Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  August 2014

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi zipembedzo zonse zimakondweretsa Mulungu?

N’kutheka kuti munamvapo nkhani zosonyeza zinthu zoipa zimene zimachitika m’dzina la chipembedzo. Mwina munamva nkhani zimenezi pa wailesi kapena munawerenga m’nyuzipepala. Zimenezi zikusonyeza kuti si zipembedzo zonse zimene zimakondweretsa Mulungu. (Mateyu 7:15) Izitu ndi umboni wakuti anthu ambiri asocheretsedwa.—Werengani 1 Yohane 5:19.

Komabe, Mulungu amachita chidwi ndi anthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino komanso kumulambira m’njira imene iye amafuna. (Yohane 4:23) Mulungu akuthandiza anthu amenewa kuti aphunzire zolondola kudzera m’Mawu ake, Baibulo.—Werengani 1 Timoteyo 2:3-5.

Kodi mungadziwe bwanji chipembedzo choona?

Yehova Mulungu akuphunzitsa choonadi anthu omwe poyamba anali m’zipembedzo zosiyanasiyana ndipo akuthandiza anthuwa kuti akhale ogwirizana komanso okondana. (Mika 4:2, 3) Choncho, chizindikiro china cha chipembedzo choona ndi choti anthu ake amakondana.—Werengani Yohane 13:35.

Yehova Mulungu akuphunzitsa choonadi anthu osiyanasiyana ndipo akuthandiza anthuwa kuti akhale ogwirizana.—Salimo 133:1

Zinthu zimene anthu a m’chipembedzo choona amakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Anthuwa amayesetsa kutsatira zimene amaphunzira m’Baibulo pa moyo wawo. (2 Timoteyo 3:16) Iwo amauza anthu dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Ndipo amathandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto padzikoli. (Danieli 2:44) Iwo amatengera chitsanzo cha Yesu ndipo ‘amaonetsa kuwala’ pochitira zabwino anthu. (Mateyu 5:16) Akhristu oona amadziwikanso chifukwa amapita kunyumba za anthu n’kumakawauza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Werengani Mateyu 24:14; Machitidwe 5:42; 20:20.

 

Onaninso

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Uthenga Wabwino N’chiyani?

Dziwani uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu, chifukwa chake ukufunika kulengezedwa mwamsanga, ndiponso zimene inuyo muyenera kuchita.

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kudziwa anthu amene ali m’chipembedzo choona.