Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Nsanja ya Olonda (Yophunzira)  |  September 2014

Kodi ‘Mukuyesetsa Kuti Mukhale Woyang’anira’?

Kodi ‘Mukuyesetsa Kuti Mukhale Woyang’anira’?

M’BALE wina dzina lake Fernando * anachita mantha pamene akulu awiri anamuuza kuti akufuna kuonana naye. Pa nthawiyi woyang’anira dera anali atayendera mpingo wawo. M’mbuyomo, woyang’anira derayo atafika maulendo angapo, akulu anafotokozera Fernando zimene angachite kuti akhale mkulu. Koma chifukwa chakuti panapita nthawi yaitali, iye anayamba kukayikira zoti angakhale mkulu. Choncho pa nthawiyi ankadera nkhawa kwambiri zimene akuluwo angamuuze.

Mkulu wina atayamba kulankhula, Fernando anatchera khutu kwambiri. Anagwiritsira ntchito lemba la 1 Timoteyo 3:1 pomufotokozera kuti akulu alandira kalata yonena kuti iye wavomerezedwa kukhala mkulu. Fernando anadabwa kwambiri n’kuwafunsa kuti, “Mwati bwanji?” Mkuluyo anabwerezanso zimene ananenazo ndipo Fernando anayamba kumwetulira. Atalengeza zimenezi kumpingo anthu onse anasangalala.

Kodi n’kulakwa kufuna kukhala woyang’anira mumpingo? Ayi. Paja lemba la 1 Timoteyo 3:1 limanena kuti: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino.” Abale ambiri amatsatira mfundo yapalembali ndipo amayesetsa kuti akhale oyang’anira mumpingo. N’chifukwa chake masiku ano pali akulu ndi atumiki othandiza ambirimbiri amene amathandiza anthu a Mulungu. Panopa mipingo ikuwonjezereka, choncho abale ena ayeneranso kuyesetsa kuti akhale oyang’anira. Koma kodi angachite bwanji zimenezi? Kodi anthu amene akuyesetsawo ayenera kuda nkhawa ngati mmene Fernando ankachitira?

ZIMENE MUYENERA KUCHITA

Mawu achigiriki amene anamasuliridwa kuti “kuyesetsa” amatanthauza zimene munthu amachita akafuna kutenga chinthu chimene chili patali. Mwina tingayerekezere ndi zimene munthu amachita akafuna kuthyola chipatso chimene chili m’mwamba. Koma izi sizikutanthauza kuti munthuyo  amachita kulakalaka mwadyera “kuti akhale woyang’anira.” Tikutero chifukwa chakuti munthu amafuna kukhala woyang’anira n’cholinga choti agwire “ntchito yabwino” osati kuti akhale pa udindo.

Zoyenera kuchita kuti munthu akhale woyang’anira zafotokozedwa pa 1 Timoteyo 3:2-7 ndi pa Tito 1:5-9. Pofotokoza zimene munthu ayenera kuchitazi, M’bale Raymond, amene wakhala mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Ndimaona kuti chofunika kwambiri ndi khalidwe la munthu. N’zoona kuti munthu amafunika kukhala wodziwa kuphunzitsa bwino. Koma munthuyo ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino, wadongosolo, wochereza alendo komanso wololera.”

Pamene mukuyesetsa kukhala woyang’anira, muzithandiza mpingo m’njira zosiyanasiyana

Munthu amene akufuna kukhala woyang’anira ayenera kupewa chinyengo komanso zinthu zodetsa n’cholinga choti akhale wopanda chifukwa chomunenezera. Ayeneranso kukhala wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino, wadongosolo komanso wololera. Akatero, abale ndi alongo amakhulupirira kuti akhoza kuwatsogolera komanso kuwathandiza. Ayenera kukhalanso wochereza alendo kuti ana ndiponso anthu amene angoyamba kumene kulambira Yehova azimasuka naye. Akakhalanso wokonda zabwino, amalimbikitsa ndiponso kuthandiza anthu odwala ndi achikulire. Iye amayesetsa kukhala ndi makhalidwewa n’cholinga choti athandize ena osati kuti apatsidwe udindo. *

