Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zotheka Kukhalabe Oyera

N’zotheka Kukhalabe Oyera

“Yeretsani manja anu . . . ndipo yeretsani mitima yanu.”—YAK. 4:8.

1. Kodi anthu m’dzikoli ali ndi makhalidwe otani?

MASIKU ano, ndi anthu ochepa kwambiri amene ali ndi khalidwe loyera. M’mayiko ambiri anthu saona kuti n’kulakwa kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndiponso kuchita chigololo. N’zomvetsa chisoni kuti mafilimu, mabuku, nyimbo ndiponso otsatsa malonda amalimbikitsa makhalidwe amenewa. (Sal. 12:8) Chiwerewere n’chofala kwambiri moti munthu angaganize kuti n’zosatheka kukhala woyera. Koma Yehova akhoza kutithandiza kukhala anthu oyera.—Werengani 1 Atesalonika 4:3-5.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuganizira zinthu zoipa? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

2 Kuti tikhale anthu oyera, tiyenera kupewa kuganizira zinthu zoipa. Popeza ndife anthu ochimwa, zinthu zachiwerewere zingatikope ngati mmene nyambo imakopera nsomba. Choncho tiyenera kusiya  msanga ngati tayamba kuganizira zinthu zoipa. Kupanda kutero, maganizo amenewa angatichimwitse mpata ukangopezeka. Paja Baibulo limati: “Chilakolako chikatenga pakati, chimabala tchimo.”—Werengani Yakobo 1:14, 15.

3 Munthu akhoza kuchita tchimo lalikulu chifukwa choganizira kwambiri zinthu zoipa. Choncho tiyenera kusamala ndi zinthu zimene tayamba kuganizira kuti tipewe chiwerewere ndiponso mavuto amene angatsatire. (Agal. 5:16) M’nkhaniyi tikambirana zinthu zitatu zimene zingatithandize kupewa kuganizira zoipa. Zinthu zake ndi ubwenzi wathu ndi Yehova, malangizo a m’Baibulo ndiponso Akhristu anzathu.

“YANDIKIRANI MULUNGU”

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyandikira Yehova?

4 Baibulo limalangiza anthu amene akufuna ‘kuyandikira Mulungu’ kuti: “Yeretsani manja anu” ndipo “yeretsani mitima yanu.” (Yak. 4:8) Tikamaona kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ndi wamtengo wapatali, timayesetsa kuchita ndiponso kuganizira zinthu zomusangalatsa nthawi zonse. Timayesetsa kuganizira zinthu zoyera kuti tikhalenso anthu oyera. (Sal. 24:3, 4; 51:6; Afil. 4:8) Yehova amamvetsa zoti ndife ochimwa komanso kuti zimativuta kupewa maganizo oipa. Koma sitifuna kumukhumudwitsa, choncho timayesetsa kupewa kuganizira zinthu zoipa. (Gen. 6:5, 6) Timachita zonse zimene tingathe kuti tiziganizira zinthu zabwino.

5, 6. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kupewa maganizo oipa?

5 Tingasonyeze kuti timadalira Yehova tikamamupempha kuti azitithandiza kupewa maganizo oipa. Tikamayandikira Mulungu popemphera iye amatiyandikiranso. Amatipatsa mzimu wake woyera kuti utithandize kukhalabe oyera n’kumapewa maganizo oipa. Choncho tizipempha Mulungu kuti azitithandiza kuganizira zinthu zomusangalatsa. (Sal. 19:14) Tiyenera kumupempha modzichepetsa kuti atithandize kuzindikira maganizo alionse amene angatichititse kuchimwa. (Sal. 139:23, 24) Tizimupempha nthawi zonse kuti azitithandiza kukhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero.—Mat. 6:13.

6 Mwina tisanaphunzire za Yehova tinkakonda kuchita zinthu zimene iye amadana nazo ndipo n’kutheka kuti zimabwerabe m’maganizo mwathu. Ngakhale zili choncho, Yehova angatithandize kukhalabe oyera. Davide ankadziwa bwino zimenezi. Iye atachita chigololo ndi Bati-seba, anapempha Yehova kuti: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10, 12) N’zoona kuti tingalakelake zinthu zoipa ndipo zingativute kusiya maganizo oipawo. Koma Yehova akhoza kutitsogolerabe kuti tizimvera malamulo ake. Iye akhoza kutithandiza kuti tisamalamuliridwe ndi maganizo oipa.—Sal. 119:133.

