Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  July 2015

“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”

“Chipulumutso Chanu Chikuyandikira”

“Mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.”—LUKA 21:28.

NYIMBO: 133, 43

1. N’chiyani chinachitika ku Yerusalemu mu 66 C.E.? (Onani chithunzi pamwambapa.)

YEREKEZERANI kuti ndinu mmodzi wa Akhristu ku Yerusalemu m’chaka cha 66 C.E. Pali zinthu zambiri zomwe zakhala zikuchitika mumzindawu. Choyamba, bwanamkubwa wachiroma dzina lake Florus, walanda matalente 17 kukachisi. Nthawi yomweyo, Ayuda akukwiya n’kuyamba kupha asilikali achiroma mu Yerusalemu kuti azidzilamulira okha. Pasanathe miyezi itatu, ufumu wa Roma ukutumiza asilikali 30,000 motsogoleredwa ndi Cestius Gallus. Asilikaliwo akufika ku Yerusalemu ndipo Ayuda oukirawo akubisala mumpanda wa kachisi. Kenako asilikali achiroma akuyamba kugumula mpandawo. Anthu onse mumzindawo akuopa kwambiri. Kodi inuyo mungamve bwanji?

2. (a) Kodi Akhristu anafunika kutsatira chenjezo liti mu 66 C.E.? (b) Kodi anakwanitsa bwanji kuthawa?

2 Ndiyeno zili choncho, mukukumbukira mawu a Yesu akuti: “Mukadzaona magulu ankhondo atazungulira Yerusalemu, mudzadziwe kuti chiwonongeko chake chayandikira. Pamenepo amene  ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo. Amene ali m’madera akumidzi asadzalowe mumzindawo.” (Luka 21:20, 21) Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatsatire bwanji chenjezo la Yesu limeneli? Nanga zingatheke bwanji kutuluka mu Yerusalemu asilikali atazungulira mzindawu?’ Koma kenako mukudabwa kuona kuti asilikali achiromawo akubwerera. Zimenezi zikukwaniritsa mawu a Yesu akuti “masikuwo adzafupikitsidwa.” (Mat. 24:22) Tsopano muli ndi mwayi wotsatira malangizo a Yesu aja. Mofulumira inuyo pamodzi ndi Akhristu anzanu okhulupirika mukuthawira kumapiri kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano. * Kenako mu 70 C.E. gulu lina la asilikali achiroma likufika n’kuwononga Yerusalemu. Koma inu mwapulumuka chifukwa chomvera malangizo a Yesu.

3. (a) Kodi n’chiyani chidzachitike posachedwapa? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

3 Posachedwapa “chisautso chachikulu” chidzayamba. (Mat. 24:3, 21, 29) Zimene zidzachitike pa nthawiyo zidzafanana ndi zimene Yesu ananena zokhudza kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Koma chosangalatsa n’chakuti “khamu lalikulu” lidzapulumuka tsoka limeneli. (Werengani Chivumbulutso 7:9, 13, 14.) Kodi Baibulo limanena kuti chidzachitike n’chiyani pa chisautso chachikulu? Tiyenera kudziwa zimenezi kuti tidzapulumuke. Tiyeni tikambirane mwatsatanetsatane zimene zidzachitike pa chisautsochi.

KODI CHISAUTSO CHACHIKULU CHIDZAYAMBA BWANJI?

4. (a) Kodi chisautso chachikulu chidzayamba bwanji? (b) Kodi “Babulo Wamkulu” adzawonongedwa bwanji?

4 Buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:5-7) Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti hule ponena za zipembedzo zonse zonyenga. Izi n’zomveka chifukwa chakuti atsogoleri a zipembedzo akhala pa ubwenzi ndi atsogoleri andale. Iwo sanakhulupirike kwa Yesu ndiponso Ufumu wake. M’malomwake, akhala akugwirizana ndi olamulira a dzikoli ndipo achita zinthu zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo pofuna kuwasangalatsa. Iwo amasiyana kwambiri ndi odzozedwa a Mulungu omwe ali ngati anamwali oyera. (2 Akor. 11:2; Yak. 1:27; Chiv. 14:4) Koma kodi amene adzawononge “Babulo Wamkulu” ndi ndani? Yehova adzaika “maganizo ake” m’mitima ya “nyanga 10” za ‘chilombo chofiira.’ Timadziwa kuti ‘chilombo chofiira’ chikuimira bungwe la United Nations ndipo “nyanga 10” zikuimira maboma onse amene amathandiza bungweli.—Werengani Chivumbulutso 17:3, 16-18.

