Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  November 2014

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oyera?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Oyera?

“Muzikhala oyera.”—LEV. 11:45.

1. Kodi buku la Levitiko lingatithandize bwanji?

M’BAIBULO lonse, buku la Levitiko ndi limene limanena mobwerezabwereza nkhani ya kukhala oyera. Atumiki a Yehova onse amafunika kukhala oyera. Choncho kumvetsa mfundo za m’buku limeneli kungatithandize kwambiri pa nkhaniyi.

2. Kodi mungalifotokoze bwanji buku la Levitiko?

2 Mose ndi amene analemba buku la Levitiko ndipo bukuli ndi mbali ya “Malemba onse” opindulitsa pa kuphunzitsa. (2 Tim. 3:16) Machaputala ake ambiri amatchula dzina la Yehova maulendo pafupifupi 10 kapena kuposerapo. Kumvetsa mfundo za m’buku la Levitiko kungatithandize kupewa zinthu zimene zinganyozetse dzina la Mulungu. (Lev. 22:32) Mawu akuti “Ine ndine Yehova” amapezeka kawirikawiri m’bukuli ndipo amatikumbutsa kufunika komvera Mulungu. Tingati bukuli ndi mphatso yochokera kwa Yehova yotithandiza kukhala oyera pomulambira. M’nkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana mfundo zofunika kwambiri za m’buku limeneli.

 KUKHALA OYERA N’KOFUNIKA

3, 4. Kodi kusamba kwa Aroni ndi ana ake kunkaimira chiyani? (Onani chithunzi patsamba 8.)

3 Werengani Levitiko 8:5, 6Yehova anasankha Aroni kuti akhale mkulu wa ansembe wa Aisiraeli ndipo ana ake anali ansembe. Aroni amaimira Yesu Khristu ndipo ana ake amaimira Akhristu odzozedwa. Ndiyeno kodi kusamba kwa Aroni kunkaimira kuyeretsedwa kwa Yesu? Ayi, Yesu anali wopanda uchimo ndiponso “wopanda chilema,” choncho sanafunike kuyeretsedwa. (Aheb. 7:26; 9:14) Koma Aroni akasamba n’kukhala woyera ankaimira Yesu yemwe ndi woyera komanso wachilungamo. Nanga kusamba kwa ana a Aroni kunkaimira chiyani?

4 Kusamba kwa ana a Aroni kunkaimira kuyeretsedwa kwa anthu odzozedwa amene asankhidwa kukhala ansembe kumwamba. Kodi odzozedwa amayeretsedwa pamene akubatizidwa? Ayi, ubatizo suchotsa machimo koma umasonyeza kuti munthuyo wadzipereka kwa Yehova Mulungu. Odzozedwa amayeretsedwa ndi “mawu a Mulungu.” (Aef. 5:25-27) Choncho kuti Mawuwa awayeretse, iwo ayenera kutsatira ndi mtima wonse zinthu zimene Khristu anaphunzitsa. Koma kodi nkhaniyi ikukhudzanso “nkhosa zina”?—Yoh. 10:16.

5. Kodi a nkhosa zina amayeretsedwa bwanji ndi Mawu a Mulungu?

5 Ana a Aroni sankaimira “khamu lalikulu” la nkhosa zina za Yesu. (Chiv. 7:9) Ndiyeno kodi Akhristu amenewa amayeretsedwanso ndi Mawu a Mulungu? Inde. Akhristuwa akawerenga m’Baibulo kuti magazi a Yesu ndi ofunika komanso angatiyeretse, amakhulupirira ndiponso amachita “utumiki wopatulika usana ndi usiku.” (Chiv. 7:13-15) Chifukwa choyeretsedwa nthawi zonse, odzozedwa ndiponso a nkhosa zina amakhalabe ndi “khalidwe labwino.” (1 Pet. 2:12) Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri akamaona odzozedwa ndiponso a nkhosa zina akugwirizana, kukhala oyera komanso kumvera Yesu, yemwe ndi M’busa wawo.

