KODI mumamva bwanji mukaganizira zoti nthawi ina mudzakalamba? Ambiri akaganizira nkhani imeneyi amada nkhawa kwambiri mwinanso kuchita mantha. Amada nkhawa chifukwa amaona kuti akadzakalamba azidzakumana ndi mavuto monga kuiwalaiwala, kudwaladwala, kukwinyika kwa khungu komanso kufooka kwa thupi.

Komabe si anthu onse amene akakalamba amakumana ndi mavuto amenewa. Ndipotu masiku ano ena amakhala ndi thanzi labwino ngakhale akalambe kwambiri. Izi zimatheka chifukwa anthu okalamba akumatha kulandira thandizo lamankhwala lomwe limachepetsa kapena kuchiza matenda omwe anthu okalamba amadwala. Zimenezi zikupangitsa kuti anthu azikhala ndi moyo wotalikirapo komanso wathanzi.

Anthu achikulire ambiri amafuna kuti azisangalalabe ngakhale kuti ndi okalamba. Ndiye kodi mungatani kuti zimenezi zitheke? Chofunika kwambiri ndi kukhala okonzeka kusintha mmene mumachitira zinthu komanso kukhala ndi maganizo oyenera. Tiyeni tione mfundo zina za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni.

MUZIDZIWA KUTI PALI ZINA ZOMWE SIMUNGAKWANITSE KUCHITA: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Mawu akuti, “anthu odzichepetsa” angatanthauzenso anthu achikulire omwe amazindikira kuti sangachite zinthu ngati mmene ankachitira ali achinyamata. Agogo ena azaka 93 omwe amakhala ku Brazil, dzina lawo a Charles, ananena kuti: “Ngati mwakhala zaka zambiri, muyenera kukalamba basi. Zimenezi n’zofanana ndi nthawi. Ngati yafika 12 koloko, n’zosatheka kuibweza kuti ikhale pa 10 koloko.”

Komatu kudzichepetsa sikukutanthauza kuti muzidziderera n’kumaganiza kuti, “Ife tinatha basi.” Maganizo amenewa ndi ofooketsa ndipo angachititse kuti muzingoona ngati palibe zimene mungachite. N’chifukwa chake lemba la Miyambo 24:10 limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” Koma munthu wodzichepetsa amakhala wozindikira n’kumachita zomwe angakwanitse.

Bambo ena azaka 77 omwe amakhala ku Italy, dzina lawo a Corrado, anati: “Ukamayendetsa galimoto pachitunda umafunika kusintha magiya, komabe umafunikanso kusamala kuti galimotoyo isakuzimire.” Ndi zimenenso munthu ayenera kuchita akamakalamba. Amafunika kusintha zinthu zina. A Corrado ndi akazi awo anasintha mmene ankagwirira ntchito zapakhomo n’cholinga choti asamapanikizike komanso kuti asamatope kwambiri. Ndi zimenenso amachita agogo ena azaka 81, dzina lawo a Marian. Mayiwa anati: “Ndimayesetsa kuti ndisamadzipanikize. Nthawi zina ndikamagwira ntchito, ndimasiya kaye n’kukhala pansi kapena kugona kuti ndipume. Popumapo  ndimakonda kuwerenga kapena kumvetsera nyimbo. Ndimadziwa zimene ndingakwanitse kuchita komanso zomwe sindingakwanitse.”

Muzidziwa kuti pali zina zomwe simungakwanitse kuchita

MUZIVALA BWINO: “Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndi mwanzeru.” (1 Timoteyo 2:9) Mawu akuti “zovala zoyenera” akusonyeza kuti tiyenera kuganizira mmene timavalira. Mayi ena azaka 74 omwe amakhala ku Canada, dzina lawo a Barbara anati: “Ndimayesetsa kuvala zovala zoyera komanso zooneka bwino. Ndimayesetsanso kudzisamalira ndipo sindiganiza kuti chifukwa choti ndine wokalamba ndiye sindingatchene.” Komanso mayi ena azaka 91 omwe amakhala ku Brazil, dzina lawo a Fern ananena kuti: “Ndikaona kuti zovala zikutha, ndimakagula zatsopano n’cholinga choti ndizioneka bwino.” Nanga bwanji azibambo achikulire? Bambo ena azaka 73 omwe amakhala ku Brazil, dzina lawo a Antônio anati: “Ndimayesetsa kuvala zovala zoyera, kusamba tsiku lililonse komanso kumeta ndevu kuti ndizioneka waukhondo.”

