Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  August 2013

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi Mulungu amamva mapemphero onse?

Mulungu amamva aliyense akamapemphera. (Salimo 145:18, 19) Mawu ake, omwe ndi Baibulo, amatilimbikitsa kuti tizimuuza chilichonse chomwe chimatidetsa nkhawa. (Afilipi 4:6, 7) Koma pali mapemphero ena amene Mulungu samasangalala nawo. Mwachitsanzo, samafuna kuti anthu azinena mapemphero ochita kuloweza.—Werengani Mateyu 6:7.

Yehova samvetseranso mapemphero a anthu amene samvera malamulo ake mwadala. (Miyambo 28:9) Mwachitsanzo, kale kwambiri, Mulungu anakana kumvetsera mapemphero a Aisiraeli amene anali ndi mlandu wakupha anthu. Zimenezi zikusonyeza kuti pali zinthu zimene tiyenera kuchita kuti Mulungu azimva mapemphero athu.—Werengani Yesaya 1:15.

Kodi tizitani kuti Mulungu azimva mapemphero athu?

Mulungu sangamve mapemphero athu ngati tilibe chikhulupiriro. (Yakobo 1:5, 6) Koma tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu aliko komanso kuti amatidera nkhawa. Tikhoza kulimbitsa chikhulupiriro chathu tikamaphunzira Baibulo chifukwa munthu amakhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati ali ndi umboni wodalirika womwe umapezeka Baibulo.—Werengani Aheberi 11:1, 6.

Tiyeneranso kupemphera kuchokera pansi pa mtima komanso modzichepetsa chifukwa ngakhale Yesu ankapemphera modzichepetsa. (Luka 22:41, 42) Choncho, m’malo momangomuuza Mulungu zoti atichitire, tiziyesetsa kuwerenga Baibulo kuti tizidziwa zimene amafuna. Zimenezi zingatithandize kuti tizipemphera mogwirizana ndi chifuniro chake.—Werengani 1 Yohane 5:14.

Onaninso

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu

Kodi Mulungu amamvetsera mukamapemphera? Kuti mupeze yankho la funso limeneli, muyenera kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya pemphero.