Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  April 2015

Zimene Mungachite Pophunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu

Zimene Mungachite Pophunzitsa Ena Kuti Akhale Akulu

“Zinthu zimene unazimva kwa ine . . . , uziphunzitse kwa anthu okhulupirika.”—2 TIM. 2:2.

1. (a) Perekani zitsanzo zakale zosonyeza kuti kuphunzitsa ena n’kofunika? (b) N’chifukwa chiyani nafenso masiku ano tiyenera kuphunzitsidwa? (c) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

ATUMIKI a Mulungu amadziwa kuti kuphunzitsa ena n’kothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, Abulamu anakwanitsa kupulumutsa m’bale wake Loti chifukwa choti anali ndi “anyamata ake odziwa kumenya nkhondo” kapena kuti ophunzitsidwa bwino. (Gen. 14:14-16) M’nthawi ya Mfumu Davide, anthu omwe ankaimba m’nyumba ya Mulungu anali “ophunzitsidwa kuimbira Yehova” ndipo izi zinkalemekeza Yehova. (1 Mbiri 25:7) Masiku ano tikumenya nkhondo yolimbana ndi Satana ndi otsatira ake. (Aef. 6:11-13) Komanso tikuyesetsa kuchita zimene tingathe kuti tizitamanda Yehova. (Aheb. 13:15, 16) Choncho nafenso tiyenera kuphunzitsidwa kuti zinthu zizitiyendera bwino. Kuti zimenezi zitheke, Yehova waika akulu m’mipingo kuti aziphunzitsa ena. (2 Tim. 2:2) Mu nkhaniyi tikambirana zimene akulu angachite pophunzitsa ena kuti akhale akulu.

 ATHANDIZENI KUTI AZIKONDA KWAMBIRI YEHOVA

2. (a) Kodi mkulu ayenera kuchita chiyani asanayambe kuphunzitsa munthu wina zinthu zatsopano? (b) Kodi zimenezi n’zothandiza bwanji?

2 Akulu ali ngati mlimi. Nthawi zina, mlimi amayamba wathira manyowa m’munda asanabzalemo mbewu. N’chimodzimodzi ndi kuphunzitsa anthu ena zinthu zatsopano. Choyamba, muyenera kuwathandiza kudya chakudya chabwino chochokera m’Mawu a Mulungu. Izi zimathandiza kuti aphunzire bwino zinthu zatsopanozo.—1 Tim. 4:6.

3. (a) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mawu a Yesu a pa Maliko 12:29, 30? (b) Kodi pemphero lingathandize bwanji munthu amene mukumuphunzitsa?

3 Kodi mungadziwe bwanji ngati mfundo za m’Malemba zikuthandiza munthuyo? Mwina mungamufunse kuti: “Kodi inuyo mutadzipereka kwa Yehova munasintha zinthu ziti?” Funso limeneli likhoza kuthandiza kuti mukambirane mfundo zambiri zolimbikitsa kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse. (Werengani Maliko 12:29, 30.) Pambuyo pokambirana mfundo ngati zimenezi mukhoza kupemphera naye. Ndiyeno m’pempherolo mungapemphe Yehova kuti amupatse mzimu woyera kuti umuthandize kuphunzira zinthu zatsopano. M’baleyo akhoza kusangalala kumva pemphero losonyeza kuti mumamuganizira kwambiri.

4. (a) Kodi mungagwiritse ntchito malemba ati pothandiza munthu kuti azikonda kwambiri Yehova? (b) Kodi akulu amafunitsitsa kuti munthu amene akumuphunzitsa atani?

4 Poyamba kuphunzitsa munthu, muyenera kukambirana naye nkhani zina za m’Baibulo zimene zingamuthandize kukhala ndi mtima wofuna kutumikira, kukhala wodalirika komanso wodzichepetsa. (1 Maf. 19:19-21; Neh. 7:2; 13:13; Mac. 18:24-26) Makhalidwe amene tatchulawa ali ngati manyowa othandiza munthu wophunzirayo. Tikutero chifukwa chakuti amathandiza kuti ayambe mwamsanga kukonda kwambiri Yehova. Mkulu wina wa ku France, dzina lake Jean-Claude, anati: “Chimene ndimafunitsitsa n’kuthandiza wophunzirayo kuti azikonda kwambiri Yehova. Ndimayesetsa kupeza mpata wokambirana naye malemba amene angamutsegule m’maso kuti aone ‘zinthu zodabwitsa’ za m’Mawu a Mulungu.” (Sal. 119:18) Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite pothandiza munthuyo pa mbali imeneyi?

