ANTHU ambiri amadziwa zoti Yesu anali ndi atumwi 12. Koma ena sadziwa zoti iye analinso ndi ophunzira ena aakazi omwe ankatumikira naye. Mmodzi mwa akazi amenewa anali Jowana.—Mat. 27:55; Luka 8:3.

Kodi Jowana anathandiza bwanji Yesu pa utumiki wake, nanga tikuphunzira chiyani pa chitsanzo chake?

KODI JOWANA ANALI NDANI?

Jowana anali “mkazi wa Kuza kapitawo wa Herode.” N’kutheka kuti Kuza ankayang’anira zinthu za m’nyumba ya Herode Antipa. Jowana anali mmodzi mwa akazi amene Yesu anawachiritsa ndipo iye ndi akazi ena ankayenda ndi Yesu ndi atumwi ake.—Luka 8:1-3.

Pa nthawiyo, atsogoleri achiyuda ankaphunzitsa kuti akazi sayenera kucheza ndi amuna amene sanali achibale awo. Ankanenanso kuti amuna achiyuda sayenera kulankhulalankhula ndi akazi. Koma Yesu sankatsatira miyamboyi ndipo ankalola kuti akazi okhulupirika ngati Jowana azitumikira limodzi ndi gulu lake.

Jowana ankachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti anthu ena sangasangalale nazo. Anthu onse amene anasankha kutsatira Yesu ankayenera kusintha zinthu pa moyo wawo. Ndiyeno ponena za anthuwo, iye anati: “Mayi anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsera mawu a Mulungu ndi kuwachita.” (Luka 8:19-21; 18:28-30) Timalimbikitsidwa kwambiri kudziwa zoti Yesu amaona kuti anthu amene adzipereka kuti amutsatire ali ngati achibale ake.

ANKAGWIRITSA NTCHITO CHUMA CHAKE POTUMIKIRA

Jowana ndi akazi ena ‘ankagwiritsa ntchito chuma chawo’ potumikira Yesu ndi atumwi ake. (Luka 8:3) Munthu wina analemba kuti: “Apa Luka sakutanthauza kuti akaziwa ankatumikira pophika chakudya, kutsuka mbale kapena kusoka zovala. Mwina ankachitadi zimenezi . . . , koma si zimene Luka ankatanthauza palembali.” Zikuoneka kuti akaziwa ankagwiritsa ntchito ndalama zawo, katundu wawo kapena nyumba zawo pothandiza pa ntchito yolalikira.

Yesu ndi atumwi ake sankagwira ntchito zina kuti azipeza zofunika polalikira. Iwo ankayenda pagulu la anthu pafupifupi 20 ndipo ayenera kuti analibe njira yopezera chakudya ndi zinthu zina zofunika.  N’zoona kuti anthu ankawalandira m’nyumba zawo, koma popeza ankayenda ndi “bokosi la ndalama,” zikusonyeza kuti nthawi zina ankafunika kupeza okha zinthu zofunikazi. (Yoh. 12:6; 13:28, 29) Mwina Jowana komanso akazi enawo ankapereka ndalama zopezera zinthuzi.

Ena amatsutsa zimenezi n’kumati mkazi wachiyuda sakanapeza ndalama kapena katundu. Koma mabuku ena amasonyeza kuti akazi achiyuda ankatha kupeza chuma m’njira izi: (1) ankalandira chuma cha bambo awo ngati panalibe mwana wamwamuna, (2) ankatha kungopatsidwa chumacho, (3) nthawi zina ankapatsidwa ndalama banja likatha, (4) ankapatsidwa chuma ngati mwamuna wake wamwalira kapena (5) ankatha kupeza okha chumacho pogwira ntchito.

N’zosakayikitsa kuti otsatira a Yesu ankapereka zimene akanakwanitsa. N’kutheka kuti pa gulu lawo panalinso akazi olemera. Ndiyeno ena amanena kuti Jowana analinso wolemera chifukwa choti anakwatiwa ndi mwamuna woyang’anira nyumba ya Herode. N’kuthekanso kuti mayi ngati Jowana ndi amene anapatsa Yesu malaya opanda msoko. Munthu wina analemba kuti chovala ngati chimenechi chinali chodula kwambiri moti “mkazi wa msodzi sakanatha kuchigula.”—Yoh. 19:23, 24.

Malemba sanena mwachindunji kuti Jowana ankapereka ndalama. Koma zomwe tikudziwa n’zakuti ankachita zimene akanakwanitsa potumikira ndipo tikhoza kuphunzira zambiri pa chitsanzo chake. Nafenso tingasankhe kupereka chilichonse chimene tingathe kuti chithandize pa ntchito yolalikira. Mulungu amangofuna kuti tizipereka zinthuzo mosangalala.—Mat. 6:33; Maliko 14:8; 2 Akor. 9:7.

ZIMENE ANACHITA YESU ATAPHEDWA

Zikuoneka kuti Jowana analipo pamene Yesu ankaphedwa. Baibulo limati panalinso akazi ena ‘amene ankayenda ndi Yesu ndi kumutumikira pamene anali ku Galileya. Amayi ena ambiri amene anabwera naye limodzi kuchokera ku Yerusalemu, analiponso.’ (Maliko 15:41) Mtembo wa Yesu utachotsedwa pamtengo, ‘amayi amene anali atayenda limodzi ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsatira mtembowo kukaona manda achikumbutso ndi mmene mtembo wake anauikira. Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira.’ Luka ananena kuti amayiwo anali “Mariya Mmagadala, Jowana ndi Mariya mayi wa Yakobo.” Iwo anabwerera kumandawo pambuyo pa tsiku la sabata ndipo anaona angelo amene anawauza kuti Yesu anaukitsidwa.—Luka 23:55–24:10.

Jowana ndi akazi ena okhulupirika ankachita zimene akanatha pothandiza Ambuye wawo

Pa nthawi ya mwambo wa Pentekosite mu 33 C.E, mayi a Yesu, azichimwene ake ndiponso ophunzira ena anasonkhana ku Yerusalemu. N’kutheka kuti Jowana analiponso. (Mac. 1:12-14) Popeza mwamuna wa Jowana ankagwira ntchito m’nyumba ya Herode Antipa, mwina iye ndi amene ankauza Luka zinthu zambiri zokhudza Herode. Tikuteronso chifukwa chakuti ndi Luka yekha amene analemba dzina la Jowana m’buku lake.—Luka 8:3; 9:7-9; 23:8-12; 24:10.

Chitsanzo cha Jowana chimatiphunzitsa zinthu zambiri. Iye ankachita zimene akanatha pothandiza Yesu. Ayenera kuti ankasangalala kuti chuma chake chinkathandiza Yesu, atumwi ake 12 ndiponso ophunzira ake ena pa ntchito yolalikira. Jowana ankatumikira Yesu mokhulupirika ngakhale pa nthawi yovuta. Nawonso akazi achikhristu angachite bwino kutsanzira mtima wake woopa Mulungu.