Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI SAYANSI INGALOWE M’MALO MWA BAIBULO?

Sayansi Singatithandize Kudziwa Zonse

Sayansi Singatithandize Kudziwa Zonse

Zaka zapitazi, anthu alemba mabuku ambiri ofotokoza zimene anthu omwe sakhulupirira kuti kuli Mulungu ananena. Anthu ambiri amachita chidwi ndi zimene mabukuwa amanena moti amayamba kukhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani yoti kuli Mulungu kapena ayi. Wasayansi wina dzina lake David Eagleman analemba kuti: “Anthu ena akawerenga mabukuwa . . . amaganiza kuti asayansi amadziwa zonse moti amakhulupirira kuti zimene asayansiwa anganene pa nkhani yoti kulibe Mulungu, zikhoza kukhala zoona. Koma asayansi enieni amadziwa kuti pali zinthu zambiri zomwe sanazidziwebe ndipo zimenezi zimaonekera bwino akatulukira chinthu chatsopano.”

Kuyambira kale kwambiri, akatswiri a sayansi akhala akufufuza kuti adziwe zambiri zokhudza chilengedwechi ndipo adabwa kwambiri ndi zimene apeza. Komabe nthawi zina zimene apeza sizikhala zolondola. Mwachitsanzo wasayansi wina, dzina lake Isaac Newton yemwe anatulukira zinthu zambiri, ankaphunzitsa kuti mphamvu yokoka imachititsa kuti mapulaneti, nyenyezi komanso magulu a nyenyezi zizikhala mwadongosolo m’mlengalenga. Anayambitsanso njira ina yosovera masamu yomwe masiku ano amagwiritsa ntchito popanga makompyuta. Asayansi amagwiritsanso ntchito masamuwa kuti adziwe mmene angayendere kupita kumapulaneti ena komanso popanga zinthu monga mabomba, magetsi ndi zina zomwe zimapangidwa pogwiritsa ntchito mphamvu ya nyukiliya. Komabe, zinthu zina zomwe Newton ankakhulupirira zinali zabodza. Mwachitsanzo ankakhulupirira kuti akhoza kugwiritsa ntchito njira zamatsenga kuti asinthe zitsulo kukhala golide.

Zaka 1,500 Newton asanapeze zimenezi, munthu wina wa ku Greece, yemwenso anali katswiri wolemba mapu, dzina lake Ptolemy, ankafufuza zinthu za m’mlengalenga ndi maso ake. Ankachita zimenezi usiku kuti aone mapulaneti omwe ali m’mlengalenga. Ptolemy ankakhulupirira kuti dzikoli ndiye pakati pa chilengedwe chonse. Komabe wasayansi wina dzina lake Carl Sagan analemba kuti: “Anthu anakhala akukhulupirira zimene Ptolemy ankanenazi kwa zaka zoposa 1,500 koma sankadziwa kuti n’zabodza. Zimenezi zikusonyeza kuti wasayansi, ngakhale wanzeru kwambiri akhoza kupeza zinthu zomwe si zolondola.”

Masiku anonso, asayansi amalephera kudziwa bwinobwino zinthu zina zokhudza chilengedwechi ndipo amapangitsa anthu kuganiza zolakwika. N’zoona kuti masiku ano sayansi yapita patsogolo kwambiri ndipo zimene asayansi apeza zikuthandiza anthu. Komatu ndi bwino kudziwa kuti asayansi sangatithandize kudziwa zonse. Wasayansi wina dzina lake Paul Davies, anati: “Takhala tikufufuza kuti tidziwe mmene zinthu zina m’chilengedwechi zimachitikira. Koma kunena zoona zinthu zambiri n’zozunguza mutu ndipo sitingathe kufotokoza bwinobwino mmene zinthuzi zimagwirira ntchito.” Apatu mfundo ndi yakuti, anthufe sitingakwanitse kudziwa zonse zokhudza chilengedwechi. Choncho anthu ena akamati sayansi ingatithandize kudziwa zonse, si bwino kufulumira kukhulupirira zimenezo.

Baibulo ndi lothandiza kwambiri kuposa sayansi

Pali zinthu zambiri zimene anthufe sitingazimvetse komanso kuzidziwa. Ponena za chilengedwechi, Baibulo limati: “Zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita [za Mulungu], ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.” (Yobu 26:14) Izi zikusonyeza kuti zimene Paulo analemba zaka 2,000 zapitazo n’zoona. Iye anati: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake?”—Aroma 11:33.