Baibulo limasonyeza kuti ku Isiraeli kunali mitengo yambiri. Kodi zimenezi n’zoona?

BAIBULO limasonyeza kuti m’madera ena a Dziko Lolonjezedwa munali mitengo yambiri. (Yos. 17:15, 18; 1 Maf. 10:27) Koma masiku ano m’madera ambiri m’dzikoli mulibe mitengo. Choncho anthu ena amakayikira zimene Baibulo limanena.

Nkhuyu

Buku lina limafotokoza kuti kale ku Isiraeli kunali mitengo yambiri kuposa yomwe iliko masiku ano. M’mapiri ambiri munali mitengo ya mitundu yosiyanasiyana monga paini. Ndiponso m’dera la Sefela, lomwe lili pakati pa mapiri ndi nyanja ya Mediterranean, munali mitengo yambiri ya mkuyu.

Buku linanso limanena kuti malo ena ku Isiraeli masiku ano kulibiretu mitengo. Limafotokoza kuti mitengoyi inkatha pang’onopang’ono ndipo limati: “Anthu ndi amene awononga kwambiri mitengo pofuna kupeza malo olima, malo odyetsera ziweto, mitengo yomangira nyumba ndiponso nkhuni.”