Komabe si bwino kumangoganizira za zovala komanso mmene mumaonekera mpaka kufika polephera kuchita zinthu “mwanzeru.” Mayi ena azaka 69, omwe amakhala ku South Korea dzina lake Bok-im, ali ndi maganizo oyenera pa nkhani ya zovalayi. Mayiwa anati: “Ndimadziwa kuti si bwino kuvala zovala zosalongosoka poganiza kuti ndine wokalamba. Komabe ndimadziwanso kuti sizingakhale bwino kuti ndizivala zovala zomwe ndinkavala ndili mtsikana.”

Musamangoganizira zimene simungathe kuchita

MUSAMANGOGANIZIRA ZIMENE SIMUNGATHE KUCHITA: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.” (Miyambo 15:15) Mwina mungakhumudwe poona kuti simukukwanitsanso kuchita zimene munkachita muli ndi mphamvu. Zimenezi n’zomveka. Komabe si bwino kumangoganizira zimene simungathe kuchita. Zimenezi zingapangitse kuti muzingokhala wokhumudwa n’kumalephera kuchita zinthu bwinobwino. Abambo ena azaka 79 omwe amakhala ku Canada, dzina lawo a Joseph, anati: “Ndimayesetsa kuti ndizisangalala ndi zomwe ndimakwanitsa kuchita, m’malo momangodandaula kuti sindikuthanso kuchita zinazake. Ndimachita zimenezi chifukwa ndikudziwa kuti kale silibwerera.”

Kukonda kuwerenga komanso kuphunzira zinthu kungakuthandizeninso kuti muzisangalala. Choncho ngati mungakwanitse, yesetsani kumawerenga zinthu zosiyanasiyana komanso kuphunzira zinthu zatsopano. Abambo ena azaka 74 a ku Philippines, dzina lawo a Ernesto, amakonda kupita kulaibulale kukawerenga mabuku osangalatsa. Bambowa anati: “Ndimakondabe kuphunzira zinthu zatsopano. Ndimasangalala ndikamawerenga nkhani za zinthu zomwe zinachitika kwinakwake ndipo zimangokhala ngati ndafikako.” Bambo ena azaka 75 a ku Sweden dzina lawo a Lennart, amaonanso choncho ndipo iwo anaphunzira chinenero china ngakhale kuti kuchita zimenezi n’kovuta.

Muzikhala wowolowa manja

MUZIKHALA WOWOLOWA MANJA: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.” (Luka 6:38) Muziyesetsa kugwiritsa ntchito nthawi ndi zinthu zanu kuthandiza ena. Kuchita zimenezi kungapangitse kuti muzisangalala. Mwachitsanzo mayi ena a ku Brazil dzina lawo a Hosa, omwe ali ndi zaka 85, amayesetsa kuthandiza ena  ngakhale kuti amadwaladwala. Mayiwa anati: “Ndimakonda kuimbira foni kapenanso kulembera kalata anthu amene akudwala kapena amene akumana ndi vuto linalake. Ndimachita zimenezi n’cholinga choti ndiwalimbikitse. Nthawi zina ndimawatumizira kamphatso kapena kuwaphikira kenakake.”

Mukakhala ndi chizolowezi chopatsa, zimakhala zosavuta kuti inunso anthu azikupatsani zinthu. Bambo Jan, omwe ali ndi zaka 66 ndipo amakhala ku Sweden, anati: “Mukamakonda anthu ena, nawonso amayamba kukukondani.” Zimenezi n’zoona chifukwa munthu akakhala wowolowa manja, anthu amamasuka naye.

