Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzigwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu Chifukwa Ndi Amoyo

Muzigwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu Chifukwa Ndi Amoyo

“Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.”—AHEB. 4:12.

1, 2. Kodi Yehova anatuma Mose kuti akachite chiyani, nanga anamutsimikizira chiyani?

KODI mungamve bwanji mutauzidwa kuti mukalankhule m’malo mwa anthu a Yehova pamaso pa wolamulira wamphamvu kwambiri padziko lonse? Mwina mungachite mantha kapena mungadzikayikire. Kodi mungakonzekere bwanji zoti mukanene? Nanga mungatani kuti mawu anu akakhale amphamvu monga woimira Mulungu Wamphamvuyonse?

2 Izi n’zimene zinachitikira Mose. Iye anali “munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Koma Yehova anamutuma kwa Farao kuti akapulumutse anthu ake omwe ankazunzika chifukwa cha ukapolo ku Iguputo. Farao anali munthu wamwano komanso wokula mtima. (Eks. 5:1, 2) Koma Yehova anatuma Mose kukauza Farao kuti alole akapolo pafupifupi 3 miliyoni kuti achoke m’dzikolo. M’pake kuti Mose anafunsa Yehova kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao ndi kutulutsa ana a Isiraeli ku Iguputo?” Mose ayenera kuti ankaona kuti sangakwanitse zimenezo. Koma Yehova anamutsimikizira kuti sadzamusiya yekha. Iye anati: “Ndidzakhala nawe.”—Eks. 3:9-12.

3, 4. (a) Kodi Mose ankaopa chiyani? (b) Kodi mavuto amene Mose anakumana nawo angafanane bwanji ndi anu?

3 Kodi Mose ankaopa chiyani? Zikuoneka kuti ankaopa kuti  Farao sangamvetsere munthu wotumidwa ndi Yehova Mulungu. Komanso ankaopa kuti anthu a mtundu wake sangakhulupirire kuti Yehova anamutuma kuti akawatulutse mu Iguputo. Choncho Mose anauza Yehova kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira ndi kumvera mawu anga? Chifukwatu adzanena kuti, ‘Yehova sanaonekere kwa iwe.’”—Eks. 3:15-18; 4:1.

4 Tonsefe tingaphunzire mfundo yofunika kwambiri pa zimene Yehova anauza Mose komanso zimene zinachitika pambuyo pake. N’zoona kuti mwina simungafunike kukalankhula ndi wolamulira winawake. Koma kodi nthawi zina zimakuvutani kulankhula za Mulungu ndi Ufumu wake kwa anthu amene mumakumana nawo? Ngati ndi choncho, tiyeni tione zimene tingaphunzire kwa Mose.

“CHILI M’DZANJA LAKOCHO N’CHIYANI?”

5. Kodi Yehova anathandiza bwanji Mose kuti asachite mantha? (Onani chithunzi patsamba 11.)

5 Mose atafotokoza zimene ankaopa, Mulungu anamuthandiza. Buku la Ekisodo limati: “Yehova anamufunsa [Mose] kuti: ‘Chili m’dzanja lakocho n’chiyani?’ ndipo Mose anayankha kuti: ‘Ndodo.’ Kenako iye anati: ‘Iponye pansi.’ Anaiponya pansi ndipo inasanduka njoka. Pamenepo Mose anayamba kuthawa. Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Igwire kumchira.’ Choncho Mose anaigwira, ndipo inasandukanso ndodo m’dzanja lake. Popitiriza Mulungu anati: ‘Ukachite zimenezi kuti akakhulupirire kuti Yehova . . . anaonekera kwa iwe.’” (Eks. 4:2-5) Mulungu anapatsa Mose umboni wotsimikizira kuti uthenga wake unalidi wochokera kwa Yehova. Mulungu anachititsa ndodo yooneka ngati chinthu wamba kukhala yamoyo. Zimenezi zikanachititsa anthu kukhulupirira kuti Mose anatumidwadi ndi Yehova. Choncho Yehova anamuuza kuti: “Ndodo iyi izikakhala m’dzanja lako kuti ukaigwiritse ntchito pochita zizindikiro.” (Eks. 4:17) Zimene Mulungu anachitazi zinathandiza Mose kuti apite molimba mtima kwa Farao ndiponso kwa Aisiraeli.—Eks. 4:29-31; 7:8-13.

6. (a) Kodi tiyenera kukhala ndi chiyani tikamalalikira ndipo n’chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti “mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu”?

6 Kodi ifeyo tikamalalikira timakhala ndi chiyani m’dzanja lathu? Nthawi zambiri timatenga Baibulo. Kwa anthu ena, Baibulo likhoza kuoneka ngati buku wamba koma Yehova amatilankhula kudzera m’Mawu akewa. (2 Pet. 1:21) M’Baibulo muli malonjezo a Mulungu okhudza zimene zidzachitike mu ulamuliro wa Ufumu wake. Ponena za malonjezowo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Werengani Aheberi 4:12.) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a Yehova ndi amoyo? Chifukwa chakuti nthawi zonse Yehova akuchita zinthu zothandiza kuti malonjezo akewo akwaniritsidwe. (Yes. 46:10; 55:11) Munthu akazindikira mfundoyi, zimene amawerenga m’Baibulo zingamupatse mphamvu kuti asinthe zinthu pa moyo wake.