Akulu amapereka malangizo komanso kulimbikitsa abale kuti ayesetse kukhala oyang’anira. Koma m’bale aliyense payekha ndi amene ali ndi udindo woyesetsa kuti akhale woyang’anira. M’bale Henry, yemwe watumikira monga mkulu kwa nthawi yaitali, anati: “Ngati munthu akufuna kukhala woyang’anira ayenera kuchita khama posonyeza kuti angakwanitsedi.” M’baleyu amagwiritsa ntchito lemba la Mlaliki 9:10 n’kumati: “‘Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse.’ Munthu ayenera kuyesetsa kuchita bwino chilichonse chimene akulu amupatsa. Ayeneranso kugwira mosangalala ntchito iliyonse imene wapatsidwa mumpingo, ngakhale  yosesa. Akulu adzaona zonse zimene akuchita mwakhamazo.” Ngati mukufuna kukhala mkulu, muyenera kutumikira Mulungu mwakhama komanso modalirika. Muyenera kukhala munthu wodzichepetsa osati wolakalaka udindo.—Mat. 23:8-12.

ZIMENE MUYENERA KUPEWA

Anthu ena amene akufuna kukhala oyang’anira amachita kuuza akulu m’njira inayake kapena kuwachitira zinazake kuti awayeneretse. Ena amakwiya akalangizidwa ndi akulu. Anthu oterewa ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikungofuna udindo kapena ndikufuna kusamalira nkhosa za Yehova modzichepetsa?’

Anthu amene akufuna kukhala oyang’anira azikumbukiranso kuti ayenera ‘kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.’ (1 Pet. 5:1-3) Munthu wachitsanzo chabwino amapewa kuchita zinthu mwachinyengo. Kaya wavomerezedwa kukhala mkulu kapena ayi, iye amayesetsa kukhala woleza mtima. Pajatu kukhala mkulu sikutanthauza kuti munthuyo sangalakwitse zinthu zina. (Num. 12:3; Sal. 106:32, 33) N’zothekanso kuganiza kuti tilibe vuto pomwe anzathu akuona mavuto ena amene tili nawo. (1 Akor. 4:4) Choncho akulu akatipatsa malangizo ochokera m’Malemba tiyenera kumvera osati kukwiya nawo. Tizingoyesetsa kutsatira zimene atiuzazo.

KODI MWAYESETSA KWA NTHAWI YAITALI?

Abale ena amaona kuti akulu akuchedwa kuwavomereza kukhala oyang’anira. Kodi nthawi zina zimakupwetekani chifukwa chakuti mwakhala mukuyesetsa kwa nthawi yaitali kuti mukhale woyang’anira? Ngati ndi choncho, kumbukirani mawu a m’Baibulo awa: “Chinthu chimene unali kuyembekeza chikalephereka, chimadwalitsa mtima. Koma chomwe unali kufuna chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.”—Miy. 13:12.

Munthu amavutika kwambiri mumtima akaona kuti zimene ankayembekezera sizikutheka. Zoterezi zinachitikiranso Abulahamu. Yehova anamulonjeza kuti adzakhala ndi mwana koma panapita zaka zambiri iye ndi Sara alibe mwana. (Gen. 12:1-3, 7) Ndiyeno atakalamba anadandaulira Yehova kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa chiyani ine? Taonani ndilibe mwana.” Ndiyeno Yehova anamutsimikizira kuti zimene walonjeza zidzachitikadi. Koma panapitanso zaka zina 14 Abulahamu asanakhale ndi mwana.—Gen. 15:2 -4; 16:16; 21:5.

Kodi Abulahamu anasiya kutumikira Yehova mosangalala ataona kuti pakupita nthawi yaitali? Ayi. Iye ankadziwa kuti Mulungu adzachita zimene walonjeza. Ankangoyembekezerabe zinthu zabwinozo. Paja mtumwi Paulo analemba kuti: “Abulahamu ataonetsa kuleza mtima, analandira lonjezo limeneli.” (Aheb. 6:15) Mulungu Wamphamvuyonse anadalitsa Abulahamu m’njira imene sankaiganizira. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Abulahamu?

