Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Munavomereza Kuti Zimenezi Zichitike”

“Munavomereza Kuti Zimenezi Zichitike”

“Mwazibisa kwa anzeru ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana.”—LUKA 10:21.

1. N’chifukwa chiyani Yesu “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera”? (Onani chithunzi pamwambapa.)

BAIBULO limanena kuti pa nthawi ina Yesu “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera.” Mwina Yesu ankamwetulira ndipo nkhope yake inkaoneka yosangalala. N’chifukwa chiyani anasangalala chonchi? Iye anatumiza ophunzira ake 70 kukalalikira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndipo ankafuna kudziwa mmene ophunzira ake angagwirire ntchitoyi chifukwa panali adani ambiri. Mwachitsanzo, anthu ophunzira kwambiri monga alembi ndi Afarisi ankadana ndi ntchito yolalikira. Iwo ankalimbikitsa anthu kuona kuti Yesu ndi kalipentala wamba komanso kuti ophunzira ake ndi “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13; Maliko 6:3) Komabe ophunzira a Yesu anabwerera ali osangalala kwambiri. Iwo anagwira bwino ntchitoyi ngakhale kuti ankatsutsidwa ndi anthu komanso ziwanda. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti agwire ntchitoyi mosangalala ndiponso molimba mtima?—Werengani Luka 10:1, 17-21.

2. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anatchula ophunzira ake kuti ana? (b) Nanga n’chiyani chinathandiza otsatira a Yesu kumvetsa mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa?

2 Yesu anauza Yehova kuti: “Ndikutamanda inu Atate pamaso  pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwabisira zinthu zimenezi anthu anzeru ndi ozindikira ndipo mwaziulula kwa tiana. Inde Atate wanga, ndikukutamandani chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike.” (Mat. 11:25, 26) Apatu Yesu sankatanthauza kuti ophunzira ake anali ana enieni. Koma ankatanthauza kuti anthu ophunzira kwambiri pa nthawiyo, omwe ankadziona kuti ndi anzeru, akanaona ophunzira a Yesu monga ana. Komanso Yesu ankaphunzitsa otsatira ake kuti ayenera kukhala odzichepetsa ndiponso ofunitsitsa kuphunzira ngati ana. (Mat. 18:1-4) Chifukwa choti ophunzirawo anali odzichepetsa, mzimu woyera unawathandiza kumvetsa mfundo zofunika kwambiri. Koma anthu anzeru omwe ankanyoza ophunzirawo anali onyada ndipo anapitirizabe kupusitsidwa ndi Satana.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

3 N’zosadabwitsa kuti Yesu anasangalala kwambiri. Anaona kuti Yehova akuthandiza anthu odzichepetsa kumvetsa mfundo zozama ngakhale kuti anali osaphunzira ndipo ankaoneka opanda nzeru. Yesu anasangalala poona kuti Atate wake amakonda kuphunzitsa m’njira yosavuta. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amakondabe kuphunzitsa m’njira imeneyi? Tiyeni tikambirane yankho la funso limeneli. Nafenso tidzasangalala ngati mmene Yesu anachitira.

MFUNDO ZOZAMA ZIKUFOTOKOZEDWA M’NJIRA YOSAVUTA

4. Kodi Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta ikuthandiza bwanji anthu?

4 M’zaka za posachedwapa, gulu la Yehova lakhala likuyesetsa kuphunzitsa m’njira yosavuta. Tiyeni tione zinthu zitatu zimene lachita. Choyamba, layamba kupanga Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta. * Magaziniyi yathandiza kwambiri anthu amene amavutika kulankhula kapena kuwerenga Chingelezi. Makolo ambiri aona kuti magaziniyi yathandiza ana awo kuphunzira Nsanja ya Olonda, yomwe ndi njira yaikulu imene gulu limatiphunzitsira. Anthu ambiri alemba makalata oyamikira zimenezi. Mlongo wina analemba kuti zinkamuvuta kwambiri kuyankha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Iye anati: “Ndinkangokhala duu osayankha.” Koma atayamba kugwiritsa ntchito magazini ya m’Chingelezi chosavuta, anati: “Tsopano ndimayankha pa phunzirolo kangapo ndipo ndasiya kuchita mantha. Ndikuthokoza kwambiri Yehova ndiponso abale inu.”

