MFUMU QIN SHI HUANG

WOFUFUZA MALO, PONCE DE LEÓN

Imfa ndi mdani woopsa ndipo timayesetsa ndi mphamvu zathu zonse kuti tithane nayo. Munthu amene timamukonda akamwalira zimativuta kuvomereza kuti wapitadi. Ndipo munthu akakhala mnyamata, saganizira n’komwe zoti adzamwalira.

Anthu ambiri amakhala ndi maganizo oti moyo sufa. Ena amene anali ndi maganizo amenewa anali mafumu a ku Iguputo. Iwo ndi antchito awo anatha nthawi yambiri akuyesetsa kuti apeze njira yoti asafe. Koma manda a mafumu a ku Iguputo, ndi umboni wosonyeza kuti anthuwa sanapeze njira yogonjetsera imfa.

Nawonso mafumu a ku China sankafuna kufa ndipo anayesetsa kupeza mankhwala amene ankawaganizira kuti angapangitse kuti asafe. Mfumu Qin Shi Huang inalamula asayansi kuti apange mankhwala opatsa moyo. Asayansiwa anapangadi mankhwala posakaniza zinthu zosiyanasiyana. Koma ena mwa mankhwalawo anali ndi poizoni moti mfumuyi inafa itamwa mankhwalawa.

M’zaka za m’ma 1500 munthu wina wofufuza malo atsopano wa ku Spain, dzina lake Juan Ponce de León anayamba ulendo wodutsa nyanja ya Caribbean kuti akafufuze mankhwala othandiza kuti anthu asamakalambe. Iye anatulukira malo ena otchedwa Florida ku America ndipo anamwalira patatha zaka zochepa atamenyana ndi anthu a kuderali. Mpaka pano palibe anapeza mankhwala amene angapangitse kuti anthufe tisamakalambe.

Anthu onsewa ankafuna kugonjetsa imfa. Ngakhale kuti njira zimene ankagwiritsa ntchitozi sizinali zabwino, tonsefe timafunadi imfa itagonjetsedwa. Izi zili choncho chifukwa munthu aliyense amafuna kukhala ndi moyo kwamuyaya.

KODI PALI ANGAGONJETSE IMFA?

N’chifukwa chiyani timadana ndi imfa? Baibulo limanena chifukwa chake timadana nayo. Ponena za Mlengi wathu Yehova, * limati: “Chilichonse iye  anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake. Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Mlaliki 3:11) Anthufe timafuna kusangalala ndi moyo padzikoli kwamuyaya, osati kwa zaka 80 zokha mwinanso osafika n’komwe zaka zimenezi.—Salimo 90:10.

N’chifukwa chiyani Mulungu anatipatsa “mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale”? Kodi ankafuna kuti tizingolakalaka kukhala ndi chinthu choti sitingakhale nacho? Ayi. Mulungu anatilonjeza kuti imfa idzatha. M’Baibulo muli mavesi ambiri amene amasonyeza kuti Mulungu adzathetsa imfa n’kubweretsa moyo wosatha.—Onani bokosi lakuti,  “Imfa Idzagonjetsedwa.”

Pa nkhaniyi, Yesu ananena kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Choncho nkhondo yolimbana ndi imfa idzatha ndipo imfayi idzagonjetsedwa. Komabe Yesu anatitsimikizira kuti Mulungu yekha ndi amene angatimenyere nkhondo imeneyi.

^ ndime 9 Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.