Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  February 2015

Khalani Olimba Mtima Ndiponso Ozindikira Ngati Yesu

Khalani Olimba Mtima Ndiponso Ozindikira Ngati Yesu

“Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupirira mwa iye.”1 PET. 1:8.

1, 2. (a) Kodi tingatani kuti tidzapulumuke? (b) Kodi tingatani kuti tipitirizebe kuyenda m’njira ya ku moyo wosatha?

TITANGOKHALA ophunzira a Yesu, tinayamba ulendo wapadera umene ungatithandize kudzapeza moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padzikoli. Yesu anati: “Koma amene adzapirire mpaka pa mapeto [a moyo wake kapena a dziko loipali], ndiye amene adzapulumuke.” (Mat. 24:13) Zoonadi, munthu angadzapulumuke ngati atayesetsa kukhalabe wokhulupirika. Komabe, tiyenera kusamala kuti tisasochere kapena kusokonezedwa ndi zinthu zina poyenda m’njira ya ku moyo wosatha. (1 Yoh. 2:15-17) Kodi tingatani kuti tipitirizebe kuyenda m’njirayi?

2 Tiyenera kutsanzira Yesu kuti tipitirizebe kuyenda pa njira imeneyi. Zimene anachita zinalembedwa m’Baibulo ndipo kuliwerenga kungatithandize kumudziwa bwino. Tingayambe kumukonda komanso kumukhulupirira. (Werengani 1 Petulo 1:8, 9.) Tisaiwale kuti mtumwi Petulo ananena kuti Yesu anatisiyira chitsanzo choti tizitsatira mapazi ake mosamala kwambiri. (1 Pet. 2:21)  Tikamatsatira mapazi akewo mosamala, tingadzapirire mpaka mapeto. * M’nkhani yapitayi, tinaphunzira zimene tingachite kuti titsanzire Yesu pa nkhani ya kukhala odzichepetsa ndiponso achifundo. Koma m’nkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tikhale olimba mtima komanso ozindikira ngati Yesu.

YESU NDI WOLIMBA MTIMA

3. Kodi munthu wolimba mtima amatani, nanga tingatani kuti tikhale olimba mtima?

3 Kulimba mtima kungatithandize kuti tisafooke. Munthu wolimba mtima amapirira mavuto ndipo amakhala wopanda mantha pochita zinthu zoyenera. Polimbana ndi mavuto, iye amakhala ndi chikhulupiriro ndipo sanyinyirika. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene munthu wolimba mtima amachita? Choyamba, amaopa Mulungu ndipo izi zimachititsa kuti asamaope anthu. (1 Sam. 11:7; Miy. 29:25) Chachiwiri, amakhala ndi chiyembekezo. Izi zimathandiza kuti aziganizira kwambiri zinthu zabwino zimene akuyembekezera osati mavuto amene akukumana nawo. (Sal. 27:14) Chachitatu, amakhala ndi chikondi chenicheni moti amalolera kuvutika pofuna kuchita zabwino. (Yoh. 15:13) Choncho kuti tikhale olimba mtima tiyenera kukhulupirira Mulungu komanso kutsatira mapazi a Mwana wake.Sal. 28:7.

4. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima pamene anali “pakati pa aphunzitsi” m’kachisi? (Onani chithunzi patsamba 10.)

4 Yesu ali ndi zaka 12 anasonyeza kuti anali wolimba mtima pochita zabwino. Kumbukirani zimene anachita “atakhala pakati pa aphunzitsi” m’kachisi. (Werengani Luka 2:41-47.) Aphunzitsiwo ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose komanso malamulo ena amene anthu anawonjezeramo. Koma Yesu sanawaope n’kungokhala chete. M’malomwake ‘ankawafunsa mafunso.’ Mafunso ake ayenera kuti sanali ngati a mwana. N’kutheka kuti ankafunsa mafunso ochititsa aphunzitsiwo kuganiza komanso kudabwa. Ngati aphunzitsiwo ankayesa kumufunsa mafunso ofuna kumukola, zinawakanika. Tikutero chifukwa Baibulo limasonyeza kuti onse amene ankamumvetsera, ngakhalenso aphunzitsiwo, “anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” N’zosachita kufunsa kuti mayankho ake ankachokera m’Mawu a Mulungu.

