Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi Mulungu ndi wotani?

Sitingathe kuona Mulungu chifukwa iye ndi mzimu. Mulungu ndi amene analenga kumwamba, dziko lapansili komanso zinthu zonse zamoyo. Mulungu sanachite kulengedwa ndipo alibe chiyambi. (Salimo 90:2) Mulungu amafuna kuti anthu adziwe zoti iye alipo komanso kuti adziwe zolondola zokhudza iyeyo.—Werengani Machitidwe 17:24-27.

Tiyeneranso kudziwa kuti Mulungu ali ndi dzina. Tingathe kudziwa makhalidwe ake poona zinthu zimene iye analenga. (Aroma 1:20) Koma kuti timudziwe bwino, tiyenera kuphunzira Baibulo, lomwe ndi Mawu ake. Baibulo limatithandiza kudziwa kuti Mulungu ndi wachikondi.—Werengani Salimo 103:7-10.

Kodi Mulungu amamva bwanji zinthu zopanda chilungamo zikamachitika?

Mlengi wathu, Yehova, amadana ndi kupanda chilungamo ndipo iye analenga anthufe m’chifaniziro chake. (Deuteronomo 25:16) N’chifukwa chake ambirife timadananso ndi zachinyengo. Zinthu zopanda chilungamo zimene zimachitikazi, si Mulungu amene amazichititsa. Mulungu anapatsa anthu ufulu wosankha. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amagwiritsa ntchito molakwika ufulu umenewu ndipo amachita zinthu zopanda chilungamo. Zimenezi zimakhumudwitsa kwambiri Yehova.—Werengani Genesis 6:5, 6; Deuteronomo 32:4, 5.

Yehova amakonda chilungamo ndipo sadzalola kuti zinthu zopanda chilungamo zipitirire kuchitika mpaka kalekale. (Salimo 37:28, 29) Baibulo limalonjeza kuti, posachedwapa Mulungu adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo.—Werengani 2 Petulo 3:7-9, 13.

Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa zinthu zonse zopanda chilungamo