Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIFUKWA CHIYANI ANTHU ABWINO NAWONSO AMAKUMANA NDI MAVUTO?

N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?

N’chifukwa Chiyani Anthu Abwino Nawonso Amakumana Ndi Mavuto?

Chifukwa choti Yehova Mulungu * ndi amene analenga zonse komanso ndi wamphamvu kuposa aliyense, anthu ambiri amaganiza kuti ndi amene amapangitsa chilichonse chimene chimachitika padziko lapansili, kuphatikizapo zoipa. Komabe, taonani zimene Baibulo limafotokoza ponena za Mulungu woona.

  • “Yehova ndi wolungama m’njira zake zonse.”—Salimo 145:17.

  • “Njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika, amene sachita chosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.”Deuteronomo 32:4.

  • “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.”Yakobo 5:11.

Mulungu si amene amachititsa kuti zinthu zoipa zizichitika. Nanga kodi ndi iyeyo amene amapangitsa kuti anthu azichita zoipa? Ayinso. Baibulo limati: “Munthu akakhala pa mayesero asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’” Chifukwa chiyani? “Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Mulungu samayesa munthu pomuchititsa kuti azichita zinthu zoipa. Choncho, Mulungu sachita zinthu zoipa komanso sachititsa kuti anthu azichita zoipa. Ndiye kodi n’chiyani chimachititsa kuti zinthu zoipa zizichitika padzikoli?

KUKHALA PAMALO OLAKWIKA, PA NTHAWINSO YOLAKWIKA

Lemba la Mlaliki 9:11 limatiuza chinthu china chimene chimapangitsa kuti anthu azivutika. Limati: “Nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.” Zinthu zosayembekezereka kapena ngozi zikachitika, anthu ena amatha kufa chifukwa choti pa nthawi ya ngoziyo, iwowo anali pamalopo. Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, Yesu Khristu ananena za ngozi ina, pamene nsanja inagwa n’kupha anthu 18. (Luka 13:1-5) Sikuti anthuwa anafa chifukwa choti anali ochimwa kwambiri kuposa anthu ena, koma n’chifukwa choti pa nthawi imene nsanjayo inkagwa, iwowo anali pamalopo. Komanso mu January 2010, ku Haiti kunachitika chivomezi choopsa ndipo anthu oposa 300,000 anafa pa ngoziyi. Anthuwa anafa mosatengera kuti anali ndani ndiponso ankachita zotani pa moyo wawo. Komanso matenda akhoza kugwira munthu aliyense pa nthawi iliyonse.

N’chifukwa chiyani Mulungu sateteza anthu abwino kuti asakumane ndi mavuto?

Koma ena amafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani Mulungu saletsa kuti zoipa zisamachitike? Nanga n’chifukwa chiyani sateteza anthu abwino kuti zoipa zisawachitikire?’ Mulungu akanakhala kuti amachita zimenezi, zikanasonyeza kuti amadziwiratu kuti zinthu zoipa zichitika, zoipazo zisanachitike. Ndi zoona kuti Mulungu ali ndi mphamvu zodziwiratu zam’tsogolo. Komabe mfundo imene tiyenera kuiganizira ndi yakuti: Kodi Mulungu nthawi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zakezi kudziwiratu chilichonse chimene chingachitike?—Yesaya 42:9.

Baibulo limati: “Mulungu wathu ali kumwamba. Chilichonse chimene anafuna kuchita anachita.” (Salimo 115:3) Choncho, Yehova amachita zinthu akaona kuti pakufunika kuchita zimenezo. Sikuti iye amangochita zinthu chifukwa choti angathe kuchita chilichonse. N’chimodzimodzinso ndi nkhani yodziwiratu zam’tsogolo. Iye amachita kusankha ngati akufuna kudziwiratu  za zinthuzo kapena ayi. Mwachitsanzo, zinthu zitafika poipa kwambiri m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora, Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Nditsikirako kuti ndikaone ngati akuchitadi monga mwa kudandaula kumene ndamva ndiponso ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho. Ndikufuna ndidziwe zimenezi.” (Genesis 18:20, 21) Izi zikusonyeza kuti kwa nthawi ndithu, Yehova anasankha kuti asadziwe zimene zinkachitika m’mizinda imeneyi. Zimenezi zikusonyeza kuti nthawi zina Yehova amasankha kuti asadziwiretu zinthu zinazake. (Genesis 22:12) Koma zimenezi sizikusonyeza kuti Mulungu si wangwiro kapena kuti mphamvu zake ndi zochepa. Tikutero chifukwa Baibulo limati, “ntchito yake ndi yangwiro.” Choncho amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zake zotha kudziwiratu zam’tsogolo ndipo amachita zimenezi mogwirizana ndi cholinga chake. Sikuti nthawi zonse iye amakakamiza anthu kuti achite zimene iyeyo akufuna. * (Deuteronomo 32:4) Ndiye kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti: Ngakhale kuti Mulungu ali ndi mphamvu zodziwiratu chilichonse, amachita kusankha zimene akufuna kudziwiratu.

N’chifukwa chiyani Mulungu sateteza anthu abwino kuti asachitiridwe zinthu zoipa?

MAVUTO ENA AMAYAMBITSIDWA NDI ANTHU

Mavuto ena amene amachitika m’dzikoli amayambitsidwa ndi anthu. Baibulo limafotokoza zimene zimachitika kuti munthu afike pochita zinthu zoipa. Limati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako chake. Ndiye chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo. Nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” (Yakobo 1:14, 15) Choncho munthu akachita zinthu zoipa zimene wakhala akuzilakalaka amakumana ndi mavuto. (Aroma 7:21-23) Kuyambira kale, anthu akhala akuchita zinthu zoipa kwambiri ndipo izi zimabweretsa mavuto adzaoneni. Komanso anthu oipa amachititsa kuti anthu ena ayambe kuchita zoipa.—Miyambo 1:10-16.

