“Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe.”—HAB. 2:3.

NYIMBO: 128, 45

1, 2. Kodi atumiki a Yehova akhala akuchita chiyani kwa nthawi yaitali?

KWA nthawi yaitali, atumiki a Yehova akhala akuyembekezera kuti maulosi ena a m’Baibulo akwaniritsidwe. Mwachitsanzo, Yeremiya analosera kuti Yuda adzawonongedwa. Izi zinachitikadi mu 607 B.C.E. pamene Ababulo anawononga Yuda. (Yer. 25:8-11) Yesaya analoseranso kuti Yehova adzathandiza Ayuda kubwerera kwawo ndipo anati: “Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezera.” (Yes. 30:18) Nayenso Mika analemba maulosi okhudza anthu a Mulungu ndipo anati: “Koma ine ndidzadikirira Yehova.” (Mika 7:7) Kwa zaka zambirimbiri, atumiki a Mulungu ankayembekezeranso kukwaniritsidwa kwa maulosi okhudza Mesiya kapena kuti Khristu.—Luka 3:15; 1 Pet. 1:10-12. *

2 Masiku ano, palinso maulosi ena onena za Mesiya amene atumiki a Mulungu akuyembekezera. Posachedwapa Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya pothetsa mavuto onse  a anthu. Adzachita zimenezi powononga anthu oipa ndiponso kupulumutsa anthu ake m’dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Choncho tiyenera kukhalabe maso chifukwa mapeto a dzikoli ali pafupi kwambiri.

3. Kodi tingafunse funso lotani ngati takhala tikuyembekezera mapeto kwa nthawi yaitali?

3 Atumiki a Yehovafe tikuyembekezera kuti chifuniro cha Mulungu ‘chichitike padzikoli ngati mmene zilili kumwamba.’ (Mat. 6:10) Ngati takhala tikuyembekezera mapeto a dziko loipali kwa nthawi yaitali, tingafunse kuti: ‘Kodi pali zifukwa zomveka zoyembekezerabe?’ Tiyeni tione.

N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUYEMBEKEZERABE?

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezerabe?

4 Dziko loipali lidzawonongedwa posachedwapa ndipo Baibulo limatiuza zimene tiyenera kuchita. Yesu anauza ophunzira ake kuti ‘akhale maso.’ (Mat. 24:42; Luka 21:34-36) Choncho tiyenera kuyembekezerabe chifukwa Yesu anatiuza kuti tikhale maso. Izi n’zimene gulu la Yehova lakhala likuchita. Mabuku athu akhala akutilimbikitsa kuti ‘tiziyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova’ ndiponso dziko latsopano limene walonjeza.—Werengani 2 Petulo 3:11-13.

5. N’chifukwa chiyani kukhalabe maso n’kofunika kwambiri masiku ano?

5 N’zoona kuti Akhristu akale ankafunika kuyembekezerabe koma kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri masiku ano. Tikutero chifukwa chakuti chizindikiro chakuti Yesu akulamulira kumwamba ndiponso cha “mapeto a nthawi ino” chakhala chikuonekera kuyambira mu 1914. Mwachitsanzo, kuyambira m’chakachi zinthu zakhala zikuipiraipira m’dzikoli komanso uthenga wa Ufumu wakhala ukulalikidwa padziko lonse. (Mat. 24:3, 7-14) Koma Yesu sananene kuti nthawi ya mapetoyi idzatha liti. Pa chifukwa chimenechi, tiyenera kukhalabe maso kwambiri.

6. N’chifukwa chiyani tingayembekezere kuti zinthu zidzaipiraipira pamene mapeto akuyandikira?

6 Baibulo limasonyeza kuti zinthu zidzaipiraipira “masiku otsiriza” ano. (2 Tim. 3:1, 13; Mat. 24:21; Chiv. 12:12) Choncho zinthu zipitirizabe kusokonekera m’dzikoli. Koma ena angaganize kuti “mapeto a nthawi ino” akunena za nthawi ina ya m’tsogolo pamene zinthu zidzakhala zoipa kwambiri kuposa masiku ano.

7. Kodi lemba la Mateyu 24:37-39 limasonyeza kuti zinthu zidzakhala bwanji m’masiku otsiriza?

7 Koma kodi zinthu zidzaipa kufika pati “chisautso chachikulu” chisanafike? (Chiv. 7:14) Ena angaganize kuti padzakhala nkhondo m’dziko lililonse, chakudya chidzasoweratu kulikonse ndipo m’banja lililonse mudzakhala matenda. Izi zitati zichitike ngakhale anthu osakhulupirira Baibulo adzadziwiratu kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa. Koma Yesu ananena kuti anthu ambiri ‘adzanyalanyaza’ chizindikiro ndipo azidzangochita zinthu za tsiku ndi tsiku moti akamadzazindikira mudzakhala m’mbuyo mwa alendo. (Werengani Mateyu 24:37-39.) Choncho Malemba akusonyeza kuti zinthu sizidzaipa mpaka kufika poti aliyense akhulupirire kuti tili m’masiku otsiriza.—Luka 17:20; 2 Pet. 3:3, 4.