5. Kodi Yesu anasonyeza kulimba mtima m’njira zina ziti?

5 Yesu anasonyeza kulimba mtima m’njira zinanso. Mwachitsanzo, anadzudzula mwamphamvu atsogoleri achipembedzo amene ankasocheretsa anthu. (Mat. 23:13-36) Iye sanalolenso kusokonezedwa ndi dziko loipali. (Yoh. 16:33) Ndiponso ankalalikirabe ngakhale kuti ankatsutsidwa kwambiri. (Yoh. 5:15-18; 7:14) Kawiri konse, iye anathamangitsa anthu ochita malonda m’kachisi.Mat. 21:12, 13; Yoh. 2:14-17.

6. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima pa tsiku limene anaphedwa?

6 Zimene Yesu ankachita akakumana ndi mavuto ndi zolimbikitsa kwambiri. Taganizirani zimene anachita usiku woti aphedwa mawa lake. Iye ankadziwa mavuto amene angakumane nawo chifukwa cha zimene Yudasi ankafuna kuchita. Koma pamene anali pa mwambo wa Pasika, Yesu anauza Yudasiyo kuti: “Zimene wakonza kuchita, zichite mwamsanga.” (Yoh. 13:21-27) Asilikali atabwera kuti adzamugwire m’munda wa Getsemane, iye sanachite mantha koma anadzipereka. Yesu ankadziwa kuti aphedwa koma analankhula molimba mtima pofuna kuteteza ophunzira ake.  (Yoh. 18:1-8) Atafika kukhoti n’kumafunsidwa mafunso, anavomereza zoti iye ndi Khristu komanso Mwana wa Mulungu. Anachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti mkulu wa ansembe ankafuna kupeza chifukwa chomuphera. (Maliko 14:60-65) Yesu anakhala wokhulupirika mpaka pamene anaphedwa pa mtengo wozunzikirapo. Atatsala pang’ono kumalizika, ananena mofuula kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”Yoh. 19:28-30.

KHALANI OLIMBA MTIMA NGATI YESU

7. Kodi achinyamatanu mungasonyeze bwanji kuti mumanyadira mwayi wodziwika ndi dzina lakuti Yehova ndiponso kuti ndinu olimba mtima?

7 Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima ngati Yesu? Kusukulu. Achinyamata amakhala olimba mtima akamauza anthu kusukulu kuti ndi a Mboni za Yehova. Amachita zimenezi ngakhale kuti amadziwa zoti anzawo angawavutitse kapena kuwanyoza. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti amanyadira kudziwika ndi dzina lakuti Yehova. (Werengani Salimo 86:12.) Mwina anzanu angakukakamizeni kuti mukhale ndi chibwenzi. Koma muli ndi zifukwa zomveka zochokera m’Baibulo zokuchititsani kuti mukane zimenezo. Mutha kugwiritsa ntchito chigawo choyamba cha m’buku lakuti Zimene Achinyamata Amadzifunsa (Buku Lachiwiri) kuti muwafotokozere zimene mumakhulupirira. (1 Pet. 3:15) Mukamachita zimenezi, mudzasangalala podziwa kuti mukutsatira mfundo za Mulungu.

8. Kodi tili ndi zifukwa ziti zotichititsa kulalikira molimba mtima?

8 Mu utumiki. Akhristufe tiyenera ‘kulankhula molimba mtima’ chifukwa chodalira “mphamvu ya Yehova.” (Mac. 14:3) Kodi tili ndi zifukwa ziti zotichititsa kulalikira molimba mtima? Choyamba, timadziwa kuti uthenga umene timalalikira ndi woona chifukwa chakuti ndi wochokera m’Baibulo. (Yoh. 17:17) Chachiwiri, timadziwa kuti “ndife antchito anzake a Mulungu” ndipo iye amatipatsa mzimu wake woyera. (1 Akor. 3:9; Mac. 4:31) Chachitatu, timadziwanso kuti tikamalalikira mwakhama timasonyeza kuti timakonda Yehova ndiponso anzathu. (Mat. 22:37-39) Choncho timakhala olimba mtima ndipo sitingasiye kulalikira. Timauza anthu mwakhama mfundo zoona za m’Baibulo kuti asamakhulupirire mabodza amene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa. (2 Akor. 4:4) Tipitirizabe kulalikira uthenga wabwino ngakhale kuti anthu ena safuna kumvetsera, amatinyoza komanso kutitsutsa.1 Ates. 2:1, 2.

