Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizithandiza Kukongoletsa Gulu la Yehova

Tizithandiza Kukongoletsa Gulu la Yehova

“Ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.”—YES. 60:13.

NYIMBO: 102, 75

1, 2. Kodi m’Malemba Achiheberi, mawu oti “chopondapo mapazi” amagwiritsidwa ntchito pofotokoza za chiyani?

YEHOVA MULUNGU ananena kuti: “Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu, ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.” (Yes. 66:1) Ndiyeno ponena za dziko lapansi, iye anati: “Ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.” (Yes. 60:13) Kodi Yehova amalemekeza bwanji malo oikapo mapazi ake? Popeza ifeyo timakhala pamalowo, kodi tiyenera kuchita chiyani?

2 M’Malemba Achiheberi, mawu oti “chopondapo mapazi” amagwiritsidwanso ntchito pofotokoza za kachisi wa ku Yerusalemu. (1 Mbiri 28:2; Sal. 132:7) Popeza kachisiyu anali ngati likulu la kulambira koona, Yehova ankaona kuti ndi wokongola kwambiri. Tingati kachisiyo ankalemekeza malo oikapo mapazi a Yehova.

3. (a) Kodi kachisi wauzimu wa Mulungu akuimira chiyani? (b) Kodi kachisiyu anayamba liti kugwira ntchito?

3 Koma masiku ano padzikoli palibe kachisi weniweni amene tinganene kuti ndi likulu la kulambira koona. M’malomwake, pali kachisi wauzimu amene amalemekeza Yehova kuposa kachisi wina aliyense. Kodi kachisi wauzimuyu akuimira chiyani?  Akuimira zimene Mulungu akuchita pothandiza anthu kuti agwirizanenso naye komanso azimulambira. Izi zikutheka chifukwa cha nsembe ya Yesu komanso udindo wake monga Mkulu wa Ansembe. Kachisiyu anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E. pamene Yesu anabatizidwa. Pa nthawiyi, iye anadzozedwa kuti akhale Mkulu wa Ansembe m’kachisi wauzimu ameneyu.—Aheb. 9:11, 12.

4, 5. (a) Kodi Salimo 99 likusonyeza kuti atumiki a Yehova amafunitsitsa kuchita chiyani? (b) Kodi aliyense ayenera kudzifunsa funso liti?

4 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kachisi wauzimuyu? Tiyenera kutamanda Yehova chifukwa cha chifundo chimene wasonyeza popereka dipo komanso tiyenera kuuza anthu za dzina lake. N’zosangalatsa kudziwa kuti masiku ano Akhristu oposa 8 miliyoni akulemekeza Yehova. Anthu a zipembedzo zina amakhulupirira kuti adzapita kumwamba ndipo amati adzatamanda Yehova akadzapita kumwambako. Koma ife timadziwa kuti tiyenera kumutamanda padzikoli ndipo nthawi yoti tiyambe ndi yomwe ino.

5 Choncho timayesetsa kutsanzira atumiki a Yehova amene afotokozedwa pa Salimo 99:1-3, 5. (Werengani.) Salimoli likusonyeza kuti Mose, Aroni ndi Samueli ankachita zonse zimene akanatha potumikira Mulungu. (Sal. 99:6, 7) Masiku anonso, pali Akhristu amene amatumikira Yehova mwakhama pabwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu. Ena amachita zimenezi podikira kupita kumwamba kukakhala ansembe limodzi ndi Yesu. Koma a “nkhosa zina” akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi. (Yoh. 10:16) Ngakhale kuti maguluwa akuyembekezera zosiyana, onse amatumikira Yehova mogwirizana pamalo oikapo mapazi ake. Koma aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikuchita zimene ndingathe pothandiza kuti zinthu ziziyenda bwino m’gulu la Yehova?’

ANTHU OTUMIKIRA M’KACHISI WA MULUNGU ANADZIWIKA

6, 7. (a) Kodi ndi mavuto otani amene anayamba mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa? (b) Kodi Yehova anali atachita chiyani pofika mu 1919?

6 Pasanathe zaka 100 kuchokera pamene mpingo wachikhristu unakhazikitsidwa, mpatuko unayamba. (Mac. 20:28-30; 2 Ates. 2:3, 4) Kuyambira nthawiyi, zinali zovuta kuzindikira anthu amene ankatumikira m’kachisi wauzimu. Koma patapita zaka zambiri, Yehova anagwiritsa ntchito Mfumu yake, Yesu Khristu, kuti akonze zinthu.

