Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

NSANJA YA OLONDA FEBRUARY 2013

Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Mose?

Werengani kuti mudziwe makhalidwe atatu mwa makhalidwe abwino amene Mose anali nawo komanso zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Mose.

Kodi Mose Anali Ndani?

Akhristu, Ayuda, Asilamu komanso anthu ena amalemekeza kwambiri munthu wokhulupirika ameneyu. Kodi inuyo mumadziwa zotani za Mose?

Mose Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba

Mose anali ndi chikhulupiriro cholimba chifukwa ankakhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza. Kodi ifeyo tingatani kuti tikhale ndi chikhulupiriro ngati chimenechi?

Mose Anali Munthu Wodzichepetsa

Anthu ambiri amaona kuti munthu wodzichepetsa ndi wofooka. Kodi Mulungu amaona bwanji nkhani ya kudzichepetsa? Kodi Mose anasonyeza bwanji kudzichepetsa?

Mose Anali Munthu Wachikondi

Mose ankakonda Mulungu komanso aisiraeli anzake. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Mose?

“Iye ndi Mulungu wa Anthu Amoyo”

Mulungu ali ndi mphamvu zothetsa imfa, ndipo walonjeza kudzaukitsa akufa. Kodi Mulungu adzachitadi zimenezi?

“Ankafuna Kuti Ndione Ndekha Kuti Zoona Ndi Ziti”

Luis Alifonso ankafuna kudzakhala mmishonale wa chipembedzo cha Mormon. Kodi kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji kuti asinthe zolinga zake komanso moyo wake?

Zimene Mungachite Ngati Muli ndi Mwana Wolumala

Werengani kuti mumve za mavuto atatu amene mwina mumakumana nawo komanso mmene Baibulo lingakuthandizireni.

Kodi Umene Ena Amati Uthenga Wabwino wa Yudasi N’chiyani?

Kodi analemba ndi Yudasi, wophunzira amene anapereka Yesu? Kodi tiyenera kusintha maganizo pa mmene timaonera Chikhristu chifukwa cha zimene zili mu uthengawu?

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Popeza Mulungu analenga zonse, kodi iye ndi amene analenga Mdyerekezi? Werengani kuti mudziwe zimene Baibulo limanena.

Zina zimene zili pawebusaiti

Khadi la M’Baibulo Lonena za Esau

Kodi Esau anasonyeza bwanji kuti sankayamikira zinthu zopatulika? Sindikizani khadili kuti mudziwe.

Tsanzirani Msamariya Wachifundo

Werengani fanizo la Msamariya wachifundo ndipo muliganizire mozama kuti muone zimene mungaphunzirepo.