Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi tingathandize bwanji abale ndi alongo amene amavutika akamva fungo la perefyumu?

N’zovuta kuti anthu amene amavutika akamva fungo la perefyumu apeweretu fungolo chifukwa amakumana ndi anthu osiyanasiyana tsiku lililonse. Ena afunsapo ngati n’zotheka kuti abale ndi alongo asiye kugwiritsa ntchito perefyumu akamapita ku misonkhano yampingo komanso ikuluikulu.

N’zoona kuti palibe amene angafune kuti abale ndi alongo azivutika akakhala pa misonkhano. Ndipotu tonse timafuna kuti tizilimbikitsana pa misonkhanoyi. (Aheb. 10:24, 25) Komabe amene amavutika kwambiri ndi fungo la perefyumu moti amalephera nthawi zina kupita ku misonkhano, akhoza kukambirana ndi akulu. Kupereka malamulo pa nkhaniyi n’kosagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Koma akulu angapereke malangizo othandiza mpingo kumvetsa mavuto amene anthu oterewo akukumana nawo. Akulu angaone mmene zinthu zilili ndipo angakambe nkhani pa nthawi ya zofunika pampingo pa Msonkhano wa Utumiki. Iwo angagwiritse ntchito nkhani za m’mbuyomu zopezeka m’mabuku athu zokhudza nkhaniyi. Kapena mwina angapereke chilengezo koma mosamala kwambiri. * Koma akulu sangapereke zilengezo zokhudza nkhani imeneyi nthawi ndi nthawi. Zimenezi zili choncho chifukwa nthawi zonse pa misonkhano yathu pamabwera anthu atsopano ndiponso alendo amene sakudziwa za vutoli. Ndiyeno tikufuna kuti anthuwo azimasuka. Sitikufuna kuti aliyense azimangika pa misonkhano yathu chifukwa chogwiritsa ntchito perefyumu.

Ngati mumpingo muli vutoli, akulu angakonze zoti anthu ovutikawo azikhala pamalo enaake kwaokha m’Nyumba ya Ufumu. Mwachitsanzo, mwina muli chipinda china chimene angakhale n’kumamvabe bwinobwino misonkhano. Ngati zimenezi n’zosatheka ndipo anthu akuvutika kwambiri, akuluwo angakonze zoti misonkhano izijambulidwa kapena anthuwo azimvera misonkhanoyo kudzera pafoni. Izi n’zimene mipingo ina imachita pothandiza anthu odwala omwe sangayende.

M’zaka za posachedwapa, Utumiki Wathu wa Ufumu wakhala ukulimbikitsa abale ndi alongo kuti aziganizira kwambiri nkhaniyi akamapita ku misonkhano yachigawo. Popeza misonkhano ikuluikulu yambiri imachitikira m’nyumba zimene simudutsa mphepo, anthu amapemphedwa kuti asamagwiritse ntchito perefyumu wokhala ndi fungo lamphamvu. Izi zili choncho makamaka pa misonkhano yachigawo chifukwa chakuti nthawi zambiri sangakonze malo apadera amene anthu oterewa angakhale. Koma malangizo amene amaperekedwa chifukwa cha misonkhano yachigawowa si lamulo loti anthu azigwiritsanso ntchito pa misonkhano yampingo.

M’dziko loipali, tonse timavutika ndi mavuto obwera chifukwa cha uchimo. Timayamikira kwambiri anthu akamatithandiza pa mavuto athu. Anthu ena amadzimana kuti asamagwiritse ntchito perefyumu akamapita ku misonkhano. Izi zingasonyeze chikondi chifukwa zingathandize anthu ovutika ndi fungolo kuti azifika bwinobwino pa misonkhanoyo.

 Kodi pali umboni wotsimikizira kuti Pontiyo Pilato analikodi?

Dzina la Pilato m’Chilatini linalembedwa pamwalapa

Baibulo limafotokoza za Pontiyo Pilato m’nkhani yokhudza mlandu umene Yesu anazengedwa komanso kuphedwa kwake. Anthu amene amawerenga Baibulo amadziwa zimenezi. (Mat. 27:1, 2, 24-26) Koma dzina lake limapezekanso m’mabuku ena a mbiri yakale. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limanena kuti Pontiyo Pilato amatchulidwa ndiponso kufotokozedwa m’mabuku a mbiri yakale kuposa bwanamkubwa wachiroma wina aliyense amene ankalamulira Yudeya.

Mwachitsanzo, katswiri wina wa mbiri yakale ya Ayuda, dzina lake Josephus, anatchula kwambiri Pontiyo Pilato m’mabuku ake. Josephus analemba za nthawi zitatu zimene Pilato anakumana ndi mavuto polamulira Yudeya. Katswiri winanso wa mbiri yakale ya Ayuda dzina lake Philo analemba za nthawi ina imene Pilato anakumana ndi mavuto. Katswiri wina wa mbiri yakale ya Aroma dzina lake Tacitus analemba mbiri yokhudza mafumu a Roma. Nayenso anatsimikizira kuti Pontiyo Pilato ndi amene analamula kuti Yesu aphedwe pa nthawi imene Tiberiyo ankalamulira Roma.

Mu 1961, akatswiri ofukula zinthu zakale, anapeza mwala pamalo amene panali bwalo la masewero ku Caesarea m’dziko la Israel. Mwalawo unalembedwa dzina la Pilato m’Chilatini. Zina zimene zinalembedwapo zikuonekabe (onani chithunzi chake) koma anthu akuti poyamba zinalembedwa kuti: “Tiberieum Pontiyo Pilato, yemwe ndi bwanamkubwa wa Yudeya, wapereka (nyumbayi) kwa milungu yolemekezeka.” Zikuoneka kuti nyumbayi inali kachisi wolemekeza Tiberiyo, yemwe anali mfumu ya Roma.

Kodi mlongo ayenera kuvala chinachake kumutu akamachititsa phunziro ali ndi m’bale amene ndi wofalitsa?

Nkhani ya “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2002 inanena kuti mlongo ayenera kuvala mpango kapena chipewa akamachititsa phunziro ali ndi m’bale amene ndi wofalitsa wobatizidwa kapena wosabatizidwa. Koma titaonanso bwino nkhaniyi, tazindikira kuti m’pofunika kusintha pang’ono malangizowa.

Ngati mlongo akuchititsa phunziro ali ndi m’bale wobatizidwa, ayenera kuvala chinachake kumutu. Akamachita zimenezi ndiye kuti akulemekeza dongosolo la Yehova mumpingo wachikhristu. Tikutero chifukwa chakuti ndi udindo wa m’baleyo kuchititsa phunzirolo. (1 Akor. 11:5, 6, 10) Koma akhozanso kupempha m’baleyo kuti achititse phunzirolo ngati ndi woyenerera ndipo angakwanitse kutero.

Komabe ngati mlongo akuchititsa phunziro ali ndi m’bale, amene ndi wofalitsa wosabatizidwa ndiponso si mwamuna wake, Baibulo silisonyeza kuti ayenera kuvala chinachake kumutu. Ngakhale zili choncho, chikumbumtima cha alongo ena chingawalimbikitse kuvalabe chinachake kumutu pa nthawi ngati imeneyi.

^ ndime 2 Mungaone mfundo zina zokhudza vutoli m’nkhani yakuti “Kuthandiza Anthu Odwala MCS” mu Galamukani! ya August 8, 2000, tsamba 24 mpaka 26.