8. Kodi anthu amene akumvera malangizo a Yesu akuti ‘akhale maso’ akuzindikira chiyani?

8 Komabe chizindikirochi chiyenera kuonekera mokwanira kuti anthu amene akumvera malangizo a Yesu oti tikhalabe  maso, achizindikire. (Mat. 24:27, 42) Ndiyeno anthu amenewa akhala akuona kuti chizindikirochi chikukwaniritsidwa kuyambira mu 1914. Choncho zikuonekeratu kuti panopa tikukhala ‘m’mapeto a nthawi ino.’ Mapetowa ndi nthawi yochepa imene idzatha dziko loipali likadzawonongedwa.

9. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhalabe maso poyembekezera mapeto a dzikoli?

9 Ndiye ngati ndi choncho, kodi pali chifukwa choti Akhristu azikhalabe maso masiku ano? Inde, paja izi n’zimene Yesu ananena. Panopa tikuonanso bwinobwino chizindikiro chosonyeza kuti Khristu akulamulira. Sikuti tikungokhulupirira za m’maluwa ayi koma pali umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti ino ndi nthawi yoyenera kukhala maso n’kumayembekezera mapeto a dziko loipali.

KODI TIYENERA KUYEMBEKEZERA MPAKA LITI?

10, 11. (a) Kodi Yesu anauza ophunzira ake kuti akhoza kudzafika nthawi iti? (b) Kodi ananena kuti Akhristu ayenera kuchita chiyani ngakhale ataona kuti adikira kwa nthawi yaitali? (Onani chithunzi patsamba 14.)

10 Ambirife takhala tili maso kwa zaka zambiri. Koma si bwino kuyamba kuodzera panopa chifukwa choona kuchedwa. Tiyenera kukhala okonzeka kuti Khristu akamadzabwera kudzawononga dziko loipali asadzatipeze tikugona. Paja Yesu anati: “Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika. Zili ngati munthu amene anali kupita kutali kudziko lina, amene anasiya nyumba m’manja mwa akapolo ake, aliyense pa ntchito yake, ndi kulamula mlonda wa pachipata kuti azikhala maso. Choncho khalani maso, pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwininyumba. Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, atambala akulira, kapena m’mawa, kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona. Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.”—Maliko 13:33-37.

11 Akhristu atazindikira kuti Yesu wayamba kulamulira mu 1914, anayamba kukonzekera podziwa kuti mapeto akhoza kufika nthawi iliyonse. Iwo anayamba kulalikira mwakhama kwambiri. Kumbukirani kuti Yesu anati akhoza kubwera “atambala akulira kapena m’mawa.” Ndiyeno kodi anati Akhristu ayenera kuchita chiyani? Iye anati: “Khalani maso.” Choncho kaya tadikira kwa nthawi yaitali bwanji, sitiyenera kuganiza kuti mapeto akuchedwa kwambiri kapena alephereka.

12. Kodi Habakuku anafunsa Yehova funso liti, nanga Yehova anamuyankha bwanji?

12 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mneneri Habakuku. Iye anauzidwa kuti alosere zoti mzinda wa Yerusalemu udzawonongedwa. Pamene iye ankayamba ntchitoyi, n’kuti ulosiwu utanenedwa kwa zaka zambiri ndipo zinthu zinali zitafika poipa. Baibulo limati ‘chilungamo chinapotozedwa chifukwa anthu oipa ankapondereza anthu olungama.’ Ndiyeno Habakuku anafunsa kuti: ‘Kodi ndidzalirira thandizo kufikira liti?’ M’malo moyankha funsoli, Yehova anangomuuza kuti aziyembekezerabe koma anamutsimikizira kuti ulosiwo sudzachedwa kukwaniritsidwa.—Werengani Habakuku 1:1-4; 2:3.

13. (a) Kodi Habakuku sanakhale ndi maganizo ati? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kukhala ndi maganizo amenewa kukanakhala kupusa?

13 Kodi chikanachitika n’chiyani ngati  Habakuku akanagwa ulesi n’kumati: ‘Aa zoti Yerusalemu adzawonongedwa tinayamba kuzimva kalekale. Mwina sizichitika posachedwa. Ndiye ine ndizidzivutitsa kulalikira ngati kuti mzindawo uwonongedwa pompanopompano? Ndingozisiya, olalikira adzapezeka.’ Habakuku akanakhala ndi maganizo amenewa ubwenzi wake ndi Yehova ukanasokonekera ndipo mwina akanafa pa nthawi imene Ababulo ankawononga Yerusalemu.