ATHANDIZENI KUKHALA NDI ZOLINGA

5. (a) Kodi kukambirana ndi munthu zolinga zake n’kothandiza bwanji? (b) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuthandiza achinyamata kukhala ndi zolinga adakali aang’ono? (Onani mawu am’munsi.)

5 Choyamba, tiyenera kufunsa munthu amene tikufuna kumuphunzitsayo zolinga zake. Ngati alibe zolinga zilizonse, muyenera kumuthandiza kukhala ndi zolinga zimene angazikwanitsedi. Mwina mungamufotokozere zolinga zomwe munali nazo ndiponso mmene munamvera mutazikwaniritsa. Zimenezi zingaoneke zazing’ono koma zimathandiza. Chitsanzo ndi m’bale wina wa ku Africa dzina lake Victor. Iye ndi mkulu komanso mpainiya ndipo anati: “Ndili wamng’ono mkulu wina anandifunsa mafunso ochepa okhudza zolinga zanga. Mafunsowo anandithandiza kuyamba kuganizira kwambiri za utumiki wanga.” Akulu enanso omwe amakonda kuphunzitsa ena anafotokoza kuti m’pofunika kuyamba kuphunzitsa achinyamata adakali aang’ono. Ndi bwino kuwapatsa ntchito zina mumpingo zogwirizana ndi msinkhu wawo. Kuphunzitsa achinyamatawa kungawathandize kukhala ndi  zolinga isanafike nthawi yomwe angasokonezedwe ndi zinthu zina.—Werengani Salimo 71:5, 17. *

Mukamapempha munthu kuchita zinazake, muzimuuza zifukwa zake ndipo muzimuyamikira ngati wachita bwino (Onani ndime 5 mpaka 8)

6. Kodi Yesu ankaphunzitsa bwanji anthu ena?

6 Pophunzitsa anthu, Yesu ankafotokoza zoyenera kuchita ndiponso zifukwa zake. Mwachitsanzo, asanauze ophunzira ake ntchito yoti agwire, Yesu anawauza chifukwa chake ayenera kumvera. Iye anati: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Kenako ananena kuti: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:18, 19) Pophunzitsa munthu, nanunso muyenera kumufotokozera zimene ayenera kuchita ndiponso zifukwa zake.

7, 8. (a) Kodi akulu masiku ano angatsanzire bwanji Yesu pophunzitsa ena? (b) N’chifukwa chiyani kuyamikira ena n’kothandiza? (c) Kodi akulu angaphunzitse bwanji anthu ena? (Onani bokosi lakuti “Kodi Tingawaphunzitse Bwanji?”)

7 Mukamauza munthu zoyenera kuchita, muzimufotokozera zifukwa zake zochokera m’Malemba. Mukamachita zimenezi mudzamuthandiza kutsatira mfundo za m’Baibulo. Tiyerekeze kuti mukupempha m’bale kuti ayeretse kanjira kopita ku Nyumba ya Ufumu. Mwina mungakambirane naye lemba la Tito 2:10 ndipo mungafotokoze kuti ntchitoyo idzakometsera “chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.” Mungamufotokozerenso mmene ntchitoyo ingathandizire anthu achikulire mumpingo. Mukamakambirana mwa njira imeneyi, zidzathandiza munthuyo kugwira ntchitoyo ndi mtima wofuna kuthandiza anthu osati mongotsatira malamulo. Iye adzasangalala kwambiri poona kuti ntchito yake yathandiza abale ndi alongo.

8 Muziyamikira munthu amene mukumuthandizayo ngati wayesetsa kutsatira zimene mukumuphunzitsa. Kodi zimenezi n’zothandiza bwanji? Kuyamikira munthu kuchokera pansi pa mtima kuli ngati kuthirira mbewu kuti zikule bwino.—Yerekezerani ndi Mateyu 3:17.

VUTO LINA

9. (a) Kodi akulu amene amatumikira m’mayiko otukuka amakumana ndi vuto liti? (b) N’chifukwa chiyani achinyamata m’mayiko amenewa saika Yehova pa malo oyamba?

