Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  April 2014

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi moyo unali wotani kwa akapolo amene ankakhala m’madera a ufumu wa Roma?

Kachitsulo kamene akapolo ankavekedwa m’khosi ku Roma

Mu ufumu wa Roma munali akapolo ambiri amene anagwidwa kunkhondo komanso kubedwa kuchokera kumadera ena. Akapolo amenewa ankagulitsidwa ndipo analibenso mwayi wobwerera kwawo komanso kuonana ndi abale awo.

Akapolo ambiri ankagwira ntchito yakalavulagaga m’migodi, ndipo ena ankafa pogwira ntchitoyi. Koma akapolo omwe ankagwira ntchito m’minda komanso m’nyumba za anthu, sankavutika kwambiri kuyerekeza ndi akapolo omwe ankagwira ntchito m’migodi. Akapolo ankakakamizidwa kuvala chinthu chinachake chopangidwa ndi chitsulo m’khosi mwawo. Pachitsulopo ankalembapo mawu onena za mphoto imene munthu yemwe angagwire kapolo wothawayo n’kumubweretsa kwa mbuye wake, adzapatsidwe. Akapolo amene ankakonda kuthawa ankawadinda ndi chitsulo cha moto pamphumi pawo. Nthawi zambiri ankawadinda chilembo cha F posonyeza kuti munthuyo amathawathawa.

Buku la m’Baibulo la Filimoni, limafotokoza kuti mtumwi Paulo anatumiza Onesimo, kapolo amene anali atathawa, kwa mbuye wake Filimoni. Ngakhale kuti Filimoni akanatha kukhaulitsa Onesimo chifukwa chomuthawa, Paulo anapempha Filimoniyo kuti ‘amulandire ndi manja awiri’ chifukwa cha chikondi komanso chifukwa chakuti anali m’bale wake wauzimu tsopano.—Filimoni 10, 11, 15-18.

N’chifukwa chiyani ku Foinike kunkadziwika ndi utoto wofiirira?

Foinike linali dera limene masiku ano limadziwika kuti Lebanon. Derali linkadziwika ndi utoto wofiirira womwe unkachokera ku Turo. Mfumu Solomo ya ku Isiraeli inakongoletsa kachisi ndi “nsalu zofiirira” zimene zinapangidwa ndi munthu wina waluso wa ku Turo.—2 Mbiri 2:13, 14.

Utoto wa ku Turo unali wodula kwambiri pa nthawi imeneyo ndipo chimodzi mwa zifukwa zake n’choti pankakhala chintchito chachikulu kuti apange utotowu. Choyamba, asodzi ankatolera nkhono * zambirimbiri kuchokera m’nyanja. Pankafunika nkhono 12,000 kuti apange utoto wokwanira kunyika nsalu imodzi. Kenako, ankafunika kuchotsa nkhonozi m’zikamba zake n’cholinga choti azifinye. Ndipo madzi ake ankawasakaniza ndi mchere n’kuwaika pa dzuwa kwa masiku atatu. Kenako ankawaika mumphika n’kuthiramo madzi a m’nyanja ndipo ankavundikira n’kuwawiritsa kwa masiku angapo.

Kwa zaka zambiri, anthu a ku Foinike anakhala akugulitsa utoto wochokera ku Turo komanso kupanga utotowu. Iwo ankachita zimenezi kudzera m’malonda amene ankachita komanso chifukwa choti anagonjetsa madera osiyanasiyana. Zotsalira za zinthu zimene anthu a ku Foinike ankapangira utoto, anazipeza ku madera ozungulira nyanja ya Mediterranean komanso dera lina lakumadzulo, ku Spain.

^ ndime 8 Nkhonozi zinkakhala zotalika pafupifupi masentimita 8.