Ngati mwakhala mukuyesetsa kwa nthawi yaitali kuti mukhale woyang’anira, pitirizani kudalira Yehova. Musasiye kumutumikira mosangalala. M’bale Warren, amene wathandiza anthu ambiri  kukhala oyang’anira anati: “Kuti munthu ayenerere kukhala woyang’anira zimatenga nthawi. Khalidwe la munthu komanso luso lake zimaonekera mwapang’onopang’ono chifukwa cha zochita zake kapena mmene amagwirira ntchito zimene wapatsidwa. Ena amaona kuti zinthu zikuwayendera bwino ngati apatsidwa udindo winawake. Koma maganizo amenewatu si abwino ndipo akhoza kusokoneza munthu. Dziwani kuti munthu amachita bwino ngati akutumikira Yehova mokhulupirika pa ntchito iliyonse ndiponso kulikonse.”

M’bale wina anadikira kwa zaka zoposa 10 kuti akhale mkulu. Iye anagwiritsa ntchito mfundo ya mu Ezekieli chaputala 1 pofotokoza zimene waphunzira. Iye anati: “Gulu la Yehova lili ngati galeta ndipo iye amaliyendetsa pa liwiro limene akufuna. Choncho Yehova amachita zinthu pa nthawi yake osati yathu. Ndiyeno pa nkhani yokhala woyang’anira, si bwino kumangoganizira zimene ifeyo tikufuna. Mwina Yehova akudziwa kuti zimene tikufunazo si zotiyenera pa nthawiyo.”

Ngati mukufuna kukhala woyang’anira, yesetsani kuthandiza mpingo kuti uzikhala wosangalala. Ngati mukuona kuti nthawi ikupita, yesetsani kuti musamade nkhawa kapena kutaya mtima. M’bale Raymond amene tamutchula kale uja anati: “Mtima wongofuna udindo umachititsa kuti munthu asamasangalale. Anthu oterewa saona zinthu zosangalatsa akamatumikira Yehova.” Muzingoyesetsa kukhala ndi makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa, makamaka kuleza mtima. Muziphunzira Malemba mwakhama kuti ubwenzi wanu ndi Mulungu ulimbe. Muzichitanso khama pa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. Muzitsogoleranso bwino banja lanu pa zinthu zokhudza kulambira. Muzisangalalanso mukakhala ndi abale ndi alongo anu. Mukamatero, mudzakhala wosangalala poyembekezera nthawi imene mudzakhale woyang’anira.

Yehova amafuna kuti abale aziyesetsa kuti akhale oyang’anira ndipo safuna kuti anthu azikhumudwa kapena kutaya mtima pomutumikira. Umu ndi mmenenso gulu lake limaonera zinthu. Mulungu amathandiza komanso kudalitsa anthu amene amakhala ndi zolinga zabwino pomutumikira. Paja Yehova akamatidalitsa “sawonjezerapo ululu.”—Miy. 10:22.

Ngakhale kuti mwayesetsa kwa nthawi yaitali kuti mukhale woyang’anira, pali zina zimene mungachite kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova. Yesetsanibe kukhala ndi makhalidwe abwino, kuchita khama mumpingo komanso kuthandiza banja lanu. Mukatero mudzakhala ndi mbiri yabwino ndipo Yehova sadzaiwala zonse zimene mukuchita. Kaya ndi udindo uti umene mungapatsidwe, pitirizani kutumikira Yehova mosangalala.

^ ndime 2 Tasintha mayina m’nkhaniyi.

^ ndime 8 Mfundo zimene tafotokoza m’nkhaniyi n’zothandizanso kwa amene akufuna kukhala atumiki othandiza. Zimene munthu angachite kuti akhale mtumiki wothandiza zili pa 1 Timoteyo 3:8-10, 12, 13.