Maganizo oipa akayamba kumera mizu mumtima mwathu tiyenera kuwazula mwamsanga (Onani ndime 6)

‘MUZICHITA ZIMENE MAWU A MULUNGU AMANENA’

7. Kodi Mawu a Mulungu angatithandize bwanji kuti tipewe maganizo oipa?

7 Yehova amayankhanso mapemphero athu pogwiritsa ntchito Mawu ake m’Baibulo. Paja nzeru yochokera kwa Mulungu imene ili m’Mawu akewo “ndi yoyera.” (Yak.  3:17) Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse ndiponso kusinkhasinkha zimene tawerengazo kungatithandize kuti tiziganizira zinthu zabwino zokhazokha. (Sal. 19:7, 11; 119:9, 11) M’Baibulo mulinso zitsanzo ndi malangizo amene angatithandize kuti tisamalakelake zinthu zosayenera.

8, 9. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti mnyamata wina agonane ndi mkazi wachiwerewere? (b) Kodi mfundo ya mu chaputala 7 cha Miyambo tingaigwiritse ntchito bwanji?

8 Lemba la Miyambo 5:8 limati: “Njira yako ikhale kutali ndi [mkazi wachiwerewere]. Usayandikire pakhomo la nyumba yake.” Chaputala 7 cha buku la Miyambo chimasonyeza mavuto amene amakhalapo tikanyalanyaza malangizowa. M’chaputalachi muli nkhani ya mnyamata wina amene anapita kukawongola miyendo pafupi ndi nyumba ya mkazi wachiwerewere. Anachita zimenezi chakumadzulo. Ndiyeno atafika pafupi ndi mphambano, mkaziyo anamuchingamira atavala zovala zokopa amuna. Mkaziyo anagwira mnyamatayo n’kumupsompsona. Anamulankhulanso mawu okopa kwambiri moti mnyamatayo anakanika kusiyana naye mpaka anakagonana. N’kutheka kuti cholinga cha mnyamatayo sichinali kukachita chiwerewere. Vuto linali loti sankaganiza bwino. Iye akanapewa kuyenda  pafupi ndi mkaziyo, sakanakumana ndi mavuto amenewa.—Miy. 7:6-27.

9 Kodi nafenso nthawi zina sitiganiza bwino? N’kutheka kuti timachita zinthu kapena kupezeka pamalo amene angatigwetsere m’mavuto. Mwachitsanzo, zinthu zokhudza chiwerewere zimakonda kuonetsedwa pa TV usiku. Ndiyeno ngati tili ndi chizolowezi chosakasaka matchanelo usikuwo, tikhoza kuona zosayenera. Nanga timachita bwanji tikakhala pa Intaneti? Kodi timangotsatira malinki amene abwera kapena kupita pamalo ochezera alionse? Kupanda kusamala pa nkhaniyi, tikhoza kuonanso zolaula. Tikaona zinthu zosayenera ngati zimenezi tikhoza kuyamba kuzilakalaka mpaka kufika pochimwira Yehova.

10. Kodi kukopana n’koopsa bwanji? (Onani chithunzi patsamba 13.)

10 Baibulo limatiuzanso zimene tiyenera kuchita ngati tili ndi munthu yemwe si mwamuna kapena mkazi mnzathu. (Werengani 1 Timoteyo 5:2.) Limasonyeza kuti si bwino kukopana. Ena amaganiza kuti palibe vuto ngati ayamba kukopana ndi maso kapena m’njira zina. Amaona kuti bola ngati sakukhudzana. Koma zoona zake n’zakuti khalidwe limeneli ndi loipa basi. Limachititsa kuti anthu aziganiza zoipa mwinanso n’kufika pochita chiwerewere. Ena zawavutapo m’mbuyomu chifukwa cha khalidweli ndipo zikhoza kukuchitikiraninso inuyo.

11. Kodi Yosefe anatani pamene ankayesedwa?

11 Yosefe anapereka chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Iye anakana pamene ankanyengereredwa ndi mkazi wa Potifara. Koma mkaziyo sanasiyire pomwepo. Tsiku lililonse ankamuuza kuti asachoke msanga. (Gen. 39:7, 8, 10) Katswiri wina wa mawu a m’Baibulo ananena kuti mkazi wa Potifara ankaganiza kuti Yosefe akhoza kuyamba kukopeka naye akacheza pa awiri. Koma Yosefe sanalole zimenezo. Iye sanafune m’pang’ono pomwe kuti ayambe zinthu zimene zingamuchititse kuganizira zoipa mumtima mwake. Tsiku lina mkaziyo atafuna kumugwirira, Yosefe ‘anangovula malaya ake n’kuwasiya m’manja mwake n’kuthawira panja.’—Gen. 39:12.

12. Kodi tikudziwa bwanji kuti zimene taona zingachititse kuti tiyambe kulakalaka zoipa?

12 Baibulo limasonyeza kuti zimene taona zikhoza kutichititsa kuyamba kulakalaka zoipa mumtima mwathu. Paja Yesu ananena kuti: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.” (Mat. 5:28) Nkhani ya Davide imasonyeza mavuto amene amakhalapo ngati tayang’anitsitsa zosayenera. Iye ali padenga la nyumba “anaona mkazi akusamba.” (2 Sam. 11:2) Ndiyeno ankangomuyang’anitsitsa osasiya. Izi zinachititsa kuti ayambe kulakalaka mkazi wamwiniyo ndipo kenako anagona naye.

13. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kuchita pangano ndi maso’ athu? (b) Kodi mfundo imeneyi tingaitsatire bwanji?

13 Kuti tisayambe kulakalaka zoipa, tiyenera kutsanzira Yobu. Paja iye ‘anachita pangano ndi maso ake.’ (Yobu 31:1, 7, 9) Tiyenera kutsimikiza mumtima mwathu kuti tisamayang’anitsitse anthu mpaka kufika powalakalaka. Mfundo imeneyi tiyenera kuitsatiranso ngati taona zithunzi zoipa pa TV, pa Intaneti, m’mabuku, kapena m’zikwangwani.

14. Kodi tingatani kuti tikhalebe oyera?

14 Mwina mukaganizira mfundo zimene takambiranazi, mukuona kuti pali zina zimene  muyenera kusintha. Ngati ndi choncho, chonde musinthiretu panopa. Yesetsani kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu amene angakuthandizeni kukhalabe oyera.—Werengani Yakobo 1:21-25.

‘MUITANE AKULU’

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani ngati zikutivuta kusiya kuganizira zinthu zoipa?

15 Mwina mukuyesetsa kuti musamaganizire zinthu zachiwerewere koma zikukuvutani. Ngati ndi choncho, musataye mtima chifukwa Akhristu anzanu angakuthandizeni. Kunena zoona, si zophweka kuuza ena zinthu ngati zimenezi. Koma mukamayesetsa kuuzako Akhristu anzanu, zidzakuthandizani kusiya kuganizira zinthu zoipa. (Miy. 18:1; Aheb. 3:12, 13) Kukambirana zimenezi ndi Akhristu omwe amadziwa zinthu zambiri kungakuthandizeni kuzindikira mavuto anu. Mukatero mudzatha kukonza mavutowo ndipo ubwenzi wanu ndi Yehova udzalimba.

16, 17. (a) Kodi akulu angathandize bwanji anthu amene akuvutika kusiya kuganizira zinthu zoipa? Perekani chitsanzo. (b) N’chifukwa chiyani anthu omwe ali ndi vuto loonera zolaula ayenera kupempha thandizo mwamsanga?

16 Akulu ndi amene angatithandize kwambiri kuti tisiye kuganizira zinthu zoipa. (Werengani Yakobo 5:13-15.) Mwachitsanzo, mnyamata wina ku Brazil ankalakalaka zinthu zoipa kwa zaka zambiri. Iye anati: “Ndinkadziwa kuti zimene ndinkaganizira zinkakhumudwitsa Yehova koma ndinkachita manyazi kuuza ena mavuto angawo.” Ndiyeno mkulu wina mumpingo wawo anazindikira kuti mnyamatayo ali ndi vuto ndipo anamulimbikitsa kuti auze akulu. Mnyamatayo anati: “Akulu anandithandiza mokoma mtima ndipo sindinayembekezere kuti adzandimvetsa choncho. Anamvetsera mwatcheru pamene ndinkawafotokozera mavuto anga. Anagwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo ponditsimikizira kuti Yehova amandikonda ndipo anapemphera nane. Zonsezi zinandithandiza kuti nditsatire mosavuta malangizo a m’Baibulo amene anandipatsa.” Mnyamatayo anakonza ubwenzi wake ndi Yehova ndipo patapita zaka zingapo anati: “Ndazindikira kufunika kopempha anthu ena kuti atithandize m’malo molimbana ndi mavuto patokha.”

17 Tiyenera kupempha ena kuti atithandize ngati tili ndi vuto loonera zolaula. Tikazengereza kupempha thandizo, maganizo oipa angakule ndipo tsiku lina tikhoza kuchita chiwerewere. Zimenezi zidzakhumudwitsa anthu ena ndiponso kunyozetsa Yehova. Mtima wofuna kusangalatsa Mulungu ndiponso kukhalabe mumpingo walimbikitsa Akhristu ambiri kupempha thandizo n’kutsatira malangizo.—Yak. 1:15; Sal. 141:5; Aheb. 12:5, 6.

MUZIYESETSA KUKHALABE OYERA

18. Kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

18 Makhalidwe a m’dziko la Satanali akuipiraipira. Choncho Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akaona atumiki ake akuyesetsa kukhala oyera n’kumapewa maganizo oipa. Tiyeni tonsefe tiziyesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso kutsatira malangizo amene amapereka m’Mawu ake komanso mumpingo. Tikakhala anthu oyera timakhala ndi mtendere mumtima ndipo timasangalala. (Sal. 119:5, 6) M’tsogolomu, Satana adzawonongedwa ndipo tidzakhala kwamuyaya m’dziko lopanda zinthu zoipa.