7 Pofika mu 1919, anthu amene ankatumikira m’kachisi wauzimu wa Yehova, anadziwika bwinobwino. Iwo anali atayeretsedwa ndi Yehova n’cholinga choti utumiki wawo ukhale wovomerezeka kwambiri. (Yes. 4:2, 3; Mal. 3:1-4) Izi zinayamba kukwaniritsa masomphenya amene mtumwi Paulo anaona.

8, 9. Kodi ‘paradaiso’ amene Paulo anaona akuimira zinthu ziti?

8 Masomphenya amene mtumwi Paulo anaona analembedwa pa 2 Akorinto 12:1-4. (Werengani.) Yehova anasonyeza Paulo zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. M’masomphenyawo, Paulo ‘anakwatulidwa n’kupita kumwamba kwachitatu’ kumene anaona paradaiso. Kodi ‘paradaiso’ amene anaona kumeneko akuimira zinthu ziti? Pamenepa Paulo ankanena za zinthu zitatu. Choyamba, ankanena za Paradaiso amene adzakhale padzikoli m’tsogolo. (Luka 23:43) Chachiwiri, ankanena za paradaiso wauzimu amene tili naye panopa koma yemwe tidzasangalale  naye kwambiri m’dziko latsopano. Ndiyeno chachitatu, ankanena zinthu zosangalatsa “m’paradaiso wa Mulungu” kumwamba.—Chiv. 2:7.

9 N’chifukwa chiyani Paulo ananena kuti “anamva mawu osatchulika, amene sikololeka munthu kuwanena”? Iye ankasonyeza kuti sinali nthawi yoti afotokoze mwatsatanetsatane zinthu zosangalatsa zimene anaona m’masomphenyawo. Koma masiku ano tingathe kufotokoza madalitso amene anthu a Mulungu ali nawo.

10. Kodi paradaiso wauzimu amasiyana bwanji ndi kachisi wauzimu?

10 Ambirife timadziwa kuti paradaiso wauzimu amanena za mtendere ndiponso mgwirizano umene tili nawo ndi Mulungu ndiponso Akhristu anzathu. Komabe paradaiso wauzimu ndi wosiyana ndi kachisi wauzimu. Paja kachisi wauzimu akuimira zimene Mulungu wakonza kuti tizimulambira. Koma paradaiso wauzimu akuimira mtendere ndiponso mgwirizano umene anthu a Mulungu ali nawo ndipo umasonyeza kuti akutumikira m’kachisi wauzimu.—Mal. 3:18.

11. Kodi tili ndi mwayi wogwira nawo ntchito iti?

11 N’zosangalatsa kuti kuyambira mu 1919, Yehova akulola anthu ochimwafe kugwira naye ntchito yokongoletsa ndiponso kukulitsa paradaiso wauzimu. Kodi inuyo mukugwira nawo ntchitoyi? Kodi mumafunitsitsa kugwira ntchito ndi Yehova polemekeza ‘malo oikapo mapazi ake’?

GULU LA YEHOVA LIKUKONGOLETSEDWA KWAMBIRI

12. Kodi tikudziwa bwanji kuti lemba la Yesaya 60:17 lakwaniritsidwa? (Onani chithunzi patsamba 7.)

12 Werengani Yesaya 60:17. Lembali linaneneratu kuti mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova idzasintha kwambiri. Akhristu achinyamata ndiponso amene angolowa kumene m’gulu la Yehova amawerenga kapena kumva kwa ena za kusintha kumeneku. Koma pali abale ndi alongo ena amene akhala ndi mwayi woona okha kusinthaku. N’chifukwa chake amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova akugwiritsa ntchito Yesu potsogolera gulu lake. Enafe timakhulupiriranso zimenezi chifukwa chakuti tili ndi umboni. Koma chikhulupiriro chathu chingalimbe kwambiri tikamamvetsera zimene abale ndi alongo amene aona kusintha kwa gululi angatifotokozere.

13. Kodi lemba la Salimo 48:12-14 limasonyeza kuti tili ndi udindo wotani?

13 Kaya takhala m’gulu la Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kuuza anthu ena za gululi. N’zodabwitsa kukhala m’paradaiso wauzimu tidakali m’dziko loipa lomwe anthu ake sakondana. Tiyenera kufotokozera “m’badwo wam’tsogolo” zinthu zosangalatsa zokhudza gulu la Yehova, kapena kuti “Ziyoni,” ndiponso paradaiso wauzimu.—Werengani Salimo 48:12-14.

14, 15. (a) Kodi zinthu zinasintha bwanji m’gulu la Yehova m’ma 1970? (b) Kodi kusinthaku kwathandiza bwanji m’gulu la Yehova?