5, 6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti anthu onse a m’zipembedzo zonyenga sadzaphedwa pa nthawi imene Babulo Wamkulu azidzawonongedwa?

5 Kodi izi zikutanthauza kuti Babulo Wamkulu akamadzaonongedwa anthu ake onse adzaphedwa? Ayi. Mneneri Zekariya analosera za nthawi imeneyo. Ponena za munthu wina amene anali m’chipembedzo chonyenga, ulosi wake umati: “Azidzanena kuti ‘Ine si mneneri. Ndine mlimi, chifukwa munthu wina anandigula kuti ndikhale kapolo wake kuyambira ndili mnyamata.’ Akadzafunsidwa kuti, ‘Kodi zilonda zimene zili pathupi pakozi watani?’ Iye azidzayankha kuti, ‘Zilonda zimenezi zinabwera chifukwa chomenyedwa m’nyumba ya anthu amene anali kundikonda kwambiri.’” (Zek. 13:4-6) Ulosiwu ukusonyeza kuti atsogoleri ena adzasiya zipembedzo zawo n’kukanitsitsa zoti anali m’zipembedzozo.

6 Nanga n’chiyani chidzachitikire atumiki a  Mulungu pa nthawiyo? Yesu anati: “Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa.” (Mat. 24:22) Taona kale kuti chisautso cha mu 66 C.E. ‘chinafupikitsidwa.’ Ndiyeno Akhristu odzozedwa, kapena kuti anthu ‘osankhidwa,’ amene anali mu Yerusalemu komanso m’madera ozungulira anathawa. Nawonso masiku a chisautso chachikulu ‘adzafupikitsidwa’ chifukwa cha anthu ‘osankhidwa.’ Yehova sadzalola kuti “nyanga 10” zija ziwononge anthu ake. Choncho chisautsocho chidzaimitsidwa kwa kanthawi.

NTHAWI YA MAYESERO NDIPONSO CHIWERUZO

7, 8. (a) Kodi aliyense adzakhala ndi mpata wochita chiyani zipembedzo zonyenga zikadzawonongedwa? (b) Kodi atumiki a Yehova okhulupirika adzasiyana bwanji ndi anthu ena?

7 Ndiyeno kodi chidzachitike n’chiyani pambuyo poti zipembedzo zonyenga zawonongedwa? Uwu udzakhala mpata woti aliyense asonyeze zimene zili mumtima mwake. Anthu ambiri adzafuna kuti atetezedwe ndi mabungwe a m’dzikoli omwe ali ngati ‘matanthwe a m’mapiri.’ (Chiv. 6:15-17) Koma anthu a Yehova adzathawira kumalo achitetezo ophiphiritsa amene Yehova adzawakonzere. Pamene chisautso chinaimitsidwa mu 66 C.E. sinali nthawi yoti Ayuda onse alowe Chikhristu. Koma inali nthawi yoti Akhristu achite zinthu mogwirizana ndi malangizo amene anapatsidwa. Ndi mmene zidzakhalirenso masiku a chisautso chachikulu akadzafupikitsidwa. Sikuti anthu ambiri adzayamba kutumikira Yehova. Koma udzakhala mpata woti Akhristu asonyeze kuti amakonda Yehova ndiponso woti athandize abale a Khristu.—Mat. 25:34-40.

