Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  November 2015

 KALE LATHU

“Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni”

“Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni”

TSIKU lina mu 1931, anthu ambirimbiri anafika kuholo inayake yotchuka mumzinda wa Paris kuti adzamvetsere nkhani ya M’bale Joseph F. Rutherford. Kunabwera anthu pafupifupi 3,000 ochokera m’mayiko 23. Pa nthawiyi, M’bale Rutherford ndi amene ankatsogolera ntchito yolalikira padziko lonse. Nkhani zimene iye anakamba zinkamasuliridwa m’Chifulenchi, Chijeremani ndiponso m’Chipolishi. Mawu ake anali amphamvu ndipo aliyense ankamva bwinobwino zimene ankanena.

Msonkhanowu unathandiza kuti ntchito yolalikira iyambe kuyenda bwino ku France. Pamsonkhanowu, M’bale Rutherford analimbikitsa kwambiri anthu, makamaka achinyamata, kuti abwere kudzachita ukopotala (kapena kuti upainiya) ku France. M’bale wina wachinyamata wa ku England dzina lake John Cooke amakumbukira bwino mawu olimbikitsa a M’bale Rutherford akuti: “Achinyamatanu, musalole kuti chilichonse chikulepheretseni kuchita ukopotala.” *

John Cooke anapitadi kukathandiza ku France ndipo patapita nthawi anadzakhala mmishonale. Panalinso anthu ena ambiri amene anasamukira ku France kukachita ukopotala. (Mac. 16:9, 10) Choncho m’dzikoli, chiwerengero cha akopotala chinawonjezeka kwambiri m’chaka chimodzi chokha. Mu 1930 kunali akopotala 27 okha, koma mu 1931 chiwerengerochi chinafika pa 104. Akopotala ambiri sankadziwa Chifulenchi, ankasowa ndalama ndiponso anthu ocheza nawo. Ndiyeno n’chiyani chinawathandiza kupirira mavuto amenewa?

VUTO LOSADZIWA CHILANKHULO

Akopotala osadziwa Chifulenchi ankagwiritsa ntchito timakadi tolalikirira kuti aziuza anthu za Ufumu. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wolankhula Chijeremani amene ankalalikira molimba mtima kwambiri mumzinda wa Paris. Iye anati: “Tinkadziwa bwino kuti Mulungu wathu ndi wamphamvu kwambiri. Koma nthawi zina tinkachita mantha polalikira osati chifukwa choopa anthu koma kuopa kuti tingaiwale timawu tina tachifulenchi timene tinaloweza takuti: ‘Voulez-vous lire cette carte, s’il vous plaît?’ [kutanthauza kuti,‘Kodi mungawerenge kakhadika?’] Sitinkakayikira ngakhale pang’ono kuti ntchito yathuyo ndi yofunika kwambiri.”

Akopotala ankakwera njinga zakapalasa komanso zamoto kuti akalalikire uthenga wabwino m’madera ambiri a ku France

Nthawi zina, akopotala akamalalikira kumalo enaake, ankathamangitsidwa ndi anthu oyang’anira malowo. Mwachitsanzo, tsiku lina alongo awiri a ku England amene sankadziwa bwino Chifulenchi anapita kukalalikira kumalo enaake ndipo anakumana ndi bambo woyang’anira malowo. Iye anakwiya n’kuwafunsa kuti akufuna kuonana ndi ndani. Mmodzi wa alongowa anaona mawu enaake olembedwa pachitseko akuti: “Tournez le bouton [kutanthauza kuti, imbani belu].” Ndiyeno pofuna kuyankha bamboyo mwaulemu anati: “Tabwera kudzaonana ndi Mayi ‘Tournez le bouton.’” Alongowa atazindikira kuti zimene ananenazo zinali  zolakwika, anaseka. Kunena zoona, kuseka kunkathandiza kwambiri akopotalawa kuti asamaganizire kwambiri mavuto awo.