5. Kodi kukonzanso Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kwathandiza bwanji?

5 Chachiwiri, Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika la Chingelezi linakonzedwanso ndipo linatuluka pa msonkhano wapachaka pa October 5, 2013. * Tsopano, malemba ambiri ali ndi mawu ochepa koma ndi omveka bwino kwambiri. Mwachitsanzo, kale lemba la Yobu 10:1 linali ndi mawu 27 koma tsopano lili ndi mawu 19 okha. Lemba la Miyambo 8:6 linali ndi mawu 20 koma tsopano lili ndi mawu 13 basi. Panopa, malemba onse awiriwa ndi osavuta kumva kuposa kale. M’bale wina wodzozedwa amene wakhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zambiri anati: “Ndangomaliza kumene kuwerenga buku la Yobu m’Baibulo latsopanoli ndipo ndikuona kuti ndayamba kulimvetsa bwino.” Anthu ambiri ananenanso zinthu ngati zimenezi.

6. Kodi mumamva bwanji mukaganizira mfundo zatsopano zokhudza lemba la Mateyu 24:45-47?

 6 Chachitatu, zinthu zina zasintha pa nkhani ya kufotokoza Malemba. Mwachitsanzo, tinasangalala kwambiri ndi mfundo zatsopano zimene Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013 inafotokoza zokhudza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Inanena kuti kapolo wokhulupirika ndi Bungwe Lolamulira pomwe ‘antchito apakhomo’ ndi anthu onse amene amalandira chakudya, kaya ndi odzozedwa kapena a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Timasangala kwambiri kuphunzira mfundo zatsopano ngati zimenezi komanso kuziphunzitsa kwa anthu ena. Koma kodi Yehova amasonyezanso bwanji kuti amakonda kuphunzitsa m’njira yosavuta?

NKHANI ZA M’BAIBULO ZAFOTOKOZEDWA M’NJIRA YOSAVUTA

7, 8. Tchulani zinthu zina za m’Baibulo zimene zinali zophiphiritsa.

7 Ngati mwatumikira Yehova kwa zaka zambiri, mwina mwaona kuti gulu lakhala likusintha mmene limafotokozera nkhani za m’Baibulo. Poyamba, linkakonda kusonyeza kuti nkhani zina za m’Malemba zinkaphiphiritsira zinthu zina zam’tsogolo. Koma kodi pali umboni wa m’Malemba wosonyeza kuti nkhani zina zimaphiphiritsira zinthu zam’tsogolo? Inde ulipo. Mwachitsanzo, Yesu ananena za “chizindikiro cha mneneri Yona.” (Werengani Mateyu 12:39, 40.) Yehova akanapanda kupulumutsa Yona, ndiye kuti manda ake akanakhala m’mimba mwa chinsomba. Ndiyeno Yesu ananena kuti masiku amene Yona anakhala m’mimba mwa chinsombacho ankaimira masiku amene Yesuyo adzakhale m’manda.

8 M’Baibulo mulinso zinthu zina zophiphiritsira zam’tsogolo. Paulo anafotokozanso zinthu zambiri zoterezi. Mwachitsanzo, ananena kuti zimene zinachitika m’banja la Abulahamu, Hagara ndi Sara zinkaimira zimene zinachitika pakati pa Yehova ndi mtundu wa Isiraeli ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. (Agal. 4:22-26) Zinthu za m’Chilamulo cha Mose monga chihema, kachisi, Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo komanso mkulu wa ansembe zinali ngati “mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera.” (Aheb. 9:23-25; 10:1) Timasangalala kwambiri kuphunzira mfundo ngati zimenezi. Koma kodi zinthu zonse ndiponso anthu onse otchulidwa m’Baibulo amaimira zinthu zina zam’tsogolo?

