Timapepala toitanira anthu tinkagwiritsidwa ntchito ku Tokyo ndipo tinkamwazidwa pa ndege ku Osaka

PA SEPTEMBER 6, 1926, m’bale wina wa ku Japan, amene anali woyang’anira dera ku United States, anabwerera kwawo kukachita umishonale. Ku Japan kunali munthu mmodzi yekha amene ankalandira Nsanja ya Olonda ndipo anayambitsa gulu la anthu ophunzira Baibulo mumzinda wa Kobe. Iye ndi amene anakachingamira m’baleyo. Ndiyeno Ophunzira Baibulo anachita msonkhano wawo woyamba mumzinda wa Kobe pa January 2, 1927. Anthu 36 anafika ndipo anthu 8 anabatizidwa. N’zoona kuti zinthu zinayamba bwino, koma kodi anthu ochepawa akanathandiza bwinobwino anthu okwana 60 miliyoni a ku Japan kuti adziwe Baibulo?

Mu May 1927, Ophunzira Baibulo akhama anayamba kuitana anthu ambirimbiri kuti adzamve nkhani za Baibulo. Abale anaika zikwangwani m’malo osiyanasiyana zoitanira anthu ku nkhani yoyamba imene inakambidwa mumzinda wa Osaka. Iwo anatumizanso timapepala tokwana 3,000 toitanira anthu otchuka. Anagawiranso timapepala toitanira anthu tokwana 150,000. Anaikanso uthenga woitanira anthu m’nyuzipepala zotchuka komanso pa matikiti a sitima okwana 400,000. Pa tsiku la nkhaniyo, ndege ziwiri zinadutsa m’mwamba mwa mzindawu n’kumamwaza timapepala toitanira anthu tokwana 100,000. Anthu pafupifupi 2,300 anabwera kudzamvetsera nkhani yakuti “Ufumu wa Mulungu Wayandikira.” Anthu anadzaziratu muholo moti anthu ena pafupifupi 1,000 anabwezedwa. Nkhaniyo itakambidwa, anthu oposa 600 anatsala kuti afunse mafunso. Pa miyezi ingapo yotsatira, nkhani zina za Baibulo zinakambidwa mumzinda wa Kyoto ndiponso m’mizinda ina kumadzulo kwa Japan.

Mu October 1927, Ophunzira Baibulo anakonza zoti nkhani zina zikambidwe mumzinda wa Tokyo. Iwo anatumizanso timapepala toitanira anthu otchuka monga wolamulira wa dzikolo, aphungu a nyumba ya malamulo, akuluakulu a asilikali ndiponso atsogoleri a zipembedzo. Ankaitana anthu pogwiritsa ntchito zikwangwani, manyuzipepala komanso anagawira timapepala tokwana 710,000. Anthu onse amene anadzamvetsera nkhani zitatu mumzindawu, anakwana 4,800.

AKOPOTALA AKHAMA

Katsuo ndi Hagino Miura

Akopotala (kapena kuti apainiya) ankathandiza kwambiri polalikira kunyumba ndi nyumba. Mlongo wina dzina lake Matsue Ishii ndi mwamuna wake Jizo anayenda pafupifupi dziko lonse la Japan. Anayambira kumpoto kwenikweni ku Sapporo kenako ku Sendai, ku Tokyo, ku Yokohama, ku Nagoya, ku Osaka, ku Kyoto, ku Okayama ndi ku Tokushima. Mlongoyu limodzi ndi mlongo Sakiko Tanaka anavala zovala zapadera za ku Japan popita kukaonana ndi akuluakulu a boma. Munthu wina amene anamupeza anapempha mabuku 300 akuti Zeze wa Mulungu ndiponso 300 akuti Deliverance kuti akawaike kumalaibulale akundende.

Munthu wina dzina lake Katsuo Miura ndi mkazi wake Hagino atapatsidwa buku ndi mlongo Ishii  anazindikira kuti apeza chipembedzo choona. Iwo anabatizidwa mu 1931 ndipo anayamba ukopotala. Nayenso Haruichi Yamada ndi mkazi wake Tane komanso achibale awo ena anamva uthenga wa Ufumu n’kubatizidwa chisanafike chaka cha 1930. Banjali linayamba ukopotala ndipo mwana wawo wamkazi dzina lake Yukiko anapita kukatumikira ku Beteli mumzinda wa Tokyo.

YEHU WAMKULU NDI WAMNG’ONO

Mumakalavani aakulu ngati awa munkagona anthu 6

Kalelo ku Japan magalimoto ankadula kwambiri ndipo misewu sinali yabwino. Choncho M’bale Kazumi Minoura ndi akopotala ena achinyamata ankagwiritsa ntchito makalavani. Makalavaniwo anawapatsa dzina loti Yehu, ati potengera Yehu amene ankayendetsa galeta ndipo anadzakhala mfumu ya Aisiraeli. (2 Maf. 10:15, 16) Makalavani ena atatu anali akuluakulu moti anali a mamita 2.2 m’litali, mamita 1.9 m’lifupi ndiponso mamita 1.9 kupita m’mwamba ndipo munkagona anthu 6. Panalinso timakalavani ting’onoting’ono tokokedwa ndi njinga ndipo munkagona anthu awiri basi. Nthambi ya ku Japan inapanga timakalavani ting’onoting’onoti tokwana 11. M’bale Kiichi Iwasaki anagwira nawo ntchito yopanga makalavaniwa ndipo anati: “Iliyonse inkakhala ndi tenti komanso batire la galimoto kuti azilumikizira kunyale zamagetsi.” Akopotala ankafalitsa uthenga wabwino m’dziko lonse la Japan. Iwo ankakoka makalavani awo kudutsa m’mapiri ndi m’zigwa kuchokera kumpoto kwenikweni ku Hokkaido mpaka kukafika kum’mwera kwenikweni ku Kyushu.

Mukakalavani ngati aka munkagona anthu awiri

Kopotala wina dzina lake Ikumatsu Ota anati: “Tikafika m’tauni, tinkaimika kalavani yathu m’mphepete mwa mtsinje kapena pamalo ena abwino. Choyamba, tinkapita kwa akuluakulu a boma kenako tinkayenda kunyumba ndi nyumba n’kumagawira mabuku athu. Tikamaliza tinkauyamba wopita kutauni ina.”

Pamene anthu 36 anasonkhana mumzinda wa Kobe, zinali ngati ‘ayamba kumanga ndi zinthu zochepa.’ (Zek. 4:10) Koma patangopita zaka 5, mu 1932 ku Japan kunali akopotala ndi ofalitsa okwana 103 ndipo anagawira mabuku oposa 14,000. Panopa abale ndi alongo akulalikira mwadongosolo kwambiri m’mizinda ya ku Japan ndipo ofalitsa pafupifupi 220,000 akuthandiza kuti uthenga wabwino uwale kwambiri kumeneko.—Nkhaniyi yachokera ku Japan.

Zithunzi za makalavani amene Kiichi Iwasaki anapanga ku Beteli ya ku Japan