ANKASOWA NDALAMA NDIPONSO ANTHU OCHEZA NAWO

M’zaka za m’ma 1930, ku France nyumba zambiri zinali zopanda zipangizo zamakono ndipo zimenezi zinkapangitsa kuti akopotala azivutika. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina dzina lake Mona Brzoska ndiponso mpainiya mnzake. Mlongoyu anati: “Nyumba zimene tinkakhala sizinali zabwino kwenikweni ndipo zipangizo zake sizinkagwira bwino ntchito. Choncho m’nyengo yozizira tinkavutika kwambiri ndipo tinkasamba madzi ozizira.” Koma apainiyawa sanataye mtima ndipo wina ananena kuti: “N’zoona kuti tinalibe chilichonse koma sitinkasowa zinthu zofunika.”—Mat. 6:33.

Apainiya a ku England amene anapezeka pamsonkhano wa ku Paris mu 1931

Akopotalawa ankasowanso anthu ocheza nawo. Zinali choncho chifukwa chakuti chakumayambiriro kwa m’ma 1930, ku France kunali ofalitsa osapitirira 700, ndipo ambiri ankakhala motalikirana. Koma n’chiyani chinawathandiza kukhalabe osangalala? Mona yemwe tamutchula kale uja anati: “Kuphunzira limodzi mabuku a sosaite, kunkatithandiza kuti tisamadandaule kuti sitikuonana ndi Akhristu anzathu. Nthawi imeneyo sitinkabwerera kwa anthu amene tinawapeza mu utumiki kapena kuchititsa maphunziro a Baibulo. Choncho, madzulo tinkapeza nthawi yolemberana makalata ndi achibale ndiponso apainiya anzathu. Tinkauzana zimene takumana nazo mu utumiki komanso kulimbikitsana.”—1 Ates. 5:11.

Akopotala odziperekawa ankakhalabe osangalala ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto. Timadziwa zimenezi tikawerenga makalata amene ankatumiza ku ofesi ya nthambi. Makalata ena anali ochokera kwa anthu amene anachita upainiya ku France kwa zaka zambiri. Kuyambira mu 1931 mpaka mu 1935, mlongo wina wodzozedwa dzina lake Annie Cregeen, anachita upainiya m’madera ambiri a ku France limodzi ndi mwamuna wake. Mlongoyu analemba kuti: “Tinkasangalala kwambiri kuchita upainiya. Tinali anthu angapo amene tinkachita utumikiwu ndipo tinkagwirizana kwambiri. Tinkathandizana ndipo malinga ndi zimene mtumwi Paulo ananena, ‘ena ankabzala, ena kuthirira, koma Mulungu ndi amene ankakulitsa.’ Tikusangalala kwambiri kuti tinali ndi mwayi wogwira nawo ntchito imeneyi.”—1 Akor. 3:6.

Apainiyawo anali akhama komanso opirira ndipo chitsanzo chawo chingathandize kwambiri anthu amene akufuna kuwonjezera zimene amachita potumikira Mulungu. Panopa ku France kuli apainiya okhazikika pafupifupi 14,000. Ambiri akutumikira m’mipingo komanso m’magulu amene amalankhula zilankhulo zina. * Nawonso salola kuti chilichonse chiwalepheretse kuchita upainiya.—Nkhaniyi yachokera ku France.

^ ndime 4 Mukhoza kuwerenga zimene anthu a ku Poland anachita pothandiza pa ntchito yolalikira ku France m’nkhani yakuti, “Yehova Anakubweretsani ku France Kuti Muphunzire Baibulo,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2015.

^ ndime 13 Kuwonjezera pa mipingo yachifulenchi, m’chaka cha 2014, nthambi ya ku France inkayang’anira magulu ndiponso mipingo ina 900. Abale ndi alongo a m’magulu ndi m’mipingoyo amalalikira m’zilankhulo zokwana 70.