MUZIKONDA KUCHEZA NDI ANTHU: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1) N’zoona kuti nthawi zina mungafune kukhala panokha. Komabe si bwino kumangokhala nokhanokha nthawi zonse. Abambo ena azaka 72 dzina lawo a Innocent, omwe amakhala ku Nigeria, amakonda kucheza ndi anzawo. Bambowa anati: “Ndimakonda kucheza ndi anthu a misinkhu yosiyanasiyana.” Nawonso Bambo Börje a ku Sweden omwe ali ndi zaka 85, anati: “Ndimakonda kucheza ndi achinyamata. Zimenezi zimachititsa kuti nanenso ndizidziona ngati mnyamata.” Achikulire ena amaona kuti ndi bwino kuyamba iwowo kuitana anthu oti acheze nawo. Mwachitsanzo a Han-sik a ku South Korea, omwe ali ndi zaka 72, anati: “Ine ndi mkazi wanga timakonda kukonza kaphwando n’kuitana achikulire ndi achinyamata omwe kuti tingosangalala basi.”

Muzikonda kucheza ndi anthu

Munthu wochezeka ndi amene amakonda kulankhula ndi anthu. Komabe mukamacheza ndi munthu, si bwino kumangolankhula nokha. Muyenera kupereka mpata woti winayo alankhule, inuyo n’kumamvetsera. Muzisonyeza kuti mumaganizira anthu ena. Mayi Helena azaka 71 omwe amakhala ku Mozambique, anati: “Ndimayesetsa kukhala wochezeka komanso kulemekeza anthu ena. Akamalankhula, ndimamvetsera kuti ndidziwe zimene akuganiza komanso zomwe amakonda.” Komanso abambo ena a ku Brazil dzina lawo a José omwe ali ndi zaka 73, anati: “Anthu amakonda kukhala ndi munthu amene amawamvetsera akamalankhula, amasonyeza kuti amaganizira ena, amawayamikira akachita zabwino komanso wanthabwala.”

Mukamalankhula, muzisankha bwino mawu kuti azimveka ‘okoma ngati mwawathira mchere.’ (Akolose 4:6) Muzilankhula zolimbikitsa komanso muziganizira kaye musanalankhule.

MUZIYAMIKIRA ZOMWE ENA AKUCHITIRANI: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.” (Akolose 3:15) Munthu wina akakuthandizani, muzimuyamikira. Zimenezi zimathandiza kuti muyambe kugwirizana kwambiri ndi munthuyo. Mayi ena a ku Canada azaka 74, dzina lawo a Marie-Paule, anati: “Nyumba imene tikukhala panopa tasamukiramo posachedwapa. Anzathu ambiri anatithandiza pamene tinkasamuka ndipo timasowa kuti tingawathokoze bwanji. Ena tinawatumizira makadi owathokoza ndipo ena tinawaitana kwathu kuti tidzadyere limodzi chakudya.” Mayi Jae-won azaka 76, omwe amakhala ku South Korea, amathokoza kwambiri anthu omwe amawatenga pa galimoto popita ndi pobwera ku Nyumba ya Ufumu. Mayiwa anati: “Ndimathokoza kwambiri zimene amandichitirazi moti nthawi zina ndimawapatsako kandalama koti awonjezere kugulira mafuta a galimoto. Nthawi zina ndimawapatsa mphatso komanso makadi owathokoza.”

Koposa zonse, muyenera kumayamikira mphatso ya moyo imene muli nayo. Baibulo limati: “Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Mfundo zomwe takambirana m’nkhaniyi zikusonyeza kuti mukamaona zinthu moyenera komanso mukamavomereza kuti pali zinthu zina zomwe simungakwanitse kuchita, mungathe kumasangalalabe ngakhale kuti ndinu wokalamba.

Muziyamikira zomwe ena akuchitirani