8 Sitikudziwa zonse zimene zidzachitike pa nthawiyo koma n’kutheka kuti padzafunika kusiya zinthu zina. Paja Akhristu oyambirira anafunika kusiya chuma chawo komanso kupirira mavuto osiyanasiyana kuti apulumuke. (Maliko 13:15-18) Kodi ifeyo tidzalolera kusiya zinthu zathu kuti tikhale okhulupirika kwa Mulungu? Kodi tidzamvera malangizo alionse amene tidzapatsidwe? Pa nthawiyo, atumiki a Yehova okhulupirika okha adzakhala ngati mneneri Danieli chifukwa adzapitiriza kulambira Yehova zinthu zitafika povuta.—Dan. 6:10, 11.

9, 10. (a) Kodi anthu a Yehova azidzalalikira uthenga wotani? (b) Kodi adani awo adzachita chiyani?

9 Nthawi imeneyi sidzakhala yolalikira ‘uthenga wabwino wa ufumu.’ Nthawi yochita zimenezi idzakhala itatha chifukwa “mapeto” adzakhala atafika. (Mat. 24:14) Atumiki a Yehovafe tiyenera kuti pa nthawiyo tizidzalengeza uthenga wachiweruzo woopsa. Mwina tizidzauza anthu kuti dziko loipa la Satanali latsala pang’ono kutheratu. Baibulo limayerekezera uthenga umenewu ndi matalala aakulu. Limanena kuti: “Matalala aakulu, lililonse lolemera pafupifupi makilogalamu 20, anagwera anthu kuchokera kumwamba. Anthuwo ananyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali waukulu modabwitsa.”—Chiv. 16:21.

10 Adani athu akadzaona zimenezi adzakwiya. Paja mneneri Ezekieli analosera zimene adzachite Gogi wa kudziko la Magogi kapena kuti mgwirizano wa mayiko. Ulosiwo umati: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pa tsikulo maganizo adzakubwerera mumtima mwako ndipo udzaganiza zochita chiwembu choipa kwambiri. Udzanena kuti: “Ndipita kukaukira dziko lokhala ndi midzi yopanda mipanda. Ndipita kukaukira anthu amene akukhala mwabata, popanda chowasokoneza. Ndikaukira anthu onsewo amene akukhala m’midzi yopanda mipanda ndipo alibe zotsekera ndiponso zitseko.” Udzapita kumeneko kuti ukalande ndi kutengako zinthu zambiri, ndiponso  kuti ukaukire dziko lowonongedwa limene tsopano mukukhala anthu. Udzapita kukaukira anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina, amene akusonkhanitsa chuma ndi katundu, komanso amene akukhala pakatikati pa dziko lapansi.’” (Ezek. 38:10-12) Atumiki a Yehova adzakhala osiyana kwambiri ndi anthu ena moti zidzakhala ngati ali “pakatikati pa dziko lapansi.” Adani awo akadzaona zimenezi adzapsa mtima ndipo adzafuna kuwawononga.

11. (a) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamaganizira zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu? (b) Kodi anthu adzamva bwanji akadzaona zizindikiro zakumwamba?

11 Ndiyeno kodi chidzatsatire n’chiyani? Pamene tikuyankha funsoli tiyenera kukumbukira kuti Mawu a Mulungu sanena nthawi yeniyeni pamene zinthuzo zidzachitike. Zikuoneka kuti zinthu zina zidzachitika pa nthawi yofanana. Ponena za masiku otsiriza, Yesu analosera kuti: “Padzakhala zizindikiro padzuwa, mwezi ndi nyenyezi. Padziko lapansi anthu a mitundu ina adzazunzika, ndipo adzathedwa nzeru chifukwa cha mkokomo wa nyanja ndi kuwinduka kwake. Mwakuti anthu adzakomoka chifukwa cha mantha ndi kuyembekezera zimene zichitikire dziko lapansi kumene kuli anthu, pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Kenako adzaona Mwana wa munthu akubwera mumtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Luka 21:25-27; werengani Maliko 13:24-26.) Kodi ndiye kuti kumwamba kudzaonekadi zizindikiro zoopsa? Tiyeni tingodikira. Koma kaya zinthuzo zidzachitika bwanji, chomwe tikudziwa n’chakuti adani a Mulungu adzachita mantha kwambiri.

