Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda  |  February 2013

Mose Anali Munthu Wodzichepetsa

Mose Anali Munthu Wodzichepetsa

KODI KUDZICHEPETSA N’KUTANI?

Kudzichepetsa kumatanthauza kusakhala wodzikuza kapena wonyada. Munthu wodzichepetsa sadziona kuti ndi wapamwamba kuposa ena. Iye amazindikira kuti ndi wopanda ungwiro ndipo amadziwa kuti pali zina zimene sangakwanitse kuchita.

KODI MOSE ANASONYEZA BWANJI KUDZICHEPETSA?

Mose atapatsidwa udindo sanayambe kudzikuza. Nthawi zambiri munthu akapatsidwa udindo zimayamba kuoneka ngati ali wodzikuza kapena wodzichepetsa. Pofotokoza mfundo imeneyi, wolemba mabuku wina wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Robert G. Ingersoll, analemba kuti: “Anthu ambiri akakhala alibe udindo sadziwika ngati ali odzichepetsa kapena odzikuza. Koma kuti mudziwe ngati munthu ndi wodzichepetsa kapena ayi, mungom’patsa udindo.” Koma Mose anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kudzichepetsayi. N’chifukwa chiyani tikutero?

Mose anapatsidwa udindo waukulu popeza Yehova anamusankha kuti azitsogolera Aisiraeli. Koma Mose sanayambe kudzikuza chifukwa cha udindo umene anapatsidwawu. Mwachitsanzo, taganizirani zimene iye anachita atafunsidwa funso lovuta lokhudza ufulu wolandira cholowa. (Numeri 27:1-11) Funso limeneli linali lovuta chifukwa mmene akanaweruzira nkhaniyi, zikanakhudzanso kaweruzidwe ka nkhani zoterezi m’tsogolo.

Kodi Mose anatani? Kodi iye anaganiza kuti popeza ndi mtsogoleri wa Aisiraeli anali ndi ufulu wopereka maganizo ake osafunsa aliyense? Kapena iye anaganiza kuti ali ndi luso, watumikira Yehova kwa zaka zambiri komanso amamudziwa bwino Yehova choncho angathe kudziwa zoyenera kuchita pa nkhaniyi?

Mose akanakhala wodzikuza akanaganiza choncho. Koma iye anali wodzichepetsa. Baibulo limanena kuti: “Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.” (Numeri 27:5) Tangoganizani, ngakhale kuti Mose anali atatsogolera Aisiraeli kwa zaka 40, iye sanadalire nzeru zake koma anadalira Yehova. Izi zikusonyezeratu kuti Mose anali wodzichepetsa kwambiri.

Mose sankaganiza kuti iye yekha ndi amene anali woyenera kukhala ndi udindo. Iye anasangalala pamene Yehova analola kuti Aisiraeli ena akhale aneneri ngati iyeyo. (Numeri 11:24-29) Komanso pamene apongozi ake anamuuza kuti agawire ena ntchito zina zimene iye ankagwira, modzichepetsa Mose anamvera malangizowo. (Ekisodo 18:13-24) Chakumapeto kwa moyo wake, ngakhale kuti anali adakali ndi mphamvu, Mose anapempha Yehova kuti asankhe munthu wina woti alowe m’malo mwake. Yehova atasankha Yoswa, Mose anathandiza Yoswa ndi mtima wonse ndipo anauza Aisiraeli kuti azimvera Yoswayo pamene ankawatsogolera kupita ku Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 27:15-18; Deuteronomo 31:3-6; 34:7) Kunena zoona Mose ankaona kuti unali mwayi waukulu kukhala mtsogoleri wa Aisiraeli. Komabe iye sankaona kuti udindo wakewo unali wofunika kwambiri kuposa anthuwo.

ZIMENE TIKUPHUNZIRA KWA MOSE:

Tisamalole udindo, mphamvu kapena luso linalake kutipangitsa kukhala odzikuza. Tizikumbukira kuti kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuposa luso limene tingakhale nalo. Kukumbukira zimenezi kudzathandiza kuti tigwire bwino ntchito imene Yehova angatipatse. (1 Samueli 15:17) Ngati tilidi odzichepetsa, tidzatsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”—Miyambo 3:5, 6.

Chitsanzo cha Mose chikutithandizanso kuti tisamangoganizira kwambiri za udindo umene tili nawo.

Koma kodi kutsatira chitsanzo cha Mose cha kudzichepetsa n’kothandiza? Inde. Kukhala wodzichepetsa kumachititsa kuti anthu azitikonda komanso asamavutike kuchita nafe zinthu. Ndiponso chofunika kwambiri n’choti kumachititsa kuti Yehova Mulungu, yemwenso ndi wodzichepetsa, azitikonda kwambiri. (Salimo 18:35) Baibulo limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Petulo 5:5) Chimenechitu ndi chifukwa chabwino kwambiri chotichititsa kukhala odzichepetsa ngati Mose.