9. Kodi nkhani ya Naboti inkafotokozedwa bwanji m’mbuyomu?

9 Kale, mabuku athu ankafotokoza kwambiri zinthu m’njira imeneyi. Chitsanzo ndi nkhani ya Naboti. Iye anaimbidwa mlandu wabodza n’kuphedwa. Yezebeli ndi amene anakonza chiwembuchi pofuna kuti Ahabu atenge munda wa Naboti. (1 Maf. 21:1-16) Mu 1932, mabuku athu ankanena kuti nkhaniyi imaimira zinthu zina. Ankati Ahabu ndi Yezebeli amaimira Satana ndi gulu lake pomwe Naboti amaimira Yesu. Ndiye ankati imfa ya Naboti imaimira imfa ya Yesu. Koma pofika mu 1961, buku lathu lina (“Let Your Name Be Sanctified”) linanena kuti Naboti amaimira odzozedwa pomwe Yezebeli amaimira matchalitchi amene amati ndi achikhristu. Ndiye linanena kuti zimene Yezebeli anachita pozunza Naboti zimaimira kuzunzidwa kwa odzozedwa m’masiku otsiriza. Kwa zaka zambiri, anthu a Yehova ankalimbikitsidwa kwambiri ndi njira imeneyi yofotokozera nkhani za m’Baibulo. Koma kodi n’chiyani chachititsa kuti pakhale kusintha?

10. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti gulu likusamala kwambiri pa nkhani yofotokoza Malemba? (b) Kodi masiku ano gulu limatsindika kwambiri chiyani?

 10 Koma Yehova wakhala akuthandiza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azichita zinthu mwanzeru kwambiri. Choncho gulu layamba kusamala kwambiri kuti lisamafulumire kunena kuti zinthu zinazake zikuphiphiritsira zinthu zina. Limachita zimenezi pokhapokha ngati pali umboni wa m’Malemba. Zikuonekanso kuti anthu ambiri zimawavuta kumvetsa nkhani za m’Baibulo zimene zinafotokozedwa m’njira yosonyeza kuti zikuphiphiritsira zinazake. Kafotokozedwe kameneka kamakhala kovuta kumvetsa, kukumbukira komanso kutsatira mfundo zake pa moyo wathu. Koma vuto lalikulu ndi lakuti phunziro lenileni la nkhaniyo limasokonekera chifukwa choti tikuyesa kufufuza kuti zinthuzo zikuimira chiyani. Choncho masiku ano, gulu lasintha ndipo limafotokoza zinthu m’njira yosavuta. Limatsindika zimene tikuphunzira pa nkhani ya chikhulupiriro, kupirira, kudzipereka kwa Mulungu komanso makhalidwe ena abwino. *

Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Naboti? (Onani ndime 11)

11. (a) Kodi masiku ano gulu limafotokoza bwanji nkhani ya Naboti? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti aliyense angaphunzire zambiri pa nkhani yake? (c) N’chifukwa chiyani masiku ano gulu silikonda kufotokoza nkhani za m’Baibulo m’njira yosonyeza kuti zikuphiphiritsira zinazake? (Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” patsamba 17.)

11 Ndiyeno kodi tingafotokoze bwanji nkhani ya Naboti? Masiku ano mabuku athu amafotokoza nkhaniyi m’njira yosavuta. Amati Naboti anafa chifukwa choti anali wokhulupirika kwa Mulungu ndipo nkhani yake siimira zimene zinachitikira Yesu kapena odzozedwa. Naboti sanasiye kumvera lamulo la Yehova ngakhale pamene ankazunzidwa ndi olamulira. (Num. 36:7; 1 Maf. 21:3) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yake? Ifenso tiyenera kumvera Yehova ngakhale pamene tikuzunzidwa. (Werengani 2 Timoteyo 3:12.) Aliyense angamvetse mosavuta, kukumbukira komanso kutsatira zimene tikuphunzira pa nkhaniyi.

12. (a) Kodi tinganene kuti nkhani zonse za m’Baibulo zimangopereka phunziro popanda kuimira zinazake? Fotokozani. (b) N’chiyani chimatithandiza kufotokoza zinthu zozama m’njira yosavuta? (Onani mawu a m’munsi.)

 12 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti nkhani zonse za m’Baibulo zimangopereka phunziro popanda kuimira zinazake? Ayi. N’zoona kuti masiku ano mabuku athu sakonda kunena kuti nkhani inayake ikuphiphiritsira zakutizakuti. Koma m’malomwake, amanena kuti nkhaniyo ikutikumbutsa zakutizakuti kapena ikufanana ndi zakutizakuti. Mwachitsanzo, tikhoza kunena kuti kukhulupirika kwa Naboti pozunzidwa kumatikumbutsa za kukhulupirika kwa Yesu ndi odzozedwa. Koma ikhoza kutikumbutsanso za kukhulupirika kwa anthu ambiri a “nkhosa zina.” Yehova amakonda kwambiri kuphunzitsa m’njira yosavuta chonchi. *

MAFANIZO A YESU AFOTOKOZEDWA M’NJIRA YOSAVUTA

13. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti masiku ano gulu limafotokoza mafanizo a Yesu m’njira yosavuta.

