Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MULUNGU AMAKUONANI KUTI NDINU WOFUNIKA?

Mulungu Amakumvetsani

Mulungu Amakumvetsani

“Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.”—SALIMO 139:1.

“Maso anu anandiona pamene ndinali mluza.” —SALIMO 139:16

N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ENA AMAKAYIKIRA? Anthu ambiri amaganiza kuti Mulungu amangoona kuti anthu ndi ochimwa komanso odetsedwa ndipo alibe nawo ntchito. Mtsikana wina dzina lake Kendra, yemwe ankadwala matenda a maganizo, ankangokhalira kudziimba mlandu chifukwa ankaona kuti amalephera kuchita zonse zimene Mulungu amafuna. Iye ananena kuti zimenezi zinachititsa kuti asiye kupemphera.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Sikuti Yehova amangoona zimene mumalakwitsa. Iye amaonanso zimene zili mumtima mwanu ndipo amakumvetsani. Baibulo limanena kuti: “Akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” Komanso ‘satichitira mogwirizana ndi machimo athu,’ koma amatikhululukira tikalapa.—Salimo 103:10, 14.

Taganizirani zimene zinachitikira Davide yemwe anali mfumu ya Aisiraeli. Iye anapemphera kuti: “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. . . . Ndifufuzeni, inu Mulungu, ndi kudziwa mtima wanga.” (Salimo 139:16, 23) Davide ankadziwa kuti ngakhale kuti pa nthawi ina anachitapo machimo akuluakulu, koma atalapa kuchokera pansi pa mtima, Yehova anazindikira zimenezi ndipo anamukhululukira.

Dziwani kuti Yehova amakumvetsani kuposa munthu wina aliyense. Baibulo limati: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Samueli 16:7) Mulungu amadziwa zimene zimakupangitsani kuti muzichita zinazake. Kaya ndi chifukwa cha chibadwa chanu, mmene munaleredwera kapenanso kumene mukukhala, Mulungu amamvetsa zonsezo. Ngati mukuyesetsa kuti muzichita zabwino, iye amaona komanso amasangalala ngakhale kuti mumalakwitsa zinthu zina.

Popeza Mulungu amakumvetsani chonchi, kodi amakuthandizani bwanji pogwiritsa ntchito zomwe amadziwazo?