6. N’chifukwa chiyani tiyenera kudzifufuza?

6 Kodi tikuphunzira chiyani pa mfundo yoti ansembe ankafunika kukhala oyera? Anthu amene timaphunzira nawo Baibulo amaona kuti timakhala aukhondo komanso malo amene timasonkhana amakhala oyera. Koma nkhani yoti ansembe ankakhala oyera ikusonyezanso kuti munthu aliyense wolambira m’phiri la Yehova ayenera kukhala “woyera mumtima mwake.” (Werengani Salimo 24:3, 4; Yes. 2:2, 3.) Tiyenera kukhala ndi maganizo oyera, mtima woyera komanso kukhala aukhondo potumikira Mulungu. Kuti izi zitheke, tiyenera kudzifufuza nthawi ndi nthawi n’kumasintha ngati pali vuto. (2 Akor. 13:5) Mwachitsanzo, munthu wobatizidwa amene amaonera zolaula ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi kutereku ndinganene kuti ndine woyera?’ Ndiyeno angachite bwino kupempha thandizo kuti asiye zonyansazo.—Yak. 5:14.

KUMVERA KUMATITHANDIZA KUKHALA OYERA

7. Mogwirizana ndi Levitiko 8:22-24, kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani?

7 Pamene Aroni ndi ana ake ankapatsidwa udindo wa ansembe, Mose anatenga magazi a nkhosa n’kuwapaka ‘pakhutu lakumanja, pachala chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha kumwendo wa kumanja.’ (Werengani Levitiko 8:22-24.) Anachita zimenezi posonyeza  kuti ansembewo ankafunika kumvera Mulungu pogwira ntchito zawo. Yesu, yemwe ndi Mkulu wa Ansembe, anapereka chitsanzo chabwino kwa odzozedwa komanso nkhosa zina. Nthawi zonse ankamvera Yehova, kuchita zomusangalatsa komanso anali woyera.—Yoh. 4:31-34.

8. Kodi atumiki a Yehova onse ayenera kuchita chiyani?

8 Odzozedwa komanso a nkhosa zina ayenera kutsanzira Yesu pa nkhani ya kukhulupirika. Atumiki a Yehova onse ayenera kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu n’cholinga choti asamvetse chisoni mzimu woyera. (Aef. 4:30) Iwo ayenera ‘kupitiriza kuwongola njira zawo.’—Aheb. 12:13.

9. (a) Kodi abale atatu amene akhala akugwira ntchito ndi abale a m’Bungwe Lolamulira ananena zotani? (b) Kodi zimene ananenazi zingakuthandizeni bwanji kukhalabe oyera?

9 Chitsanzo pa nkhani yomvera ndi zimene ananena abale atatu omwe agwira ntchito kwa nthawi yaitali limodzi ndi abale a m’Bungwe Lolamulira. Mmodzi mwa abalewa anati: “Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira limodzi ndi abale odzozedwa. Koma poti timachitira limodzi zinthu zambiri, ndimatha kuona kuti nawonso si angwiro. Koma kwa zaka zonsezi, ndakhala ndikuyesetsa kumvera amene akutitsogolera.” M’bale wachiwiri anati: “Malemba monga 2 Akorinto 10:5, omwe amatilimbikitsa ‘kumvera Khristu’ andithandiza kuti ndizimvera ndi mtima wonse amene akutitsogolera.” M’bale wachitatu anati: “Tiyenera kumvera gulu la Yehova komanso anthu amene iye akuwagwiritsa ntchito. Tikatero tidzasonyeza kuti timakonda zimene iye amakonda komanso kudana ndi zimene amadana nazo. Tidzasonyezanso kuti timadalira malangizo ake komanso timafuna kumusangalatsa.” M’baleyu ankaona kuti chitsanzo chabwino pa nkhani yomvera ndi M’bale Nathan Knorr, yemwe anadzakhala m’Bungwe Lolamulira. Pa nthawi ina, abale ena ankakayikira mfundo zimene zinali mu Nsanja ya Olonda ya 1925 pa nkhani yakuti “Kubadwa kwa Mtundu.” Koma M’bale Knorr sanakayikire mfundozi ngakhale pang’ono. Maganizo amene abale atatuwa ananena angatithandize kuti tikhale anthu omvera n’cholinga choti tikhale oyera.

