Anandimenya kwambiri m’mutu moti pa nthawiyi ndinkaona kuti basi, kwanga kwatha. Ndinaganiza zoti ndipemphere kwa Mulungu ndipo ndinamuuza kuti: “Yehova pepani kuti sindinamvere Mawu anu.  Ngati ndingakhalebe ndi moyo, ndikulonjeza kuti ndiyambanso kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova komanso ndisintha moyo wanga.” Mwamwayi ndinapulumukadi ndipo nditachira ndinayambadi kuphunzira Baibulo.

M’kupita kwa nthawi, ndinamaliza maphunziro anga aja ndipo mu 2006, ndinasamukira ku England kuti ndikapeze ndalama zoti ndidzawonjezere maphunziro anga azamalamulo. Ndili kumeneko, ndinapitiriza kuphunzira Baibulo. Ndikukumbukira kuti nthawi ina ndinawerenga lemba lina lomwe linandifika pamtima. Lemba lake ndi la Afilipi 3:8, ndipo palembali Paulo anati: “Ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala, kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu.” Ndinkaona kuti Paulo anali ndi moyo wofanana kwambiri ndi wanga. Anachita maphunziro azamalamulo komanso anali wankhanza. (Machitidwe 8:3) Koma anaona kuti zimene ankachita zinali zopanda phindu. Paulo anasintha kwambiri n’kuyamba kutumikira Mulungu komanso kutsanzira Yesu. Nditaganizira nkhani ya Pauloyi, ndinaona kuti ntchito yapamwamba komanso kuchita makhalidwe oipa, sikungandithandize kukhala wosangalala. Ndinaonanso kuti ngati Paulo anasintha, inenso ndikhoza kusintha. Choncho ndinaganiza kuti ndisabwererenso ku Poland kukapitiriza maphunziro anga aja.

Nditaphunzira zambiri za Yehova, ndinayamba kumukonda kwambiri. Ndipo zinandikhudza nditadziwa kuti iye amafunitsitsa kukhululukira anthu amene akuyesetsa kusiya makhalidwe oipa. (Machitidwe 2:38) Nditaganizira lemba la 1 Yohane 4:16 lomwe limati, “Mulungu ndiye chikondi,” ndinazindikira kuti Mulungu amadana ndi anthu andewu.

Nanenso ndinkafuna nditakhala wa Mboni za Yehova chifukwa ndinkaona kuti amakondana kwambiri

Chinanso chimene chinandichititsa chidwi n’choti amene ankandiphunzitsa Baibulo anali ndi makhalidwe abwino. Ndinkaona kuti amayesetsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso amakondana kwambiri moti nanenso ndinkafuna nditakhala wa Mboni. Ndinayesetsa kusintha moyo wanga ndipo ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova mu 2008.

Ine ndi Esther timaphunzira Baibulo ndi anthu olankhula Chipolishi

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Baibulo landithandiza kuti ndisinthe moyo wanga. Poyamba ndinali ndi makhalidwe oipa kwambiri. Ndinali wandewu, ndinkagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo komanso ndinkakonda kwambiri mpira. Ndinkafunanso kuti ndidzagwire ntchito yapamwamba. Koma panopa ndimasangalala kuthandiza ena kudziwa Baibulo. Sikuti ndinasiya kukonda mpira, koma ndimadziwa kuti palinso zinthu zina zofunika kwambiri.

Panopa ndili pa banja ndipo mkazi wanga dzina lake ndi Esther. Nayenso ndi wa Mboni za Yehova ndipo timaphunzira Baibulo ndi anthu olankhula Chipolishi, omwe amakhala kumpoto chakumadzulo m’dziko la England. Ndine munthu wosangalala kwambiri komanso sindimadziimba mlandu. Ndimaona kuti panopa m’pamene zinthu zikundiyenderadi.