9 Akulu amene akutumikira m’mayiko  otukuka amakumana ndi vuto lina. Zimakhala zovuta kwambiri kulimbikitsa achinyamata a zaka za m’ma 20 kapena 30 kuti azichita zambiri mumpingo. Titafunsa akulu amene atumikira nthawi yaitali m’mayiko 20 oterewa, anatiuza chimene chimachititsa vutoli. Chifukwa chimodzi ndi chakuti achinyamatawo amalimbikitsidwa kuphunzira kwambiri kapena kupeza ntchito zapamwamba osati kutumikira Yehova. Achinyamata oterewa saika Yehova pa malo oyamba.—Mat. 10:24.

10, 11. (a) Kodi mkulu angathandize bwanji m’bale amene akuoneka kuti safuna kuchita zambiri mumpingo? (b) Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene angagwiritse ntchito pokambirana naye? (Onani mawu am’munsi.)

10 Pamafunika khama komanso kuleza mtima kuti tithandize wachinyamata amene safuna kuchita zambiri mumpingo. Alimi ena amapeza njira yowongolera mbewu zopindika kuti zikule bwino. Amachita zimenezi mwapang’onopang’ono. N’chimodzimodzi ndi kuthandiza achinyamata kuti asinthe maganizo n’kukhala ndi mtima wofuna kutumikira. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?

11 Choyamba muyenera kupeza mpata wocheza nawo. Athandizeni kudziwa kuti ndi anthu ofunika kwambiri mumpingo. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono muzikambirana nawo malemba amene angawathandize kuganizira zimene analonjeza podzipereka kwa Yehova. (Mlal. 5:4; Yes. 6:8; Mat. 6:24, 33; Luka 9:57-62; 1 Akor. 15:58; 2 Akor. 5:15; 13:5) Mwina mungamufunse kuti, ‘Kodi pamene unkadzipereka kwa Yehova unamulonjeza kuti chiyani?’ Kenako mungamufunse kuti, ‘Ukuganiza kuti Yehova anamva bwanji tsiku limene unabatizidwa?’ (Miy. 27:11) ‘Nanga ukuganiza kuti Satana anamva bwanji?’ (1 Pet. 5:8) Dziwani kuti mukawerenga naye malemba oyenerera akhoza kusintha kwambiri.—Werengani Aheberi 4:12. *

MUZIYESETSA KUKHALA OKHULUPIRIKA

12, 13. (a) Kodi Elisa anasonyeza khalidwe lotani pamene ankaphunzitsidwa? (b) Kodi Elisa anadalitsidwa bwanji chifukwa chokhala wokhulupirika?

12 Kodi achinyamata muyenera kuchita chiyani kuti zinthu zikuyendereni bwino? Kuti tiyankhe funsoli tiyeni tikambirane za munthu wina wakale.

13 Zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, mneneri Eliya anapempha Elisa kuti akhale mtumiki wake. Nthawi yomweyo iye anavomera ndipo anali wokhulupirika. Ankatumikira Eliya ngakhale pa ntchito zooneka zonyozeka. (2 Maf. 3:11) Ndiyeno patapita zaka 6, Elisa anazindikira kuti kwatsala nthawi yochepa kuti Eliya asiye kutumikira ku Isiraeli. Pa nthawiyi Eliya anali ataphunzitsa Elisa zinthu zambiri ndipo anamuuza katatu kuti asiye kumutsatira. Pa nthawi zonsezi Elisa ankayankha kuti: “Sindikusiyani.” Iye sanafune kusiyana ndi Eliya ngakhale pang’ono. Yehova anadalitsa Elisa chifukwa cha kukhulupirika kwake. Iye anali ndi mwayi woona zinthu zochititsa mantha pa nthawi imene Eliya ankachoka.—2 Maf. 2:1-12.

14. (a) Kodi achinyamata angatsanzire bwanji Elisa? (b) N’chifukwa chiyani achinyamata ayenera kukhala okhulupirika?

14 Kodi achinyamatanu mungatsanzire bwanji Elisa? Mukapatsidwa ntchito zooneka ngati zonyozeka muzizigwira mokhulupirika. Muziona kuti akulu amene akupatsani ntchitoyo ndi anzanu ndipo asonyezeni kuti mumayamikira kwambiri zimene akuchita pokuthandizani. Mukamatero mudzakhala  ngati mukuuza akuluwo kuti: “Sindikusiyani.” N’chifukwa chiyani muyenera kukhala okhulupirika? Mukakhala okhulupirika akulu adzaona kuti Yehova akufuna kuti mupatsidwe maudindo ena mumpingo.—Sal. 101:6; Werengani 2 Timoteyo 2:2.

