Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  July 2014

Kodi Mungatani Kuti Muzilangiza Bwino Ana Anu?

Kodi Mungatani Kuti Muzilangiza Bwino Ana Anu?

“Ndinkati ndikamva kulira kwa galimoto, ndimangoti mwina ndi Jordan akubwera. Nthawi imene tinamuuza kuti azikhala atafika panyumba inali itadutsa ndipo aka kanali kachitatu kuti abwere mochedwa. Ndinkada nkhawa ndipo ndinkangodzifunsa kuti, ‘Mwana ameneyu ali kuti? Kodi ali bwinobwino? Koma ameneyu akudziwa kuti akachedwa kubwera ife timada nkhawa?’ Mmene ankafika, ndinali nditalusa kwambiri.”GEORGE.

“Tsiku lina ndinamva mwana wanga wina akulira mofuula, ndipo ndinada nkhawa kuti akulira chiyani. Nditacheuka, ndinamuona akulira momvetsa chisoni kwinaku atagwira mutu. Kamchimwene kake kazaka 4 kanali katamukhoma.”—NICOLE.

“‘Sindinabetu ine ndalamayi, ndangoitola.’ Natalie, mwana wathu wamkazi wazaka 6, ananena zimenezi m’maso muli gwa. Iye anakana kwamtuwagalu kuti sanabe. Zimenezi zinatikhudza kwambiri moti mpaka tinagwetsa misozi chifukwa tinkadziwa kuti akunama.”—STEPHEN.

NGATI ndinu kholo, mwina nthawi ina zoterezi zinakuchitikirani. N’kutheka kuti munadzifunsapo kuti: “Kodi mwana ameneyu tim’patse chilango chotani? Kodi ndi bwino kupatsa mwana chilango akalakwitsa zinazake?

KODI KULANGA N’KUTANI?

M’Baibulo, mawu akuti kulanga samangotanthauza kupereka chilango. Mawuwa amatanthauzanso kulangiza, kuphunzitsa komanso kudzudzula. Koma satanthauza kuchitira munthu nkhanza.—Miyambo 4:1, 2.

Kulangiza mwana kuli ngati ulimi wa zipatso. Mlimi amafunika kukumba maenje, kuthira manyowa, kuchotsa udzu, kuthirira mitengoyo komanso kuiteteza ku tizilombo. Mitengoyo ikamakula, mlimi amafunika kuidulira kuti izikula bwino. Iye amazindikira kuti kuchita zonsezi kumathandiza kuti adzakolole zipatso zabwino. Mofanana ndi zimenezi, makolo nawonso amayesetsa kusamalira ana awo m’njira zosiyanasiyana. Koma nthawi zina amafunika kulanga komanso kudzudzula ana awo. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti mwana asiye khalidwe lolakwika komanso kuti akule bwino ngati mmene kudulira mtengo kumathandizira. Komansotu mlimi akamadulira mtengo, amaudulira mosamala kuopera kuti ungawonongeke. Mofanana ndi zimenezi, makolo akaona kuti ana awo akufunika kuwalangiza, ayenera kuchita zimenezi mosamala komanso mwachikondi.

Yehova Mulungu amapereka chitsanzo chabwino kwa makolo pa nkhani imeneyi. Iye akafuna kulangiza kapena kudzudzula atumiki ake, amachita zimenezi mwachikondi ndipo atumiki akewo sadana ndi zimenezi. (Miyambo 12:1) Iwo ‘amagwira malangizo’ ndipo ‘samawataya.’ (Miyambo 4:13) Nanunso mukhoza kuthandiza ana anu kuti asamadane ndi malangizo ngati, mofanana ndi Yehova, malangizo anuwo atamakhala (1) achikondi (2) oyenera komanso (3) osasinthasintha.

MALANGIZO ANU AZIKHALA ACHIKONDI

Mulungu amalangiza komanso kudzudzula atumiki ake chifukwa chowakonda. Baibulo limati: “Yehova amadzudzula munthu amene amam’konda, monga momwe bambo amadzudzulira mwana amene amakondwera  naye.” (Miyambo 3:12) Limatinso Yehova ndi ‘wachifundo, wachisomo ndiponso wosakwiya msanga.’ (Ekisodo 34:6) Malembawa akusonyeza kuti Yehova sachita zinthu mwankhanza. Iye satilankhula mawu achipongwe kapena onyoza, chifukwa mawu otere ndi “olasa ngati lupanga.”—Miyambo 12:18.

KUMVETSERA

N’zoona kuti makolo sangathe kutsanzira Mulungu ndendende pa nkhani ya kuugwira mtima. Nthawi zina mungaone kuti mwakwiya kwambiri moti simungathenso kupirira. Koma kumbukirani kuti kulanga mwana chifukwa choti mwapsa mtima kungachititse kuti muchite zinthu mwankhanza komanso mwaukali ndipo mwanayo sangaphunzirepo chilichonse. Kulanga mwana chifukwa chopsa mtima kumangosonyeza kuti mwalephera kudziletsa.

Koma kulanga mwana chifukwa chomukonda, kungathandize mwanayo kuti aphunzirepo kanthu. Taonani zimene George ndi Nicole, makolo amene tawatchula kumayambiriro aja, anachita.