Sitidzaopa chilichonse podziwa kuti tipulumuka basi (Onani ndime 12 ndi 13)

12, 13. (a) Kodi chidzachitike n’chiyani Yesu akadzabwera ndi “mphamvu ndi ulemerero waukulu”? (b) Kodi atumiki a Yehova adzatani pa nthawiyo?

12 Nanga chidzachitike n’chiyani Yesu akadzabwera ndi “mphamvu ndi ulemerero waukulu”? Imeneyi idzakhala nthawi yopereka mphoto kwa anthu okhulupirika komanso yolanga anthu osakhulupirika. (Mat. 24:46, 47, 50, 51; 25:19, 28-30) Malinga ndi zimene Mateyu analemba, Yesu anamaliza kufotokoza chizindikiro cha masiku otsiriza popereka fanizo la nkhosa ndi mbuzi. Iye anati: “Mwana wa munthu akadzafika mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mmene m’busa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Adzaika nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzere kwake.” (Mat. 25:31-33) Nangano n’chiyani chidzachitikire nkhosa ndi mbuzi? Anthu oipa, amene ali ngati mbuzi, “adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu.” Koma anthu olungama, omwe ali ngati nkhosa, adzalandira moyo wosatha.—Mat. 25:46.

13 Kodi anthu amene ali ngati mbuzi adzatani akadzazindikira kuti atsala pang’ono kuwonongedwa? Baibulo limati “adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni.” (Mat. 24:30) Nanga abale a Khristu limodzi ndi anzawo okhulupirika adzachita chiyani? Iwo adzakhulupirira kwambiri Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu ndipo adzatsatira malangizo a Yesu akuti: “Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.” (Luka 21:28) Pa nthawi imeneyo sitidzaopa chilichonse podziwa kuti tipulumuka basi.

ODZOZEDWA ADZAWALA MU UFUMU WA MULUNGU

14, 15. Kodi Yesu adzasonkhanitsa bwanji osankhidwa pambuyo poti Gogi wa ku Magogi wayamba kuukira anthu a Mulungu?

14 Kodi n’chiyani chidzachitike Gogi wa ku  Magogi akadzayamba kuukira anthu a Mulungu? M’Baibulo, Mateyu ndiponso Maliko anafotokoza zimene zidzachitike. Maliko anati Mwana wa munthu “adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero ake a dziko lapansi kukafika kumalekezero a m’mlengalenga.” (Maliko 13:27; Mat. 24:31) Lembali silikunena za nthawi imene odzozedwa anasankhidwa koyamba kapena za nthawi imene odzozedwa amene atsala padzikoli adzadindidwa chidindo komaliza. (Mat. 13:37, 38) Paja iwo adzadindidwa komaliza chisautso chachikulu chisanayambe. (Chiv. 7:1-4) Ndiye kodi Yesu adzasonkhanitsa bwanji osankhidwawo? Adzachita zimenezi pamene odzozedwa amene atsala padziko lapansi adzalandire mphoto yawo kumwamba. (1 Ates. 4:15-17; Chiv. 14:1) Izi zidzachitika pa nthawi inayake pambuyo poti Gogi wa ku Magogi wayamba kuukira anthu a Mulungu. (Ezek. 38:11) Ponena za nthawi imeneyo, Yesu ananena kuti: “Olungama adzawala kwambiri ngati dzuwa mu ufumu wa Atate wawo.”Mat. 13:43. *

15 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti odzozedwa adzakwatulidwa? Anthu a m’matchalitchi ambiri amakhulupirira kuti Akhristu adzakwatulidwa ndipo adzapita kumwamba ndi matupi awo. Ndiyeno amati Yesu adzaonekanso akubwera kudzalamulira dziko lapansi. Koma Baibulo limanena kuti “chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba” komanso kuti Yesu adzabwera “pamitambo ya kumwamba.” (Mat. 24:30) Mawuwa akusonyeza kuti Yesu sadzaonekera kwa anthu. Tisaiwalenso kuti Baibulo limati: “Mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu.” Izi zikusonyeza kuti odzozedwa asanatengedwe kupita kumwamba ‘adzasandulika, m’kamphindi,  m’kuphethira kwa diso, pa kulira kwa lipenga lomaliza.’ * (Werengani 1 Akorinto 15:50-53.) Choncho odzozedwa amene atsala padzikoli adzasonkhanitsidwa pa kanthawi kochepa kwambiri.

