Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  April 2015

 MBIRI YA MOYO WANGA

Ndadalitsidwa “M’nthawi Yabwino ndi M’nthawi Yovuta”

Ndadalitsidwa “M’nthawi Yabwino ndi M’nthawi Yovuta”

NDINABADWA mu March 1930 m’mudzi mwa a Namkumba pafupi ndi mzinda wa Lilongwe ku Malawi. Ndinkakhala ndi achibale komanso anzanga amene ankatumikira Yehova mokhulupirika. Mu 1942, ndinadzipereka kwa Yehova ndipo ndinabatizidwa mumtsinje winawake. Kwa zaka 70, ndakhala ndikutsatira zimene Paulo anauza Timoteyo zakuti: “Lalikira mawu. Lalikira modzipereka, m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.”—2 Tim. 4:2.

Mu 1948, M’bale Nathan H. Knorr ndi Milton G. Henschel anabwera ku Malawi ndipo izi zinandilimbikitsa kuti ndiyambe utumiki wa nthawi zonse. Ndimakumbukira mfundo zolimbikitsa zimene abale ochokera kulikulu lathuwa ananena. Anthu okwana 6,000 anaimirira pamalo ena amatope n’kumamvetsera nkhani imene M’bale Knorr anakamba. Nkhaniyo inali yonena za Mfumu imene idzalamulire anthu onse.

Pa nthawi ina ndinakumana ndi mlongo wokongola kwambiri dzina lake Lidasi. Iye anabadwiranso m’banja la Mboni ndipo ndinasangalala kumva kuti nayenso amafuna utumiki wa nthawi zonse. Tinakwatirana mu 1950 ndipo pofika mu 1953, tinali ndi ana awiri. Ngakhale kuti kulera anawa inali ntchito yaikulu, tinaganiza zoti ndiyambe upainiya wokhazikika. Patangopita zaka ziwiri ndinapemphedwa kukatumikira monga mpainiya wapadera.

Kenako ndinapemphedwa kuti ndikhale woyang’anira dera. Lidasi ankandithandiza kwambiri moti ndinkakwanitsa kusamalira banja langa bwinobwino uku ndikutumikira. * Koma tinkafunitsitsa kuti tonse tizichita utumiki wa nthawi zonse. Tinasintha bwinobwino zinthu pamoyo wathu ndipo titagwirizana zochita ndi ana athu, Lidasi anayambanso utumiki wa nthawi zonse mu 1960.

Misonkhano inatilimbikitsa pokonzekera mavuto

Imeneyi inali nthawi yabwino ndipo tinkasangalala kwambiri kutumikira abale ndi alongo m’mipingo yosiyanasiyana. Tinkayendera mipingo yambiri kuchokera kuphiri la Mulanje kufika kunyanja ya Malawi. Ofalitsa ndiponso mipingo inkawonjezeka kwambiri m’dera lathu.

Mu 1962, tinasangalala kwambiri kupezeka pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Atumiki Olimba Mtima.” Msonkhanowu unachitika pa nthawi yake chifukwa pasanapite nthawi yaitali mavuto anayamba. Mu 1963, M’bale Henschel anafikanso ndipo anachititsa msonkhano pafupi ndi mzinda wa Blantyre. Pa msonkhanowu panali  anthu okwana 10,000 ndipo unatilimbikitsanso pokonzekera mavuto.

NTHAWI YOVUTA INAFIKA

Boma linaletsa ntchito yathu ndiponso linalanda ofesi ya nthambi

Mu 1964, a Mboni za Yehova anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa chosalowerera ndale. Zimenezi zinachititsa kuti Nyumba za Ufumu zoposa 100 ndiponso nyumba za abale zoposa 1,000 ziwonongedwe. Koma ife tinapitirizabe ntchito yoyendera dera mpaka mu 1967 pamene boma la Malawi linaletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Ofesi ya nthambi ku Blantyre inalandidwa ndipo amishonale anathamangitsidwa. Ine ndi Lidasi pamodzi ndi abale ambiri tinamangidwa. Titamasulidwa tinapitirizabe kugwira ntchito yoyendera dera mobisa.

