Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  April 2013

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi N’zotheka Kumvetsa Bwino Zimene Baibulo Limaphunzitsa?

Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Lili ngati kalata yochokera kwa bambo wachikondi. (2 Timoteyo 3:16) M’Baibulo, Mulungu anatifotokozera zimene tingachite kuti tizimusangalatsa, chifukwa chake walola kuti padzikoli pakhale mavuto komanso zimene adzachitire anthu m’tsogolo. Koma aphunzitsi achipembedzo amapotoza zimene Baibulo limaphunzitsa ndipo izi zachititsa kuti anthu ambiri aziona kuti n’zosatheka kumvetsa bwino Baibulo.—Machitidwe 20:29, 30.

Yehova Mulungu amafuna kuti tidziwe zoona zokhudza iyeyo. N’chifukwa chake anatipatsa buku lonena za iye, lomwe ndi losavuta kumvetsa.—Werengani 1 Timoteyo 2:3, 4.

Kodi mungatani kuti muzilimvetsa bwino Baibulo?

Sikuti Yehova anangotipatsa Baibulo. Iye amatithandizanso kuti tilimvetse ndipo n’chifukwa chake anatumiza Yesu kuti adzatiphunzitse. (Luka 4:16-21) Yesu ankafotokoza kugwirizana kwa mavesi ndipo izi zinathandiza anthu kumvetsa Malemba.—Werengani Luka 24:27, 32, 45.

Yesu anakhazikitsa mpingo wachikhristu kuti upitirize kugwira ntchito imene anayambitsa. (Mateyu 28:19, 20) Masiku ano otsatira a Yesu enieni amathandiza anthu kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza Mulungu. Ngati mukufuna kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa, a Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani.—Werengani Machitidwe 8:30, 31.

 

Onaninso

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu

Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kupirira mavuto anu? N’chifukwa chiyani muyenera kukhulupirira maulosi a m’Baibulo?

NSANJA YA OLONDA

Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena

Ngati Baibulo linalembedwa momveka bwino, n’chifukwa chiyani muyenera kuthandizidwa kuti mumvetse zimene limanena?