16, 17. N’chiyani chiyenera kudzachitika ukwati wakumwamba usanachitike?

16 Ntchito yokonzekera ukwati wa Mwanawankhosa idzamalizidwa odzozedwa onse amene adakali padzikoli akadzapita kumwamba. (Chiv. 19:9) Koma pali zinthu zina zimene ziyenera kuchitika ukwatiwu usanachitike. Kumbukirani kuti odzozedwa amene ali padzikoli atatsala pang’ono kupita kumwamba, Gogi adzaukira anthu a Mulungu. (Ezek. 38:16) Pa nthawiyo, anthu a Mulunguwo adzaoneka kuti ndi osatetezeka. Koma iwo adzatsatira malangizo amene Mulungu anapereka pa nthawi ya Mfumu Yehosafati akuti: “Ulendo uno simufunikira kumenya nkhondo. Khalani m’malo anu, imani chilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani. Inu Ayuda ndi anthu a ku Yerusalemu, musaope kapena kuchita mantha.” (2 Mbiri 20:17) Koma kodi kumwamba kudzachitika chiyani pa nthawiyo? Kumbukirani kuti Gogi atayamba kuukira anthu a Mulungu, odzozedwa amene atsala padzikoli adzatengedwa kupita kumwamba. Ndiyeno lemba la Chivumbulutso 17:14 limanena zimene zidzachitike odzozedwa onse ali kumwamba. Limati adani a anthu a Mulungu “adzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosayo adzawagonjetsa. Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.” Lembali likusonyeza kuti odzozedwa onse 144,000 adzabwera limodzi ndi Yesu kudzapulumutsa anthu a Mulungu.

17 Iwo adzamenya nkhondo ya Aramagedo ndipo izi zidzachititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe. (Chiv. 16:16) Pa nthawi imeneyi, anthu onse amene ali ngati mbuzi “adzachoka kupita ku chiwonongeko chotheratu.” Zoipa zonse zidzachotsedwa padzikoli ndipo khamu lalikulu lidzapulumuka mbali yomaliza ya chisautso chachikulu. Ndiyeno kenako ukwati wa Mwanawankhosa udzachitika. (Chiv. 21:1-4) * Anthu amene adzakhale padzikoli adzadalitsidwa kwambiri ndi Yehova ndipo adzaona umboni wosaneneka wa chikondi chake. Kunena zoona ukwati umenewu udzakhala wosangalatsa kwambiri. Tikulakalaka kwambiri nthawi imene ukwatiwu udzachitike.—Werengani 2 Petulo 3:13.

18. Popeza tadziwa zimene zidzachitike posachedwapa, kodi aliyense ayenera kuchita chiyani?

18 Popeza tadziwa zimene zidzachitike posachedwapa, kodi aliyense ayenera kuchita chiyani? Mtumwi Petulo analemba kuti: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. Muzichita zimenezi poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova, . . . Chotero okondedwa, pakuti mukuyembekezera zinthu zimenezi, chitani chilichonse chotheka kuti iye adzakupezeni opanda banga, opanda chilema ndiponso muli mu mtendere.” (2 Pet. 3:11, 12, 14) Choncho tiyeni tiyesetse kukhalabe anthu oyera n’kumamvera Mfumu ya Mtendere.

^ ndime 2 Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 25 mpaka 26.

^ ndime 15 Odzozedwa amene adzakhalapo pa nthawiyo sadzatengedwa kupita kumwamba ndi matupi awo. (1 Akor. 15:48, 49) Zimene zidzachitikire matupi awo n’zofanana ndi zimene zinachitikira thupi la Yesu.

^ ndime 17 Salimo 45 limasonyezanso mmene zinthuzi zidzachitikire. Limasonyeza kuti choyamba, Mfumu idzamenya nkhondo kenako ukwati udzachitika.