Nkhani ili m’munsiyi ikusonyeza mmene a Mboni za Yehova amachitira akamakambirana ndi anthu nkhani za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti mtsikana wina wa Mboni, dzina lake Alinafe, wafika pakhomo pa Mayi Phiri.

KODI MULUNGU AMAMVA BWANJI ANTHUFE TIKAMAVUTIKA?

Alinafe: Muli bwanji Mayi Phiri. Ndasangalala kuti ndakupezani.

Mayi Phiri: Ndili bwino, inenso ndasangalala kuti mwabweranso.

Alinafe: Tsiku lijali tinakambirana funso lakuti, ‘Kodi Mulungu amamva chisoni tikamavutika?’ * Munandiuza kuti mwakhala mukudzifunsa funso limeneli kwa nthawi yaitali, makamaka kuyambira pamene amayi anu anavulala pa ngozi ya galimoto. Koma kodi mayi anu akupeza bwanji?

Mayi Phiri: Ali bwino choncho. Poti amangoti lero adzukeko bwino, mawa adwale. Koma lero bola adzukako bwino.

Alinafe: Ndasangalala kuti akupezako bwino. Ndikudziwa kuti kudwazika matenda n’kovuta, komabe mukuyesetsa kuti musamangokhala wokhumudwa chifukwa cha zimenezi.

Mayi Phiri: N’kovutadi. Moti nthawi zina ndimadzifunsa kuti, akhala chonchi mpaka liti?

Alinafe: Ndi mmene aliyense angamvere. Tsiku lijali, ndinati lero tidzakambirana funso lakuti, ‘Popeza Mulungu ali ndi mphamvu zothetsera mavuto, n’chifukwa chiyani walola kuti mavutowa azichitikabe?’

Mayi Phiri: Ndakumbukiradi.

Alinafe: Tisanakambirane yankho la funso limeneli, tiyeni tikumbutsane kaye zimene tinakambirana tsiku lijali.

Mayi Phiri: Chabwino.

Alinafe: Choyamba, tinaona kuti m’Baibulo muli nkhani ya mtumiki wina wa Mulungu amene ankadabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika. Koma Mulungu sanam’dzudzule chifukwa cha zimenezi komanso sanamuuze kuti alibe chikhulupiriro.

Mayi Phiri: Ndakumbukiradi kuti tinakambirana zimenezi.

Alinafe: Tinaphunziranso kuti Mulungu sasangalala akamationa tikuvutika. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu ake akamavutika, ‘iyenso ankavutika.’ * Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti Mulungu amamva chisoni tikamavutika?

Mayi Phiri: N’zolimbikitsadi.

Alinafe: Pomalizira, tinagwirizana pa mfundo yoti, popeza Mlengi ali ndi mphamvu zambiri, atafuna angathe kuthetsa mavuto amene ali padzikoli.

Mayi Phiri: N’zoonadi. Koma ine ndikudabwa kuti n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti zoipa zizichitikabe, pomwe iyeyo ali ndi mphamvu zoti akhoza kuzithetsa?

NDANI ANANENA ZOONA?

Alinafe: Kuti tipeze yankho la funso lanuli, tiyeni tiyambe n’kukambirana nkhani imene ili koyambirira kwa buku la Genesis. Kodi munamvapo za Adamu  ndi Hava komanso za chipatso chimene Mulungu anawauza kuti asadye?

Mayi Phiri: Ee, ndinaphunzirapo nkhani imeneyi ku Sande Sukulu. Mulungu anawauza kuti asadye zipatso za mtengo winawake koma iwo sanamvere ndipo anadya zipatso za mtengowo.

Alinafe: Mwafotokoza bwino. Ndiye tiyeni tione zimene zinachititsa kuti Adamu ndi Hava adye zipatso za mtengowo, komwe kunali kuchimwira Mulungu. Zimene zinachitikazo zitithandiza kudziwa kuti n’chifukwa chiyani anthufe timavutika. Kodi mungawerenge lemba la Genesis 3, vesi 1 mpaka 5?

Mayi Phiri: Ee ndikhoza kuwerenga. “Tsopano njoka inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: ‘Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?’ Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: ‘Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, “Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.”’ Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.’”

Alinafe: Zikomo, mwawerenga bwino. Tatiyeni tikambirane bwinobwino mavesi amenewa. Choyamba, onani kuti njoka inalankhula ndi Hava. Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso, limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ndi amene analankhula ndi Hava kudzera mwa njokayo. * Ndipo anafunsa Hava za lamulo limene Mulungu anawapatsa. Kodi mwaona chilango chimene Mulungu ananena kuti Adamu ndi Hava adzalandira akadzadya zipatso za mtengowo?

Mayi Phiri: Ee, anawauza kuti adzafa.

Alinafe: Zoona zimenezo. Taonaninso zimene Satana ananena potsutsa zimene Mulungu ananena. Iye anati: “Kufa simudzafa ayi.” Apatu Satana ankanena kuti Mulungu ndi wabodza.

Mayi Phiri: Ndinali ndisanamvepo zimenezi.

Alinafe: Ponena kuti Mulungu ndi wabodza, Satana anayambitsa nkhani imene inafunika nthawi kuti ithetsedwe. Kodi mukudziwa chifukwa chake zili choncho?

Mayi Phiri: Ayi, sindikudziwa.

Alinafe: N’takufunsani funso ili, kodi mungatani munthu wina atanena kuti ndi wamphamvu kuposa inuyo?

Mayi Phiri: Ndikhonza kumuuza kuti tichite chinachake kuti wamphamvu adziwike.