14 Akhristu ena achikulire aona zinthu zina zimene zasintha m’gulu la Yehova kuti likhale lokongola kwambiri. Mwachitsanzo, kale mpingo unkatsogoleredwa ndi mtumiki wa mpingo, nthambi inkatsogoleredwa ndi mtumiki wa nthambi ndipo kulikulu kunkakhala munthu mmodzi wotsogolera zinthu. N’zoona kuti abalewo ankakhala ndi owathandiza koma iwo ndi amene ankasankha zochita. Ndiyeno m’ma 1970 izi zinasintha n’cholinga choti udindo wosankha  zochita ukhale wa gulu la abale osati munthu mmodzi. M’malo mwa mtumiki wa mpingo panakhazikitsidwa bungwe la akulu, m’malo mwa mtumiki wa nthambi panakhazikitsidwa Komiti ya Nthambi ndipo m’malo moti munthu mmodzi azitsogolera zinthu kulikulu Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linayamba kuchita zimenezi.

15 Kusintha kumeneku kwathandiza kwambiri. Zili choncho chifukwa chakuti abale anasankha kusintha zinthuzi atamvetsa zimene Malemba amanena pa nkhani yotsogolera mpingo. M’malo moyendera nzeru za munthu mmodzi, abale osiyanasiyana amathandiza kutsogolera m’gulu la Yehova.—Aef. 4:8; Miy. 24:6.

Yehova akuthandiza anthu kulikonse kuti apeze malangizo ofunika kwambiri (Onani ndime 16 ndi 17)

16, 17. Kodi ndi zinthu ziti masiku ano zimene zikukusangalatsani? Perekani chifukwa.

16 Taganiziraninso zimene zasintha m’mabuku athu. Panopa mabuku athu ndi okongola kwambiri, mumakhala nkhani zogwira mtima kwambiri komanso anthu ambiri akhoza kuwapeza kuposa kale. Muyenera kuti mumasangalala kugawira mabukuwa mu utumiki. Tikamagwiritsa ntchito webusaiti ya jw.org kuti tilalikire, timasonyeza mtima wa Yehova wofuna kuthandiza anthu kulikonse kuti apeze malangizo ofunika kwambiri.

17 Timayamikiranso kuti zinthu zinasintha kuti tikhale ndi nthawi yochita Kulambira kwa Pabanja kapena kuphunzira Baibulo patokha. Mapulogalamu a misonkhano ikuluikulu asinthanso ndipo zinthu zosangalatsa pa misonkhanoyi zimawonjezereka chaka chilichonse. Timayamikiranso kuti masiku ano pali masukulu ambiri ophunzitsa Baibulo. Zonsezi zikusonyeza kuti Yehova ndi amene akuyendetsa zinthu. Iye akupitiriza  kukongoletsa gulu lake ndiponso paradaiso wauzimu.

INUYO MUNGATHANDIZE KUKONGOLETSA PARADAISO WAUZIMU

18, 19. Kodi tingathandize bwanji kukongoletsa paradaiso wauzimu?

18 Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wokongoletsa nawo paradaiso wauzimu. Timachita zimenezi polalikira mwakhama ndiponso kuphunzitsa anthu. Tikaphunzitsa munthu mpaka kufika poti wadzipereka kwa Mulungu, timakhala titakulitsa paradaisoyu.—Yes. 26:15; 54:2.

19 Timakongoletsanso paradaisoyo poyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Izi zimathandiza kuti anthu ena aziona kuti gulu la Yehova ndi lokongola. Nthawi zambiri anthu amayamba kutumikira Yehova ndi Yesu chifukwa choona makhalidwe athu abwino ndiponso mtendere wathu osati chifukwa cha zimene timawaphunzitsa m’Baibulo.

Mukhoza kuthandiza kuti paradaiso wauzimu akule (Onani ndime 18 ndi 19)

20. Kodi tiyenera kuchita chiyani potsatira mfundo ya pa Miyambo 14:35?

20 Yehova ndi Yesu ayenera kuti amasangalala kwambiri kuona mmene paradaiso wauzimu wakongolera masiku ano. Komatu zinthu zimene zikutisangalatsa masiku anozi n’zochepa tikaziyerekezera ndi zimene zidzachitike tikamadzasintha dzikoli kukhala paradaiso weniweni. Tiyeni nthawi zonse tizikumbukira mfundo ya pa Miyambo 14:35 yakuti: “Mfumu imasangalala ndi wantchito wochita zinthu mozindikira.” Tonsefe tiyenera kuchita zinthu mozindikira pamene tikuyesetsa kukongoletsa nawo paradaiso wauzimu.