TIZIMVERA LAMULO LA MULUNGU LOKHUDZA MAGAZI

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera lamulo la Mulungu lokhudza magazi?

10 Werengani Levitiko 17:10. Yehova anauza Aisiraeli kuti ‘asamadye magazi alionse.’ Akhristu ayeneranso kupewa magazi alionse, kaya a nyama kapena a munthu. (Mac. 15:28, 29) Palibe aliyense amene angafune kuti Yehova ‘amukane’ n’kumuchotsa mumpingo wake. Tikutero chifukwa chakuti timamukonda ndiponso timafunitsitsa kumumvera. Ngakhale zitaoneka kuti tikhoza kumwalira, sitingamvere zonena za anthu amene sadziwa Yehova komanso samumvera. Timadziwa kuti anthu angatinyoze chifukwa chokana magazi, komabe timasankha kumvera Mulungu. (Yuda 17, 18) Kodi n’chiyani chingatithandize ‘kutsimikiza mumtima’ mwathu kuti tisadye kapena kuikidwa magazi?—Deut. 12:23.

11. Kodi zimene zinkachitika pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo zinali zofunika bwanji?

11 Zimene mkulu wa ansembe ankachita pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo zimatithandiza kumvetsa maganizo a Mulungu pa nkhani ya magazi. Magazi ankagwiritsidwa ntchito m’njira yapadera pophimba machimo a anthu amene  ankafuna kuti Mulungu awakhululukire. Ankawaza magazi a ng’ombe yamphongo komanso a mbuzi patsogolo pa chivundikiro cha likasa la pangano. (Lev. 16:14, 15, 19) Izi zinkathandiza kuti Yehova akhululukire Aisiraeli. Yehova ananenanso kuti munthu akapha nyama kuti adye ayenera kukhetsa magazi ake n’kuwafotsera ndi dothi chifukwa chakuti magaziwo amaimira “moyo wa nyama.” (Lev. 17:11-14) Kodi zimene ankachita ndi magaziwo zinangokhala mwambo chabe? Ayi. Mulungu anali atapereka kalekale lamulo loletsa kudya magazi kwa Nowa ndi ana ake. (Gen. 9:3-6) Kodi Akhristu ayeneranso kutsatira lamuloli?

12. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti magazi ndi ofunika kuti machimo akhululukidwe?

12 Paulo anauza Akhristu achiheberi kuti magazi ali ndi mphamvu yoyeretsa anthu. Iye anati: “Pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi malinga ndi Chilamulo, ndipo popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe machimo awo.” (Aheb. 9:22) Ananenanso kuti nsembe za nyama zinali zofunika koma zinkangokumbutsa Aisiraeli kuti anali ochimwa ndipo ankafunika nsembe ina yoti ichotseretu machimo awo. Chilamulo chinangokhala ‘mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zinali kubwera osati zinthu zenizenizo.’ (Aheb. 10:1-4) Ndiyeno kodi zikanatheka bwanji kuti machimo akhululukidwe?

13. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zoti Yesu anapereka kwa Yehova nsembe ya magazi ake?

13 Werengani Aefeso 1:7. Yesu ‘anadzipereka yekha chifukwa cha ifeyo’ ndipo nsembe yake imathandiza kwambiri anthu amene amakonda Yesuyo komanso Atate wake. (Agal. 2:20) Koma zimene Yesu anachita ataukitsidwa, ndi zimene zinathandiza kwambiri kuti anthufe tikhululukidwe machimo athu. Zimene anachitazo zikufanana ndi zimene zinkachitika pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Paja pa tsikulo, mkulu wa ansembe ankatenga  magazi a nyama n’kupita nawo ku Malo Oyera Koposa. Zinkakhala ngati wapita kwa Yehova n’kukapereka magaziwo. (Lev. 16:11-15) Mofanana ndi zimenezi, Yesu ataukitsidwa anapita kumwamba n’kukapereka kwa Yehova nsembe ya magazi ake. (Aheb. 9:6, 7, 11-14, 24-28) Timayamikira kwambiri kuti timakhululukidwa machimo n’kukhala ndi chikumbumtima choyera chifukwa chokhulupirira nsembe ya Yesu.