Tsiku lina mu October 1972, kagulu ka mayufi pafupifupi 100, anabwera kunyumba kwathu. Koma mmodzi wa mayufiwo anathamanga kudzandiuza kuti ndibisale chifukwa gululo linkabwera kuti lidzandiphe. Nthawi yomweyo ndinauza mkazi wanga ndi ana kuti akabisale m’nthochi zimene zinali chapafupi. Ine ndinathamanga n’kukakwera mumtengo wa mango ndipo ndili mumtengomo ndinaona nyumba yathu ikuwotchedwa.

Nyumba za abale zinkawotchedwa

A Mboni za Yehova ambiri anathawa m’dzikoli. Ine pamodzi ndi mkazi komanso ana anga tinakhala kumsasa wa kumadzulo kwa dziko la Mozambique mpaka mu June 1974. Pa nthawiyi ine ndi Lidasi tinapemphedwa kuti tizichita upainiya wapadera ku Dómue chakumalire ndi dziko la Malawi. Tinachita utumikiwu mpaka mu 1975, pamene dziko la Mozambique linalandira ufulu wodzilamulira. Ndiyeno a Mboni za Yehova onse anakakamizidwa kubwerera ku Malawi.

Nditafika ku Malawi, ndinapatsidwa ntchito yoyang’anira mipingo ya mumzinda wa Lilongwe. Ngakhale kuti tinkazunzidwa ndiponso kukumana ndi mavuto ambiri, chiwerengero cha ofalitsa chinkawonjezeka.

YEHOVA ANATITHANDIZA

Tsiku lina titafika m’mudzi wina tinapeza anthu akuchita msonkhano wachipani. Anthu ena atazindikira kuti ndife a Mboni anatitenga n’kutikhazika pamene panali a Young Pioneer. Apa tinadziwiratu kuti zavuta ndipo tinapempha Yehova kuti atithandize komanso kutitsogolera. Msonkhanowo utatha anayamba kutimenya. Kenako mayi wina wachikulire anabwera mwamsanga uku akufuula kuti: “Inu tawasiyeni amenewo! Tawasiyeni azipita! Simukudziwa kuti uyu ndi mwana wa mchimwene wanga?” Ndiyeno munthu amene ankachititsa msonkhanowo analamula kuti: “Asiyeni azipita!” Tinadabwa ndi zimene mayiyo anachita chifukwa sanali wachibale wathu. Tikuganiza kuti inali njira imene Yehova anayankhira pemphero lathu.

Khadi la chipani

 Mu 1981, tinakumananso ndi a Young Pioneer. Anatilanda njinga zathu, zikwama, makatoni a mabuku komanso mafaelo a dera. Tinathawira kwa mkulu wina m’deralo ndipo tinapempha Yehova kuti atithandize. Tinkaopa kuti zinthu zivuta kwambiri akaona zimene zinali m’mafaelowo. Koma ataona mafaelowo anapeza kuti muli makalata anga ochokera m’madera osiyanasiyana a m’Malawi. Iwo anachita mantha kwambiri poganiza kuti ndine munthu waudindo m’boma. Nthawi yomweyo anabwera kudzabweza zinthu zonse moti palibe chimene chinasowa.

Tsiku lina tinapulumukanso pamene tinkawoloka mtsinje pa boti. Mwini wa botilo anali tcheyamani wa chipani ndipo anayamba kufunsa aliyense kuti aonetse khadi lake. Atatsala pang’ono kutipeza anazindikira zoti m’botilo munali wakuba wina amene a boma ankamufufuza. Apa tsopano nkhani yofufuza makadi ija inatha n’kuyamba kulimbana ndi wakubayo. Tinaonanso kuti Yehova watithandiza kwambiri.

NDINAMANGIDWA

Tsiku lina mu February 1984, ndinanyamuka kupita ku Lilongwe kukapereka malipoti oti apite kunthambi ya ku Zambia. Ndiyeno ndinakumana ndi wapolisi amene anayamba kufufuza zimene ndinatenga m’chikwama. Atapeza mabuku athu anandigwira n’kupita nane kupolisi. Titafika anayamba kundimenya kenako anandimanga n’kundiika m’chipinda chimene munali akuba.

