Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“M’mapiri Ake Mudzakumbamo Mkuwa”

“M’mapiri Ake Mudzakumbamo Mkuwa”

Mu March 1961, gulu lina la anthu ofukula zinthu zakale linkafufuza zinthu m’zigwa ndi m’mapanga a m’chipululu cha Yudeya. Kenako anthu ena a m’gululi anafika paphanga lina lomwe lili pamalo okwera kwambiri. Iwo sanaganize kuti pamalowa angapezepo zinthu zakale zamtengo wapatali ngati mipukutu ya ku Nyanja Yakufa. Koma anadabwa kwambiri atapeza zinthu zamtengo wapatali, zimene n’kupita kwa nthawi anayamba kuzitchula kuti Nahal Mishmar.

ZINTHU zimenezi zinalipo 400 ndipo zambiri zinali za mkuwa. Zinthuzi anazipeza mumng’alu winawake ndipo zinali zitakulungidwa mu mphasa. Zina mwa zinthuzi zinali zipewa, ndodo zachifumu komanso zipangizo zina. Zimene anapezazi ndi zochititsa chidwi kwa anthu amene amawerenga Baibulo, chifukwa lemba la Genesis 4:22 limanena za Tubala-kaini kuti anali “mmisiri wosula zipangizo zamtundu uliwonse, zamkuwa ndi zachitsulo.”

Anthu amene anapeza zinthuzi sadziwa kuti zinachokera kuti, ndipo anaziikapo ndani. Komabe kupezeka kwa zinthu zimenezi kumasonyeza kuti anthu a m’madera otchulidwa m’Baibulo ankakumba, kuyenga komanso kupanga zinthu za mkuwa.

MALO AMENE MUNKAPEZEKA MKUWA M’DZIKO LOLONJEZEDWA

Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawauza kuti: “M’mapiri ake [a dzikolo] mudzakumbamo mkuwa.” (Deuteronomo 8:7-9) Ofukula zinthu zakale anapeza kuti ku Isiraeli komanso ku Yorodano kuli malo monga Feinan, Timna ndi Khirbat en-Nahas, kumene anthu akale ankakumbako komanso kuyenga miyala yamtengo wapatali. Kodi malo amenewa akusonyeza chiyani?

Nthaka ya ku Feinan ndi ku Timna ili ndi malo okumbikakumbika amene kwa zaka zoposa 2,000 anthu okumba miyala ankakumbamo mkuwa. Ngakhale masiku ano kumalowa kumapezeka miyala yokhala ndi zotsalira za mkuwa. Anthu amenewa ankakumba ndiponso kugoba miyalayi mwakhama kwambiri pogwiritsa ntchito zokumbira zamiyala, n’cholinga choti achotse mkuwa umene unkakhala pakati pa miyala. Akaona kuti pamalo amene akumbawo sipakupezekanso mkuwa, ankapitiriza kukumba pansi kwambiri pogwiritsa ntchito zokumbira zachitsulo zimene zinkapangitsa kuti phangalo likhale lalikulu kwambiri. M’buku la m’Baibulo la Yobu, timapezamo mawu ofotokoza zinthu ngati zimenezi. (Yobu 28:2-11) Imeneyi inali ntchito yowawa kwambiri, ndipotu kuyambira zaka za m’ma 200 C.E. kukafika zaka za m’ma 400 C.E., boma la Roma linkalamula akaidi opalamula milandu yoopsa kwambiri kuti akagwire ntchito yokumba mkuwa.

Ku Khirbat en-Nahas anapezakonso milu ikuluikulu ya zotsalira poyenga mkuwa, ndipo izi zikusonyeza kuti kuderali ankayengerako kwambiri mkuwa. Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti mkuwa wina umene unkayengedwa kumalowa unkachokera  kumadera monga Feinan ndi Timna. Poyenga mkuwa, ankapemerera moto pogwiritsa ntchito mvukuto kwa maola 8 kapena 10 ndipo motowo unkatentha kwambiri mpaka kufika madigiri 1,200. Nthawi zambiri pankafunika miyala yolemera makilogalamu 5 kuti apange mkuwa wolemera kilogalamu imodzi yomwe ankatha kuigwiritsa ntchito popanga zinthu zosiyanasiyana.