14. Kodi chidzachitike n’chiyani tikatsatira malangizo oti tiziyembekezerabe?

14 M’dziko latsopano tizidzakumbukira kuti maulosi onse onena za mapeto a dziko loipali anakwaniritsidwa. Kuganizira zimenezi kudzatithandiza kukhulupirira kwambiri Yehova ndiponso malonjezo ake. (Werengani Yoswa 23:14.) Tidzayamikira kwambiri kuti Mulungu anasankha nthawi yabwino yowonongera dziko loipa ndiponso anatilimbikitsa kukhalabe maso pamene mapetowo ankayandikira.—Mac. 1:7; 1 Pet. 4:7.

KODI TIZICHITA CHIYANI POYEMBEKEZERAPO?

Kodi timalalikira mwakhama uthenga wabwino? (Onani ndime 15)

15, 16. N’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira mwakhama panopa?

15 Gulu la Yehova lipitirizabe kutikumbutsa kuti tizitumikira Mulungu mwakhama kwambiri podziwa kuti nthawi yomwe yatsala ndi yochepa. Lizichita zimenezi n’cholinga chotithandizanso kukumbukira kuti chizindikiro chimene Yesu anapereka chikukwaniritsidwa. Kodi tiyenera kuchita chiyani poyembekezera mapeto a dzikoli? Tiyenera ‘kupitiriza kufunafuna ufumu choyamba’ n’kumagwira nawo mwakhama ntchito yolalikira.—Mat. 6:33; Maliko 13:10.

16 Mlongo wina ananena kuti: ‘Tikamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu tikhoza kuthandiza anthu kudzapulumuka chisautso chimene chikubweracho.’ Mlongoyu ndi mwamuna wake anapulumutsidwa pa ngozi ina yoopsa ya sitima yapamadzi mu 1945 ndipo amadziwa kufunika kopulumutsa anthu. Iye ananena kuti pa nthawi ya ngoziyo mayi wina ankalira kuti: “Amayoo! Sutukesi yanga inee! Katundu wanga wodula akupitaa! Amayoo!” Koma anthu ena anazindikira kuti chofunika kwambiri ndi moyo wa anthu osati katunduyo ndipo anayesetsa kuti apulumutse anzawo amene anagwera m’madzi. Panopa, moyo wa anthu ambiri uli pa ngozi. Nafenso tiyenera kuchita zonse zimene tingathe pothandiza anthu kuti apulumuke. Tizilalikira  mwakhama n’kumathandiza anthuwo madzi asanafike m’khosi.

Kodi timasankha zochita mwanzeru kuti tisamaiwale zoti mapeto ayandikira? (Onani ndime 17)

17. Kodi tikudziwa bwanji kuti mapeto akhoza kufika nthawi iliyonse?

17 Zinthu zomwe zikuchitika padzikoli zikusonyeza kuti maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa ndipo mapeto afika posachedwapa. Lemba la Chivumbulutso 17:16 limanena kuti “nyanga 10” ndiponso “chilombo” zidzawononga Babulo Wamkulu kapena kuti zipembedzo zonyenga zonse. Koma tisamaganize kuti nthawi yoti zimenezi zichitike ili kutali. Paja Baibulo limanena kuti Mulungu ‘adzaika izi m’mitima yawo.’ Choncho zikhoza kuyambika mofulumira pa nthawi iliyonse. (Chiv. 17:17) Mapeto a dzikoli sali kutali choncho ndi bwino kukumbukira chenjezo la Yesu lakuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34, 35; Chiv. 16:15) Tiyeni tizitumikira Yehova mwakhama kwambiri podziwa kuti ‘amathandiza anthu amene akumuyembekezera.’—Yes. 64:4.

18. Kodi tidzakambirana funso liti m’nkhani yotsatira?

18 Pamene tikuyembekezera mapeto, tiyeni tizitsatira mawu a m’Baibulo amene Yuda analemba akuti: “Inu okondedwa, podzilimbitsa pamaziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana, ndi kupemphera mu mphamvu ya mzimu woyera, pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani. Chitani zimenezi pamene mukuyembekezera kuti chifundo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chidzakutsegulireni njira yoti mulandirire moyo wosatha.” (Yuda 20, 21) Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuyembekezera kwambiri dziko latsopano limene Mulungu walonjeza? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

^ ndime 1 Kuti mudziwe za maulosi ena a m’Baibulo okhudza Mesiya ndiponso kukwaniritsidwa kwake, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 200.