Tsiku lotsatira mkulu wa apolisi ananditengera m’chipinda china. Titafika m’chipindacho analemba papepala kuti: “Ine Trophim R.Nsomba ndikufuna kuti ndimasulidwe choncho ndasiya kukhala wa Mboni za Yehova.” Ndiyeno anandiuza kuti ndisainire. Ndinakana kusaina ndipo ndinamuuza kuti: “Sindingasiye kukhala wa Mboni ndipo ndine wokonzeka kumangidwa ngakhalenso kuphedwa.” Nditatero anakwiya kwambiri n’kumenya tebulo moti wapolisi wina anadzidzimuka n’kubwera kuti aone chimene chikuchitika. Mkulu wa apolisiwo anati: “Eti uyu akukana kusaina chikalata chonena kuti wasiya kukhala wa Mboni. Tiyeni timusainitse chikalata chonena kuti ndi wa Mboni za Yehova ndipo timutumize kupolisi ya ku Lilongwe.” Nthawi yonseyi mkazi wanga sankadziwa zimene zikuchitika. Patapita masiku 4, abale ena anamuuza zoti ndili kupolisi.

Kupolisiko sankandizunza ayi. Mkulu wa apolisi anabwera n’kunena kuti: “Eni mpunga uwu mudye. Inu akumangani chifukwa cha Mawu a Mulungu pomwe enawa amangidwa chifukwa choti ndi mbava.” Kenako ndinatumizidwa kundende ya Kachere ndipo ndinakhalako miyezi 5.

Msilikali wina anasangalala kwambiri atandiona ndipo ankafuna kuti ndikhale “m’busa” wa  kundendeko. Anachotsa paudindo m’busa amene analiko n’kumuuza kuti: “Sindikufuna kuti uzilalikiranso muno. Iwe si unamangidwa chifukwa choti unaba kutchalitchi kwanu?” Choncho anandiuza kuti ndiziphunzitsa Baibulo mlungu uliwonse pa msonkhano wa akaidi.

Koma kenako zinthu zinavuta. Asilikali a kundendeko anandipanikiza kuti nditchule chiwerengero cha Mboni m’Malawi. Nditakana kutchula anandimenya koopsa mpaka ndinakomoka. Tsiku lina anandipanikizanso kuti nditchule kumene kuli likulu lathu. Poyankha ndinawauza kuti: “Aa funso limeneli ndi losavuta. Ndikuuzani.” Nditatero apolisiwo anasangalala n’kutchera zojambulira mawu. Ndiye ndinawauza kuti likulu la Mboni za Yehova latchulidwa m’Baibulo. Nditatero anadabwa n’kufunsa kuti: “Alemba pati m’Baibulomo?”

Ndinayankha kuti: “Pa Yesaya 43:12.” Iwo anatsegula Baibulo n’kuyamba kuwerenga kuti: “Choncho inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.” Anawerenga vesili katatu kenako n’kundifunsa kuti: “Iwe! Ukunena bwanji kuti likulu la Mboni za Yehova lili m’Baibulo osati ku America?” Ndinawayankha kuti: “A Mboni za Yehova amene ali ku America amanenanso kuti likulu lawo lili pa lemba lomweli.” Ataona kuti sindikuwayankha bwino ananditumiza kundende ya ku Dzaleka.

MULUNGU ANATIDALITSA PA NTHAWI YOVUTA

Mu July 1984, ndinatumizidwa kundende ya Dzaleka kumene kunalinso a Mboni ena 81. Kundendeko akaidi 300 ankagona pansi m’chipinda chimodzi mopanikizana. Kenako a Mbonife tinkagawana m’timagulu kuti tizikambirana malemba tsiku lililonse. Tinkachita kuuzana lemba lomwe tidzakambirane tsiku lotsatira. Zimenezi zinkatilimbikitsa.

