Kodi Mulungu angatikhululukire machimo athu?

N’zotheka anthufe kumachita zinthu zokondweretsa Mulungu

Baibulo limanena kuti tonse ndife ochimwa chifukwa choti tinatengera uchimo kwa kholo lathu Adamu. N’chifukwa chake nthawi zina timachita zinthu zoipa zimene pambuyo pake timakhumudwa nazo. Koma Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wa Mulungu, anatifera kuti tizitha kukhululukidwa. Choncho, nsembe yake ya dipo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.—Werengani Aroma 3:23, 24.

Anthu ena anachitapo machimo akuluakulu ndipo amakayikira ngati Mulungu angawakhululukire. Koma chosangalatsa n’chakuti Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Magazi a Yesu Mwana wake akutiyeretsa ku uchimo wonse.” (1 Yohane 1:7) Yehova ndi wofunitsitsa kukhululukira aliyense, ngakhale atachita tchimo lalikulu bwanji, pokhapokha ngati munthuyo walapa kuchokera pansi pa mtima.—Werengani Yesaya 1:18.

Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu azitikhululukira?

Ngati tikufuna kuti Yehova Mulungu azitikhululukira tifunika kuphunzira zambiri za iyeyo zomwe zikuphatikizapo kudziwa njira zake, malangizo ake komanso zimene amafuna kuti tizichita. (Yohane 17:3) Yehova amakhululukira aliyense amene amalapa machimo ake n’kusiya kuchita zoipazo.—Werengani Machitidwe 3:19.

Ndipo n’zotheka anthufe kumachita zinthu zokondweretsa Mulungu. Yehova amatimvetsa tikalakwitsa zinazake chifukwa iye ndi wachifundo komanso ndi wokoma mtima. Kudziwa kuti Yehova ndi wachifundo kuyenera kutilimbikitsa kufuna kuphunzira zimene tingachite kuti tizimukondweretsa.—Werengani Salimo 103:13, 14.