MMENE AISIRAELI ANKAGWIRITSIRA NTCHITO MKUWA

Paphiri la Sinai, Mulungu anauza Aisiraeli kuti agwiritse ntchito mkuwa pomanga chihema ndipo patapita nthawi, anagwiritsanso ntchito mkuwa pamanga kachisi ku Yerusalemu. Ndipotu Aisiraeliwo ankatha kuyenga okha mkuwawo. (Ekisodo chaputala 27) N’kutheka kuti Aisiraeli ankadziwa kale kuyenga zitsulo asanapite ku Iguputo, apo ayi ndiye kuti anaphunzira ku Iguputoko. Pa nthawi imene anali pa ulendo wochokera ku Iguputo anapanga mwana wa ng’ombe wopangidwa ndi golide. Iwo anathanso kupanga zipangizo zamkuwa monga beseni lalikulu, mapoto, mafosholo ndi mafoloko, zomwe ankazigwiritsa ntchito pachihema.—Ekisodo 32:4.

Ali m’chipululu, mwina pafupi ndi dera lotchedwa Punoni (lomwe masiku ano ndi Feinan), limene kunkapezeka mkuwa wambiri, Aisiraeli anayamba kudandaula za mana komanso kusowa kwa madzi. Powalanga, Yehova anatumiza njoka zapoizoni zimene zinapha anthu ambiri. Aisiraeli atalapa, Mose anawachonderera kwa Yehova ndipo Yehovayo anamuuza kuti apange chifanizo cha njoka ya mkuwa n’kuchipachika pamtengo. Nkhaniyi imati: “Munthu akalumidwa ndi njoka n’kuyang’ana njoka yamkuwayo, anali kukhalabe ndi moyo.”—Numeri 21:4-10; 33:43.

KUCHULUKA KWA MKUWA UMENE MFUMU SOLOMO INALI NAWO

Mbali zambiri za kachisi wa ku Yerusalemu zinali zopangidwa ndi mkuwa

Mfumu Solomo inagwiritsa ntchito mkuwa wambiri pomanga kachisi ku Yerusalemu. Wambiri mwa mkuwa umene Solomo anagwiritsa ntchitowu, unali wochokera kwa Davide, bambo ake, womwe anaupeza atagonjetsa Asiriya kunkhondo. (1 Mbiri 18:6-8) “Thanki yamkuwa” imene ansembe ankagwiritsa ntchito pa utumiki wawo inali yaikulu malita 66,000 ndipo mwina inkalemera matani 30. (1 Mafumu 7:23-26, 44-46) Ndiye panalinso zipilala ziwiri za mkuwa zomwe zinali pakhomo la kachisi. Zipilalazi zinali ndi zibowo zazikulu kuposa mita imodzi, khoma lake linali lonenepa masentimita 7 ndi hafu ndipo zinali zazitali mamita 8. Pamwamba pa zipilalazi panali mitu yotalika kupitirira pang’ono mamita awiri. (1 Mafumu 7:15, 16; 2 Mbiri 4:17) Ndiye tangoganizani kuchuluka kwa mkuwa umene anagwiritsa ntchito kupanga zinthu zimenezi.

Ngakhalenso anthu wamba ankagwiritsa ntchito mkuwa pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, timawerenga za zinthu monga maunyolo, zida zoimbira, zitseko komanso zida za nkhondo zopangidwa ndi mkuwa. (1 Samueli 17:5, 6; 2 Mafumu 25:7; 1 Mbiri 15:19; Salimo 107:16) Komanso Yesu ananena za kusatenga “mkuwa” m’zikwama za ndalama ndipo mtumwi Paulo anatchula za “Alekizanda, wosula zinthu zamkuwa.”—Mateyu 10:9; 2 Timoteyo 4:14.

Anthu ofukula zinthu zakale ndiponso akatswiri a mbiri yakale akufufuzabe kuti adziwe kumene kunachokera mkuwa wotchulidwa m’Baibulo komanso zinthu zotchedwa Nahal Mishmar zija. Komabe mfundo ndi yoti, monga mmene Baibulo limanenera, dziko limene Aisiraeli anapatsidwa linalidi ‘dziko labwino, . . . limene m’mapiri ake ankakumbamo mkuwa.’—Deuteronomo 8:7-9.