KUPEMPHERA

George anati: “Mmene Jordan ankafika, n’kuti ine ndi mkazi wanga titalusa kwambiri. Komabe tinayesetsa kuugwira mtima ndipo tinamusiya kuti afotokoze chifukwa chake anabwera mochedwa. Koma popeza unali usiku kwambiri, tinamuuza kuti tikambirana nkhaniyi m’mamawa. Tinapemphera limodzi kenako n’kukagona. Mmene kunkacha, n’kuti aliyense mtima wake uli m’malo. Tinakambirana nkhaniyi modekha moti anamvetsa bwino zimene tinamuuza. Iye anavomera kuti azitsatira malamulo amene tinam’patsa komanso kuti azilandira chilango akaphwanya malamulowo. Tikuona kuti zinthu zinayenda bwino chonchi chifukwa tinazindikira mfundo yoti kupereka chilango chifukwa chopsa mtima sikuthandiza. Chinanso chimene chinathandiza n’choti, tinamulola kuti afotokoze kaye ndipo ifeyo tinamvetsera modekha.”

KUKAMBIRANA

Nicole anati: “Ndinalusa koopsa nditaona mmene mwana wanga wamng’ono anapwetekera mchemwali wake. Komabe sindinamupatse chilango nthawi yomweyo. Ndinamulowetsa kuchipinda chake chifukwa ndinazindikira kuti si bwino kuti ndim’patse chilango nditalusa. Kenako mtima wanga utakhala m’malo, ndinamufotokozera kuti si bwino kuchita ndewu ndipo ndinamuonetsa mmene anapwetekera mchemwali wakeyo. Zimenezi zinamuthandiza kwambiri moti anam’pepesa n’kumukumbatira.”

Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti chilango choyenera chimaperekedwa chifukwa cha chikondi osati chifukwa chopsa mtima.

MALANGIZO ANU AZIKHALA OYENERA

Yehova amapereka chilango “pamlingo woyenera.” (Yeremiya 30:11; 46:28) Iye amadziwa zonse zimene zapangitsa munthu kuti alakwe kuphatikizapo zimene anthu sangazidziwe. Kodi makolo angatengere bwanji chitsanzo chimenechi? Stephen, amene tamutchula kumayambiriro kwa nkhaniyi, ananena kuti: “Tinakhumudwa kwambiri ndipo sitinkamvetsa chifukwa chimene Natalie ankakanira kuti sanabe  ndalama pamene zinkachita kuonekeratu kuti waba. Komabe tinaganizira kuti ndi mwana ndipo tinadziwa kuti akuchita zimenezo chifukwa cha chibwana.”

Mwamuna wa Nicole, dzina lake Robert, nayenso amayesetsa kuganizira zimene zachititsa mwana kuti asamvere malangizo. Ana ake akalakwitsa zinazake, amadzifunsa kuti: ‘kodi aka n’koyamba kuti mwanayu achite zimenezi kapena ndi khalidwe lake? Kodi akudwala kapena watopa? Kodi zimene wachitazi ndi chizindikiro choti wayamba khalidwe linalake loipa?’

Makolo oganiza bwino amakumbukiranso mfundo yoti mwana ndi mwana ndipo nthawi zambiri sangachite zinthu ngati wamkulu. Mtumwi Paulo ankadziwa mfundoyi, ndipo analemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana.” (1 Akorinto 13:11) Robert ananena kuti: “Chimene chimandithandiza kuti ndizimvetsa mwana wanga akalakwitsa, ndi kukumbukira zimene ineyo ndinkachita ndili mwana.”

Muzikumbukira kuti mwana sangachite zinthu zonse moyenera. Koma izi sizikutanthauza kuti muzingomulekerera akayamba kusonyeza khalidwe linalake loipa. Muziganizira zimene mwana wanu angakwanitse ndi zimene sangakwanitse komanso zimene zapangitsa kuti achite zinazake. Zimenezi zidzakuthandizani kuti mudziwe chilango choyenera kum’patsa.

MUSAMASINTHESINTHE

Lemba la Malaki 3:6 limati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” Atumiki a Mulungu amaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona ndipo zimawapangitsa kudalira malangizo a Yehova. Makolo amafunikanso kupereka malangizo odalirika kwa ana awo ndipo sayenera kumangosinthasintha. Mukamangoti lero kunena izi, mawa kunena zina, mwana wanuyo akhoza kusokonezeka ndipo zingamuvute kutsatira malangizo anu.

Kumbukirani zimene Yesu ananena. Iye anati: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.” Malangizo amenewa ndi othandiza kwambiri polera ana. (Mateyu 5:37) Musanapatse mwana wanu lamulo komanso musanamuuze chilango chimene mungam’patse akaphwanya lamulolo, muziganizira kaye ngati mungadzam’patsedi chilangocho. Mwachitsanzo, ngati mutauza mwana wanu kuti akabwera mochedwa muzimukwapula, muzionetsetsa kuti mwamukwapuladi.

Makolonu mukamagwirizana pa nkhani yolera ana, zimathandiza kuti malangizo anu asamasiyane. Robert ananena kuti: “Ngati mwana wathu wandipempha chinachake chimene mayi ake anamukaniza, ineyo n’kuvomera koma ndisakudziwa kuti mayi ake anamukaniza, ndikadziwa ndimamukaniza kuti ndigwirizane ndi zimene mkazi wanga anamuuza.” Ngati makolo akusiyana maganizo pa zimene angachite zokhudza ana awo, ayenera kukambirana kaye paokha n’kumanga chimodzi.

KULANGIZA ANA N’KOFUNIKA

Mukamatsanzira Yehova popatsa ana anu malangizo achikondi, oyenera komanso osasinthasintha, malangizowo amakhala othandiza kwa anawo. Malangizo otero angathandize ana anu kuti akadzakula adzakhale oganiza bwino, odalirika komanso kuti azidzachita zinthu mwanzeru. Pa mfundo imeneyi, Baibulo limati: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—Miyambo 22:6.

Onaninso

GALAMUKANI!

Zimene Mungachite Kuti Mwana Wanu Azikumverani

Cholinga cha chilango ndi kuphunzitsa. Mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kuti muphunzitse mwana wanu kumvera.