9. Kodi tingasonyeze bwanji kulimba mtima pa mavuto?

9 Pa mavuto. Tikamadalira Mulungu timakhala ndi chikhulupiriro ndipo timatha kupirira mavuto molimba mtima. Mnzathu akamwalira timalira koma sititaya mtima. Timadalira ndi mtima wonse “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse” kuti atipatse mphamvu. (2 Akor. 1:3, 4; 1 Ates. 4:13) Tikadwala kapena kuvulala kwambiri zimatipweteka koma sitisiya kumvera Mulungu. Timakana chithandizo chilichonse chimene chimasemphana ndi mfundo za m’Baibulo. (Mac. 15:28, 29) Tikakhala ndi nkhawa, “mitima yathu ingatitsutse” koma sititaya mtima podziwa kuti Mulungu amakhala “pafupi ndi anthu a mtima wosweka.” *1 Yoh. 3:19, 20; Sal. 34:18.

YESU NDI WOZINDIKIRA

10. Kodi munthu wozindikira amatani?

10 Munthu wozindikira amatha kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika n’kusankha zinthu mwanzeru. (Aheb. 5:14) Anthu ena amati munthu wozindikira ndi amene “amatha kusankha  zinthu mwanzeru pa nkhani zokhudza ubwenzi wake ndi Mulungu.” Munthu wotere amalankhula komanso kuchita zinthu zimene zimasangalatsa Mulungu. Iye amayesetsa kulankhula mawu amene angalimbikitse ena osati kuwafooketsa. (Miy. 11:12, 13) Amakhalanso “wosafulumira kukwiya.” (Miy. 14:29) Munthuyo “amayenda panjira yabwino,” kapena kuti amayesetsa kuchita zinthu zabwino pa moyo wake. (Miy. 15:21) Kodi tingatani kuti tikhale ozindikira? Tikufunika kumaphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kutsatira zimene tikuphunzirazo. (Miy. 2:1-5, 10, 11) Chofunika kwambiri ndi kuphunzira chitsanzo cha Yesu, yemwe anali wozindikira kuposa munthu aliyense.

11. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wozindikira pa zimene ankalankhula?

11 Pa zinthu zonse zimene Yesu ankachita ndiponso kulankhula, anasonyeza kuti ndi wozindikira. Zolankhula zake. Iye ankachita zinthu mwanzeru polalikira uthenga wabwino. Mwachitsanzo, ankagwiritsa ntchito “mawu ogwira mtima” ndipo anthu ankachita chidwi kwambiri. (Luka 4:22; Mat. 7:28; Luke 4:16-21) Pophunzitsa anthu, nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu basi. Ankachita kuwerenga kapena kutchula malemba oyenerera kuti anthuwo amvetse mfundo yake. (Mat. 4:4, 7, 10; 12:1-5) Yesu ankafotokozanso Malemba momveka bwino ndipo ankawafika pa mtima omvera ake. Iye atangoukitsidwa, analankhula ndi ophunzira ake awiri amene ankapita ku Emau. Pa nthawiyo, ‘anawatanthauzira zinthu zokhudza iyeyo m’Malemba onse.’ Kenako ophunzirawo anati: ‘Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kutifotokozera Malemba momveka bwino?’Luka 24:27, 32.

12, 13. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu sankakwiya msanga ndiponso anali wololera?

12 Maganizo ndi mtima wake. Popeza Yesu anali wozindikira, ‘sankakwiya msanga’ ndipo anali “wofatsa.” (Miy. 16:32; Mat. 11:29) Nthawi zonse ankachita zinthu moleza mtima ndi ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina. (Maliko 14:34-38; Luka 22:24-27) Anakhalabe wodekha ngakhale pamene anthu ena ankamuchitira zachipongwe.1 Pet. 2:23.

13 Mtima wozindikira unathandiza Yesu kukhala wololera. Iye sankangokakamira Chilamulo cha Mose, koma ankachita zinthu mogwirizana ndi mfundo za m’Chilamulocho. Chitsanzo ndi nkhani imene ili pa Maliko 5:25-34. (Werengani.) Mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi anadutsa m’chigulu cha anthu n’kukagwira malaya a Yesu, ndipo anachiritsidwa. Malinga ndi Chilamulo, mayiyu sankayenera kukhudza aliyense. (Lev. 15:25-27) Koma Yesu ankazindikira “zinthu zofunika za m’Chilamulo” monga ‘chilungamo ndi chifundo.’ Choncho sanadzudzule mayiyu. (Mat. 23:23) M’malomwake anamuuza mokoma mtima kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.” N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yesu ndi wozindikira ndipo anakomera mtima mayiyu.