MUZITSATIRA ZIMENE MWAPHUNZITSIDWA

15, 16. (a) Kodi Elisa anasonyeza bwanji kuti ankatsatira zimene anaphunzitsidwa? (Onani chithunzi patsamba 9.) (b) N’chiyani chinatsimikizira aneneri a ku Yeriko kuti mzimu wa Eliya uli pa Elisa?

15 Nkhani ya Elisa ikusonyezanso zimene abale angachite posonyeza kuti amalemekeza akulu amene atumikira nthawi yaitali. Tsiku lina, Eliya ndi Elisa anakumana ndi ana a aneneri ku Yeriko ndipo kenako anapita kumtsinje wa Yorodano. Atafika, “Eliya anatenga chovala chake chauneneri n’kuchipinda. Atatero anamenya nacho madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika.” Iwo anawoloka pouma ndipo ankayenda, uku akulankhulana. Pa nthawiyi Elisa sankadzitenga kuti akudziwa zonse. Elisa ankasunga mumtima mawu onse amene Eliya ankamuuza. Ankachita zimenezi mpaka nthawi imene Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho. Ndiyeno pobwerera Elisa anafikanso pamtsinje paja. Iye anatenga chovala cha Eliya chija n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Atatero madziwo anagawanikanso.—2 Maf. 2:1-14.

16 Taonani kuti chozizwitsa choyamba chimene Elisa anachita chinali chofanana ndendende ndi chimene Eliya anachita. Kodi tikuphunzirapo chiyani? N’kutheka kuti Elisa sankaganiza kuti ali ndi mphamvu zonse moti akhoza kuchita zosiyana ndi zimene Eliya ankachita. Iye ankatsatira zimene Eliya ankachita potumikira Yehova ndipo izi zinachititsa aneneri a ku Yeriko kutsimikizira kuti mzimu wa Eliya uli pa Elisa. (2 Maf. 2:15) Elisa anagwira ntchito yauneneri kwa zaka 60 ndipo Yehova anamuthandiza kuchita zozizwitsa zambiri kuposa zimene Eliya anachita. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

17. (a) Kodi anthu amene akuphunzitsidwa angatsanzire bwanji Elisa? (b) Kodi Yehova angathandize bwanji anthu okhulupirika amene aphunzitsidwa bwino?

17 Mukapatsidwa udindo mumpingo, musamakhale ndi mtima wofuna kusinthiratu zinthu. Kumbukirani kuti zinthu zimasinthadi mumpingo malinga ndi mmene zinthu zilili kapena malinga ndi malangizo amene gulu lapereka, osati chifukwa cha mtima wanu wofuna kusintha zinthu. Paja aneneri ena aja anatsimikizira zoti Elisa ndi mneneri chifukwa choti ankatsatira zimene Eliya ankachita. Anthu mumpingo adzatsimikiziranso kuti muchita bwino udindo wanu ngati mutsatira njira zimene akulu ena ankatsatira mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba. (Werengani 1 Akorinto 4:17.) Pang’ono ndi pang’ono, mudzayamba kudziwa zambiri ndipo mudzathandiza kuti mpingo usinthe zinthu zina n’cholinga choti uzitsatira malangizo a gulu la Yehova. Mukatero, Yehova akhoza kukuthandizani ngati mmene anachitira ndi Elisa ndipo mukhoza kuchita zambiri kuposa aphunzitsi anu.—Yoh. 14:12.

18. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa ena mumpingo n’kofunika kwambiri masiku ano?

18 Tikukhulupirira kuti malangizo amene ali mu nkhaniyi komanso yapita ija athandiza akulu kupeza nthawi yophunzitsa ena. Tikukhulupiriranso kuti anthu ophunzitsidwawo alandira bwino malangizo amene angapatsidwe n’cholinga choti athandize poweta nkhosa za Yehova. Zonsezi zidzathandiza kuti mipingo ikhale yolimba ndiponso kuti aliyense adzakhalebe wokhulupirika pa nthawi yovuta kwambiri imene ikubwerayi.

^ ndime 5 Ngati wachinyamata akukonda kwambiri Yehova, ndi wodzichepetsa ndipo akukwaniritsa zimene Malemba amanena, akulu angamuvomereze kukhala mtumiki wothandiza ngakhale kuti sanakwanitse zaka 20.—1 Tim. 3:8-10, 12; onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1989, tsamba 29.

^ ndime 11 Mungakambirane naye mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 14 mpaka 16, ndime 8 mpaka 13; ndiponso buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” mutu 16, ndime 1 mpaka 3.