13 Yesu anali mphunzitsi wabwino kwambiri kuposa aliyense padzikoli. Iye ankakonda kugwiritsa ntchito mafanizo. (Mat. 13:34) Mafanizo ake ankathandiza anthu kumvetsa nkhani ndipo ankawafika pamtima. Masiku ano, mabuku athu akufotokozanso mafanizo a Yesu m’njira yosavuta. Mwachitsanzo, Nsanja ya Olonda ya July 15, 2008 inafotokoza m’njira yosavuta fanizo la zofufumitsa, kanjere kampiru ndiponso la khoka. Panopa timadziwa kuti mafanizowa akuimira Ufumu wa Mulungu ndiponso zimene Ufumuwu wachita pothandiza kuti anthu achoke m’dziko loipali n’kulowa m’gulu la Yehova.

14. (a) Kodi m’mbuyomu tinkafotokoza bwanji fanizo la Msamariya wachifundo? (b) Kodi timafotokoza bwanji fanizoli masiku ano?

14 Kodi timafotokozanso nkhani zina zimene Yesu ananena m’njira yomweyi? Inde koma si zonse. Pali nkhani zina zimene zimaphiphiritsira zinazake pomwe zina zimangopereka phunziro lofunika. Ndiyeno kodi tingasiyanitse bwanji nkhani zoterezi? Pang’ono ndi pang’ono tayamba kuzindikira mmene tingazisiyanitsire. Mwachitsanzo, taganizirani mmene tinkafotokozera fanizo la Yesu lonena za Msamariya wachifundo. (Luka 10:30-37) Mu 1924, Nsanja ya Olonda inanena kuti Msamariyayu amaimira Yesu. Inati msewu wopita ku Yerusalemu kuchokera ku Yeriko, womwe unali wotsetsereka, umaimira makhalidwe a anthu amene akhala akulowa pansi kuyambira pamene Adamu ndi Hava anachimwa. Inanenanso kuti achifwamba a mu fanizoli amaimira makampani akuluakulu ndipo wansembe ndi Mlevi amaimira magulu achipembedzo. Koma masiku ano mabuku athu amagwiritsa ntchito fanizoli posonyeza kuti Akhristufe sitiyenera kukhala ndi tsankho tikamathandiza anthu ena, makamaka polalikira. Timasangalala kwambiri kuona kuti Yehova akutiphunzitsa m’njira yosavuta.

15. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

15 M’nkhani yotsatira tidzakambirana fanizo lina la Yesu lokhudza anamwali 10. (Mat. 25:1-13) Kodi Yesu ankafuna kuti fanizoli litithandize bwanji masiku ano? Kodi chinthu chilichonse m’nkhaniyi chimaphiphiritsira zinazake? Kapena kodi ankangofuna kupereka phunziro lotithandiza m’masiku otsiriza ano? Tidzayankha mafunsowa m’nkhani yotsatira.

^ ndime 4 Nsanja ya Olonda ya m’Chingelezi chosavuta inayamba kutuluka mu July 2011. Koma tsopano magaziniyi yayamba kutuluka m’zilankhulo zinanso.

^ ndime 5 Zinthu zikukonzedwa kuti Baibulo limeneli lituluke m’zilankhulo zinanso.

^ ndime 10 Mwachitsanzo, buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo limafotokoza moyo wa anthu 14 otchulidwa m’Baibulo. Koma limatsindika kwambiri zimene tikuphunzira kwa anthuwo osati zimene nkhani yawo ikuphiphiritsira.

^ ndime 12 M’Mawu a Mulungu muli nkhani zina “zovuta kuzimvetsa” ndipo zina zimapezeka m’makalata a Paulo. Koma anthu onse amene analemba Baibulo ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera. Mzimu womwewo umathandiza Akhristu masiku ano kumvetsa mfundo za m’Malemba. Timatha kumvetsa ngakhale zitakhala “zinthu zozama za Mulungu.”—2 Pet. 3:16, 17; 1 Akor. 2:10.