Anthu akhala akuchita zinthu zoipa kwambiri ndipo izi zabweretsa mavuto osaneneka

Koma mwina mungafunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu salepheretsa anthu kuchita zinthu zoipa?’ Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tiganizire mmene Mulungu analengera anthu. Baibulo limati Mulungu analenga munthu m’chifaniziro chake. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu angathe kusonyeza makhalidwe amene Mulungu ali nawo. (Genesis 1:26) Ndipotu Mulungu anapatsa anthu ufulu wosankha. Choncho anthu angathe kusankha kumukonda komanso kuchita zimene iye amafuna. (Deuteronomo 30:19, 20) Zikanakhala kuti Mulungu amangokakamiza anthu kuti azichita zimene iyeyo akufuna, kodi sikukanakhala kuwalandanso ufuluwo? Ndiye kutitu anthu akanakhala ngati makina amene amangochita zinthu mogwirizana ndi mmene anawapangira basi. Bwenzi zilinso chimodzimodzi zikakhala kuti Mulungu analemberatu chilichonse chimene chidzachitike pa moyo wathu. Komatu n’zosangalatsa kudziwa kuti Mulungu anatilemekeza potipatsa ufulu wosankha zochita pa moyo wathu. Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti mavuto amene anthu amayambitsa padzikoli adzapitirira mpaka kalekale.

 KODI ANTHU AMAVUTIKA CHIFUKWA CHA ZOIPA ZOMWE ANACHITA ASANABADWE MOYO UNO?

Mutafunsa munthu amene ali m’chipembedzo chachibuda kapena chachihindu funso lomwe lili pachikuto cha magazini ino, mwina angayankhe kuti, “Anthu abwino amavutika chifukwa cha zoipa zomwe anachita m’moyo wina umene anali nawo asanabadwe moyo uno. Ndipo anthu amenewa akukolola zimene anadzala m’moyo wapitawo.” *

Kuti tidziwe ngati chiphunzitsochi chili cholondola, tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya imfa. Anthu oyamba ankakhala m’munda wa Edeni ndipo Mulungu anali atauza Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:16, 17) Adamu akanamvera Mulungu, bwenzi atakhala ndi moyo kwamuyaya. Choncho, imfa inabwera chifukwa choti Adamu sanamvere Mulungu ndipo anachimwa. Ndiyeno iye atabereka ana, ‘imfa inafalikira’ kwa anawo ndipo kenako kwa anthu onse. (Aroma 5:12) N’chifukwa chake Baibulo limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa.” (Aroma 6:23) Limatinso: “Munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7) M’mawu ena tingati, munthu akamwalira amakhala kuti wapereka malipiro a machimo ake.

Anthu ambiri amene amakhulupirira kuti munthu amavutika chifukwa cha zoipa zomwe anachita asanabadwe moyo uno, sadandaula kwambiri ndi mavuto amene iwowo komanso anthu ena akukumana nawo. Iwo amaona kuti akukolola zimene anafesa. Koma vuto ndi loti anthu amenewa sakhala ndi chiyembekezo choti zinthu zoipa zidzatha. Amaona kuti chimene chingathandize munthu kuti asiye kuvutika, n’kuphunzira zinazake komanso kukhala ndi makhalidwe abwino. Amati zimenezi zingathandize kuti akadzafa, asadzabadwenso kwina n’kumakazunzika. Koma izi n’zosagwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. *

AMENE ANAYAMBITSA MAVUTO ONSE

Kodi mukudziwa kuti amene anayambitsa mavuto padzikoli ndi Satana Mdyerekezi, yemwenso ndi “wolamulira wa dziko?”Yohane 14:30.

Komatu amene anayambitsa mavuto padzikoli si anthu. Satana Mdyerekezi, yemwe poyamba anali mngelo wokhulupirika wa Mulungu, “sanakhazikike m’choonadi” ndipo anachititsa kuti anthu oyamba achimwire Mulungu. (Yohane 8:44) Iye anachita zimenezi m’munda wa Edene. (Genesis 3:1-5) Yesu Khristu ananena kuti Satana ndi ‘woipa’ komanso “wolamulira wa dziko.” (Mateyu 6:13; Yohane 14:30) Masiku ano anthu ambiri amatsatira zofuna za Satana ndipo sachita zimene Yehova amafuna. (1 Yohane 2:15, 16) N’chifukwa chake lemba la 1 Yohane 5:19 limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” Palinso angelo ena oipa amene anachimwira Mulungu n’kugwirizana ndi Satana. Baibulo limasonyeza kuti Satana ndi ziwanda zake “akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Komanso akubweretsa ‘tsoka padziko lapansili.’ (Chivumbulutso 12:9, 12) Choncho Satana Mdyerekezi ndiye woyenera kuimbidwa mlandu kwambiri chifukwa ndi amene anayambitsa mavuto padzikoli.

Monga taonera, Mulungu si amene amachititsa kuti anthu, kaya oipa kapena abwino, azivutika. M’malomwake iye walonjeza kuti adzachotsa mavuto onse. Nkhani yotsatirayi ikufotokoza zimenezi.

^ ndime 3 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 11 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu walola kuti zoipa zizichitika, werengani mutu 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 16 Kuti mudziwe zambiri za chiphunzitso choti anthu amavutika chifukwa cha zoipa zomwe anachita asanabadwe moyo uno, onani kabuku kachingelezi kakuti, What Happens to Us When We Die? Kabukuka ndi kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 18 Kuti mudziwe zimene zimachitika munthu akamwalira komanso chiyembekezo choti akufa adzauka, werengani mutu 6 ndi 7 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?