Alinafe: Zoona. Mwina mungapeze chinthu cholemera kwambiri kuti muone amene angakwanitse kuchinyamula. Choncho sizingavute kuti anthu adziwe kuti, pakati pa inuyo ndi munthuyo, wamphamvu ndani.

Mayi Phiri: Tsopano ndayamba kumvetsa.

Alinafe: Koma bwanji zitakhala kuti munthu wina akunena kuti iyeyo ndi wachilungamo kuposa inuyo? Mwina zingakhale zovuta kuti anthu adziwe mwamsanga kuti wachilungamo ndani, si choncho?

Mayi Phiri: Zingakhaledi zovuta.

Alinafe: N’zoona, chifukwa pamafunika nthawi kuti anthu azindikire munthu wachilungamo.

Mayi Phiri: Mukutanthauza chiyani?

Alinafe: Njira yabwino yothetsera nkhaniyi ingakhale kulola kuti padutse nthawi kuti anthu aone zochita za inuyo komanso za munthu winayo, n’kuzindikira kuti wachilungamo ndani.

Mayi Phiri: Zimenezidi n’zomveka.

Alinafe: Ndiyeno tiyeni tionenso nkhani ya m’buku la Genesis ija. Kodi Satana ananena kuti iyeyo ali ndi mphamvu zambiri kuposa Mulungu?

Mayi Phiri: Ayi.

Alinafe: Mwayankha bwino. Akanakhala kuti ananena zimenezo, nthawi yomweyo Mulungu akanatha kuchita zinthu zosonyeza kuti iye ndi wamphamvu kuposa Satana. Koma Satana ananena kuti iyeyo ndi wachilungamo kuposa Mulungu. Tingati iye anauza Hava kuti, ‘Mulungu anakunamizani, ine ndi amene ndikukuuzani zoona.’

Mayi Phiri: Komaditu eti!

Alinafe: Choncho, mwanzeru zake, Mulungu anadziwa kuti njira yabwino yothetsera nkhani imeneyi n’kulola kuti papite nthawi yokwanira kuti chilungamo chidziwike. Anadziwa kuti pakapita nthawi, zidzadziwika kuti ananena zoona ndani, nanga wabodza ndani.

 PAMENE PANAGONA NKHANI

Mayi Phiri: Koma pamene Hava anafa, sindiye kuti zinadziwika kuti Mulungu ndi amene ananena zoona?

Alinafe: Tingati zinadziwikadi. Komabe nkhaniyi inali isanathe. Taonaninso zimene vesi 5 likunena. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene Satana anauza Hava?

Mayi Phiri: Anamuuza kuti akadya zipatso za mtengo woletsedwa, maso ake adzatseguka.

Alinafe: Zoona, ndipo anamuuzanso kuti ‘adzafanana ndi Mulungu ndipo adzadziwa zabwino ndi zoipa.’ Choncho, Satana ananena kuti Mulungu anabisira anthu zinthu zinazake zabwino.

Mayi Phiri: N’zoonadi.

Alinafe: Nkhani imeneyinso ndi yaikulu.

Mayi Phiri: Mukutanthauza chiyani?

Alinafe: Satana anatanthauza kuti Hava, komanso anthu ena onse, angakhale mosangalala popanda kulamulidwa ndi Mulungu. Apanso Yehova anaona kuti njira yabwino yothetsera nkhaniyi, n’kumulola Satana kuti asonyeze ngati zimene ananenazo zinali zoona. Choncho Mulungu analola kuti Satana alamulire dzikoli kwa nthawi. N’chifukwa chake padzikoli pali mavuto ambiri poti Satana, osati Mulungu, ndi amene akulamulira dzikoli. * Komabe pali nkhani yabwino.

Mayi Phiri: Nkhani yabwino yotani?

Alinafe: Baibulo limasonyeza kuti Yehova sasangalala anthufe tikamavutika. Mwachitsanzo, taonani zimene Mfumu Davide inalemba pa Salimo 31:7. Davide anakumana ndi mavuto ambiri, koma tiyeni tione zimene anauza Yehova m’pemphero lake. Kodi mungawerenge vesi limeneli?

Mayi Phiri: Chabwino. Lembali likuti: “Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha, pakuti mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.”

Alinafe: Zikomo kwambiri. Choncho ngakhale kuti Davide ankakumana ndi mavuto, iye ankalimba mtima chifukwa chodziwa kuti Yehova akudziwa mavuto ake onse. Kodi si zolimbikitsa kudziwa kuti Yehova amadziwa mavuto athu onse, ngakhale amene anthu ena sangawamvetsetse?

Mayi Phiri: Koma ndiye n’zolimbikitsadi.

Alinafe: Chinanso n’chakuti Mulungu sadzalola kuti mavuto amene akuchitika padzikoli apitirire mpaka kalekale. Baibulo limaphunzitsa kuti posachedwapa, Satana sadzalamuliranso dzikoli chifukwa Mulungu adzamuchotsa. Komanso Mulungu adzakonza zinthu zoipa zonse zimene Satana wabweretsa padzikoli, kuphatikizapo mavuto amene inuyo ndi mayi anu mukukumana nawo. Bwanji ndidzabwerenso mlungu wamawa kuti ndidzakusonyezeni zimene Mulungu adzachite posachedwapa pochotsa mavuto onse padzikoli? *

Mayi Phiri: Ee mudzabwere mudzandipeza.

Kodi pali nkhani inayake ya m’Baibulo imene simumaimvetsa? Kapena mumafuna mutadziwa zimene a Mboni za Yehova amakhulupirira? Ngati ndi choncho, funsani a Mboni za Yehova ndipo adzasangalala kwambiri kukambirana nanu.