Patapita nthawi msilikali wa kundendeko anatisiyanitsa ndi akaidi ena. Tsiku lina msilikali wotilondera anatiuza kuti: “Bomatu silidana nanu koma likukusungani m’ndende muno kuopera kuti mungaphedwe ndi a Young Pioneer. Paja inunso mumalalikira za nkhondo imene ikubwera ndiye boma likuopa kuti asilikali ake angadzaphedwe.”

Abale akuchokera kukhoti

Mu October 1984, tonse amene tinali kundendeko tinaitanidwa kukhoti ndipo tinaweruzidwa kuti tikhale m’ndende zaka ziwiri. Pa nthawiyi tinaikidwanso m’ndende ndi anthu oti si a Mboni. Koma msilikali wa kundendeko analengeza kuti: “A Mboni za Yehova sasuta fodya. Chonde amene mukuwalondera musawavutitse kuti akupatseni fodya kapena kuwatuma kuti akapale moto woti muyatsire fodya. Amenewatu ndi anthu Mulungu. Muziwapatsa chakudya kawiri patsiku. Iwo sanamangidwe chifukwa cha kuba, koma chifukwa cha zimene amakhulupirira m’Baibulo.”

 Chifukwa cha makhalidwe athu abwino zinthu zinkatiyendera ndithu kundendeko. Nthawi zina usiku kapena kukamagwa mvula, akaidi sankaloledwa kutuluka. Koma ife tinkaloledwa kutuluka chifukwa amadziwa kuti sitingathawe. Tinkayesetsa kuchita zinthu zabwino. Nthawi ina tikulima kumunda, msilikali wotilondera anadwala ndipo tinamunyamula kupita naye kuchipatala chakundendeko. Tinadalitsidwa kwambiri chifukwa chosonyeza makhalidwe abwino ndipo zimenezi zinachititsa kuti Yehova atamandike.—1 Pet. 2:12. *

NTHAWI YABWINO INAFIKANSO

Pa May 11, 1985, ndinatulutsidwa m’ndende ya Dzaleka. Ndinasangalala kwambiri kukumananso ndi banja langa. Timathokoza Yehova chifukwa chotithandiza kukhalabe okhulupirika pa nthawi yovutayo. Tikaganizira zimenezi, timamva ngati mmene mtumwi Paulo ankamvera pamene anati: “Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo . . . moti tinalibenso chiyembekezo choti tikhala ndi moyo. Ngakhalenso m’mitima mwathu, tinali kumva ngati talandira chiweruzo cha imfa. Zinatero kuti tisakhale ndi chikhulupiriro mwa ife tokha, koma mwa Mulungu amene amaukitsa akufa. Iye anatipulumutsadi ku chinthu choopsa, ndicho imfa, ndipo adzatipulumutsabe.”—2 Akor. 1:8-10.

M’bale Nsomba ndi mkazi wake ali pa Nyumba ya Ufumu mu 2004

Kunena zoona, nthawi zina tinkaganiza kuti tifa basi. Koma tinkapempha Yehova kuti atithandize kukhala olimba mtima, anzeru ndiponso odzichepetsa kuti tipitirize kulemekeza dzina lake.

Yehova watithandiza kuti timutumikire m’nthawi zovuta ndiponso zabwino. Tsopano tikusangalala kwambiri kuona ofesi ya nthambi imene inamangidwa ku Lilongwe ndipo inatha m’chaka cha 2000. Tikusangalalanso kuona Nyumba za Ufumu zatsopano zoposa 1000. Yehova watidalitsa kwambiri ndipo ine ndi mkazi wanga Lidasi timangomva ngati tikulota. *

^ ndime 7 Masiku ano, abale amene ali ndi ana aang’ono saloledwa kukhala oyang’anira madera.

^ ndime 30 Kuti mudziwe zokhudza mavuto amene a Mboni za Yehova anakumana nawo ku Malawi, onani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1999, masamba 171 mpaka 223.

^ ndime 34 M’bale Nsomba anamwalira nkhaniyi ikulembedwa ndipo anamwalira ali ndi zaka 83.