Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NSANJA YA OLONDA December 2013 | Kodi Timafunikiradi Mulungu?

Anthu ambiri amaona kuti safunikira Mulungu ndipo alibe nthawi yoganizira za Mulungu. Kodi kudziwa Mulungu kuli ndi phindu lililonse?

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Ena Amaganiza Kuti Anthufe Sitifunikira Mulungu?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chifukwa chake anthu ambiri amene amati amakhulupirira kuti kuli Mulungu, amachita zinthu ngati Mulungu kulibe.

NKHANI YAPACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Timafunikira Mulungu?

Werengani kuti mudziwe mmene kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu kungatithandizire kuti tikhale ndi moyo wosangalala.

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndinasankha Kutumikira Yehova Moyo Wanga Wonse

Kutatsala miyezi yochepa kuti amalize maphunziro a zomangamanga, Bill Walden anaganiza zoyamba kutumikira Yehova. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mmene kugwira ntchito yolalikira kunasinthira moyo wake.

YANDIKIRANI MULUNGU

“Taonani! Zinthu Zonse Zimene Ndikupanga N’zatsopano”

Kodi mumafuna mutakhala m’dziko lopanda imfa komanso mavuto ena? Werengani kuti mudziwe mmene Mulungu adzakwaniritsire malonjezo ake.

“M’mapiri Ake Mudzakumbamo Mkuwa”

Posachedwapa, anthu ena ofukula zinthu zakale apeza zinthu zimene zingatithandize kudziwa mmene anthu akale ankagwiritsira ntchito mkuwa.

PHUNZITSANI ANA ANU

Kodi Yesu Khristu Tizimukumbukira Bwanji?

Kodi Yesu tizimukumbukira ngati mwana wakhanda? Kodi anthu amene amatchulidwa kuti anzeru akum’mawa anali ndani? Kodi Yesu akuchita chiyani panopa?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi cholinga cha kubweranso kwa Yesu n’chiyani? Kodi adzabwera bwanji, nanga akadzabwera adzachita chiyani?

Zina zimene zili pawebusaiti