14, 15. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsa komanso kumvera lamulo la Mulungu lokhudza magazi?

14 Kodi mwaona tsopano chifukwa chimene Yehova amanenera kuti tisamadye magazi alionse? (Lev. 17:10) Kodi mwazindikira chifukwa chake Mulungu amanena kuti magazi ndi opatulika? Iye amaona kuti magazi amaimira moyo. (Gen. 9:4) Mwina pano mwaona kuti ndi bwino kuona magazi mmene Mulungu amawaonera ndiponso kumvera lamulo lake loti tiziwapewa. Kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, tiyenera kukhulupirira nsembe ya Yesu komanso kuona kuti magazi ndi opatulika kwa Yehova.—Akol. 1:19, 20.

15 Koma kodi mungatani ngati mwakumana ndi vuto lofuna kuti inuyo, wachibale wanu kapena mnzanu wapamtima aikidwe magazi? Nanga mungatani ngati mukufunika kusankha zochita pa nkhani yokhudza tizigawo tamagazi kapena njira zina zogwiritsira ntchito magazi? Ndi bwino kufufuziratu nkhani zimenezi panopa n’kukonzekera zimene mungachite. Kuchita zimenezi komanso kupemphera kungakuthandizeni kuti musadzasankhe zolakwika pa nthawi imene zinthu zavuta. Palibe amene angafune kukhumudwitsa Yehova pochita zinthu zimene iye watiletsa. Anthu ambiri, monga ogwira ntchito zachipatala, amalimbikitsa anzawo kupereka magazi n’cholinga choti apulumutse anthu. Koma Akhristu amadziwa kuti Yehova ndi woyenera kutiuza zochita pa nkhani ya magazi. Iye amanena kuti “magazi alionse” ndi opatulika. Choncho tiyenera kumvera lamulo lakeli zivute zitani. Tikudziwa kuti magazi a Yesu okha ndi amene angapulumutse anthu, kuthandiza kuti machimo awo akhululukidwe komanso kuti apeze moyo wosatha. Choncho tikamakhala oyera timasonyeza kuti timayamikira zimenezi.—Yoh. 3:16.

Kodi mudzamvera lamulo la Yehova lokhudza magazi zivute zitani?(Onani ndime 14 ndi 15)

N’CHIFUKWA CHIYANI MULUNGU AMAFUNA KUTI TIKHALE OYERA?

16. N’chifukwa chiyani anthu a Yehova ayenera kukhala oyera?

16 Mulungu atapulumutsa Aisiraeli, anawauza kuti: “Ndine Yehova amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti ndikusonyezeni kuti ndine Mulungu. Muzikhala oyera, chifukwa ine ndine woyera.” (Lev. 11:45) Yehova ankafuna kuti anthu ake akhale oyera chifukwa iye ndi woyera. Buku la Levitiko limatithandiza kuona kuti ifenso a Mboni za Yehova tiyenera kukhala oyera.

17. Kodi buku la Levitiko lakuthandizani bwanji?

17 Kukambirana mfundo zina za m’buku la Levitiko kwatithandiza kwambiri. Mwina panopa mukuyamikira kwambiri buku la m’Baibulo limeneli. Muyenera kuti mwamvetsa bwino kufunika kokhala oyera. Koma kodi pali mfundo zinanso zofunika zimene tingaphunzire m’bukuli? Kodi lingatithandizenso bwanji pa nkhani yokhala oyera potumikira Yehova? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.