Mayi wina yemwe amakhala ku California m’dziko la United States, dzina lake Becky, anati: “Pali munthu winawake wa Mboni za Yehova, dzina lake Mike ndipo ndinadziwana naye pa kanthawi ndithu. Komabe zimene anthu a m’chipembedzo chakechi amachita zimandiimitsa mutu. Mwachitsanzo, popeza amati iwowo ndi a Mboni za Yehova, ndimadabwa kuti Yehovayo ndi ndani? Nanga n’chifukwa chiyani a Mboni sakondwerera nawo maholide? Kodi chipembedzo cha Mike si kagulu kampatuko?

Bambo wina dzina lake Zenon, yemwe amakhala ku Ontario m’dziko la Canada, anati: “Anthu ena omwe ndimakhala moyandikana nawo nyumba atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova, ndinayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi dzina lakuti Mboni za Yehova limatanthauza chiyani?’ Ndinkafuna kudziwa kuti, ‘N’chifukwa chiyani chipembedzochi chili ndi dzina limeneli?’”

Bambo wina amene amakhala ku Washington m’dziko la United States, dzina lake Kent, anati: “Ine ndi mkazi wanga tinkaganiza kuti a Mboni za Yehova anapezerapo mwayi womabwera kwathu atadziwa kuti sitipita kutchalitchi. Tinkaona kuti ngati zipembedzo zikuluzikulu zikulephera kutiphunzitsa zomveka, ndiye kodi a Mboni za Yehova angatithandize?”

Mayi wina yemwe amakhala ku Esbjerg m’dziko la Denmark, dzina lake Cecilie, anati: “A Mboni za Yehova sindinkawadziwa komanso sindinkadziwa zimene amakhulupirira.”

N’kutheka kuti nanunso mumaona a Mboni za Yehova akulalikira kunyumba za anthu komanso m’malo amene kumapezeka anthu ambiri. Mwina mumawaona akugawira mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo komanso akuphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. N’kuthekanso kuti nthawi ina anakupatsanipo magazini. Kodi nanunso mumadzifunsa mafunso ofanana ndi amene ali pamwambawa? Nanga kodi mumafuna mutadziwa kuti a Mboni za Yehova ndi anthu otani?

Kodi mayankho a mafunso amenewa mungawapeze kuti? Nanga mungadziwe bwanji zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira, mmene amapezera ndalama zoyendetsera ntchito yawo komanso chifukwa chake amabwera kwanu ndiponso kulalikira m’malo osiyanasiyana?

Mayi Cecilie, omwe tawatchula kumayambiriro kwa nkhaniyi, ananenanso kuti: “Ndinawerengapo nkhani zimene anthu ena analemba pa Intaneti zokhudza a Mboni za Yehova. Ndinali nditamva mphekesera zambiri zonyoza a Mboni za Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti ndizidana kwambiri ndi a Mboni.” Kenako a Cecilie anaganiza zokumana ndi a Mboni ndipo anawafunsa mafunso ambiri. Mayiwo anasangalala kwambiri ndi mmene a Mboniwo anawayankhira mafunso awo.

Kodi inunso mukufuna mutadziwa zoona zokhudza a Mboni za Yehova? Mungachite bwino kukumana ndi a Mboniwo, omwenso ndi amene amafalitsa magazini mukuwerengayi, n’kuwafunsa. (Miyambo 14:15) Tikukhulupirira kuti nkhani yotsatirayi ikuthandizani kudziwa zimene timakhulupirira komanso zimene timachita.