14. Kodi Yesu anasankha kuchita chiyani pa moyo wake, nanga n’chiyani chinamuthandiza kuti asasokonezedwe?

14 Posankha zochita. Yesu anasonyezanso kuti ndi wozindikira chifukwa ankasankha zochita mwanzeru ndipo sankalola chilichonse kumusokoneza. Iye anasankha kuti pa moyo wake wonse azigwira ntchito yolalikira uthenga wabwino basi. (Luka 4:43) Sanalole chilichonse kumulepheretsa ndipo ankasankha zochita mogwirizana ndi ntchito yakeyi. Moyo wake unali wosalira zambiri n’cholinga choti akhale ndi nthawi yambiri yotumikira Mulungu. (Luka 9:58) Anaphunzitsanso anthu ena ntchitoyi n’cholinga choti anthuwo  adzaipitirize iye akadzaphedwa. (Luka 10:1-12; Yoh. 14:12) Yesu analonjeza otsatira ake kuti aziwathandiza pa ntchitoyi mpaka “m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”Mat. 28:19, 20.

KHALANI OZINDIKIRA NGATI YESU

Zindikirani zimene anthu angachite nazo chidwi n’kukambirana nawo mogwirizana ndi zinthuzo (Onani ndime 15)

15. Kodi zolankhula zathu zingasonyeze bwanji kuti ndife ozindikira?

15 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhani yozindikira? Zolankhula zathu. Tikakhala ndi Akhristu anzathu tiyenera kulankhula mawu olimbikitsa osati okhumudwitsa. (Aef. 4:29) Tikamauza anthu ena za Ufumu wa Mulungu, mawu athu ayenera kukhala ‘okoma ngati tawathira mchere.’ (Akol. 4:6) Tizionetsetsa mavuto amene anthu akukumana nawo komanso zinthu zimene angachite nazo chidwi kenako n’kulankhula nawo mogwirizana ndi zinthuzo. Tisaiwale kuti kulankhula mokoma mtima kungathandize anthu kuti atilandire bwino n’kumvetsera uthenga wathu. Pofotokoza zimene timakhulupirira, tizigwiritsa ntchito Baibulo. Tiyenera kutchula malemba ndipo ngati n’kotheka tizichita kuwawerenga. Tizikumbukira kuti uthenga wa m’Baibulo ndi wamphamvu kwambiri kuposa zilizonse zimene tinganene.Aheb. 4:12.

16, 17. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitifulumira kukwiya komanso ndife ololera? (b) Kodi tingatani kuti chilichonse chisatisokoneze pa ntchito yathu?

16 Maganizo ndi mtima wathu. Munthu wozindikira amakhala wodziletsa ndipo ‘safulumira kukwiya.’ (Yak. 1:19) Anthu ena akatilakwira timaganizira zimene zawachititsa. Tikatero mtima wathu umakhala m’malo ndipo zimakhala zosavuta kuti ‘tinyalanyaze zolakwa’ zawo. (Miy. 19:11) Munthu wozindikira amakhalanso wololera. Sitiyembekezera zambiri kwa Akhristu anzathu podziwa kuti mwina akukumana ndi mavuto ena amene sitikuwadziwa. Timalemekeza maganizo awo ndipo ngati n’zotheka timalolera zimene akufuna.Afil. 4:5.

17 Posankha zochita. Akhristufe timazindikira kuti palibe ntchito ina yofunika kuposa yolalikira uthenga wabwino. Timasankha bwino zochita n’cholinga choti tisasokonezedwe pa ntchito yathuyi. Nthawi zonse timaika patsogolo zinthu zokhudza kulambira ndipo moyo wathu umakhala wosalira zambiri. Timachita izi pofuna kuti nthawi yathu yambiri tiigwiritse ntchito polalikira uthenga wabwino mapeto asanafike.Mat. 6:33; 24:14.

18. (a) Kodi tingatani kuti tiyendebe m’njira ya ku moyo wosatha? (b) Kodi inuyo mukufunitsitsa kuchita chiyani?

18 Kunena zoona, tasangalala kwambiri kukambirana makhalidwe ena abwino a Yesu. Tikhoza kusangalalanso kwambiri kuphunzira makhalidwe ena a Yesu n’kumayesetsa kumutsanzira. Tiyeni tiziyesetsa kutsatira mapazi ake mosamala kwambiri ndipo tikatero tidzakhala tikutsanziranso Yehova. Izi zidzathandiza kuti tiyendebe m’njira ya ku moyo wosatha komanso tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehovayo.

^ ndime 2 Mawu amene ali pa 1 Petulo 1:8, 9 ndi opita kwa Akhristu amene adzapite kumwamba. Komabe, mfundo ya mulembali ikukhudzanso anthu amene adzakhale padziko lapansili.

^ ndime 9 Onani zitsanzo za anthu amene analimba mtima pokumana ndi mavuto mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 2000, tsamba 24 mpaka 28 ndi Galamukani! ya May 8, 2003, tsamba 26 mpaka 29.