7. Kodi tingatani kuti ‘tizifotokoza bwino mawu a choonadi’?

7 Yehova watipatsa Mawu ake amoyo omwe angatithandize kutsimikizira kuti uthenga wathu ndi wochokera kwa iye. M’pake kuti Paulo atalemba kalata yake yopita kwa Aheberi, analemberanso Timoteyo n’kumulimbikitsa kuti ‘achite chilichonse chotheka kuti azifotokoza bwino mawu a choonadi.’ (2 Tim. 2:15) Kodi ifeyo tingatsatire bwanji malangizo a Paulowa? Tingachite zimenezi powerenga mokweza malemba oyenera omwe angafike anthu pamtima. Timapepala timene tinatulutsidwa mu 2013 tinapangidwa n’cholinga choti tizitithandiza kuchita zimenezi.

WERENGANI LEMBA LOYENERA

8. Kodi woyang’anira utumiki wina anati chiyani za timapepala tatsopano?

8 Timapepala tonse tatsopanoti anatipanga  mofanana. Choncho tikaphunzira kugwiritsa ntchito kamodzi, ndiye kuti taphunzira kugwiritsa ntchito tonse. Kodi n’tovuta kugwiritsa ntchito? Woyang’anira utumiki wina ku Hawaii, m’dziko la United States, analemba kuti: “Poyamba sitinkadziwa kuti timapepala tatsopanoti n’tothandiza kwambiri polalikira kunyumba ndi nyumba kapena m’malo ena.” M’baleyu anaona kuti anthu amayankha mosavuta funso limene lili patsamba loyamba la timapepalati, ndipo kawirikawiri zimenezi zimathandiza kuti azikambirana nawo mosavuta. Iye akuona choncho chifukwa chakuti funsolo limakhala ndi mayankho angapo. Choncho munthu amene akukambirana naye amangosankha yankho limodzi moti saopa kuti ayankha zolakwika.

9, 10. (a) Kodi timapepala tathu timatilimbikitsa bwanji kuwerenga Baibulo? (b) Kodi inuyo mumakonda kugwiritsa ntchito timapepala titi, ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Pakapepala kalikonse pali lemba limene tiyenera kuwerenga. Mwachitsanzo, onani kapepala kakuti Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi? Kaya munthu ayankhe kuti “inde,” “ayi” kapena “mwina adzatha,” mungapite patsamba lachiwiri n’kunena kuti, “Tiyeni tione zimene Baibulo limanena.” Kenako werengani Chivumbulutso 21:3, 4.

10 N’chimodzimodzinso ndi kapepala kakuti Kodi Baibulo Mumalikhulupirira? Kaya munthu wasankha yankho liti, ingopitani patsamba lachiwiri n’kunena kuti, “Baibulo limanena kuti ‘Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.’” Kenako munganene kuti, “Ndipotu palembali pali mfundo zinanso.” Ndiyeno tsegulani Baibulo lanu n’kuwerenga lemba lonse la 2 Timoteyo 3:16, 17.

11, 12. (a) N’chiyani chimatisangalatsa tikakhala mu utumiki? (b) Kodi timapepala tingatithandize bwanji kukonzekera maulendo obwereza?

11 Zimene munthu angachite zingakuthandizeni kuona ngati mungakambirane naye zinthu zina kapena ayi. Mulimonse mmene zingakhalire, timasangalala kuti tamupatsa kapepalako komanso kuti tamuwerengera Mawu a Mulungu, ngakhale litakhala vesi limodzi lokha. Mungadzapitirize kukambirana naye nthawi ina.

12 Patsamba lomaliza la kapepalaka pali kamutu kakuti “Ganizirani Mfundo Iyi.” Pansi pake pali funso komanso malemba amene mungadzakambirane naye nthawi ina. Kapepala kakuti Kodi Mukuganiza Kuti Zinthu Zidzakhala Bwanji M’tsogolo? kalinso ndi funso loti  mudzakambirane nthawi ina. Funso lake ndi lakuti, “Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti asinthe dzikoli kukhala labwino?” Pansi pa funsoli pali lemba la Mateyu 6:9, 10 ndi la Danieli 2:44. Kapepala kakuti Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka? kali ndi funso lakuti, “N’chifukwa chiyani timakalamba n’kufa?” Pansi pake pali lemba la Genesis 3:17-19 ndi la Aroma 5:12.

13. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji timapepala poyambitsa maphunziro a Baibulo?

13 Muzigwiritsa ntchito timapepalati poyambitsa maphunziro a Baibulo. Kapepala kalikonse kamatchulanso phunziro lina la m’kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, kapepala kakuti Kodi Dziko Lapansili Lili M’manja mwa Ndani? kamatchula phunziro 5 m’kabukuka. Kapepala kakuti Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala? kamatchula phunziro 9. Mukamagwiritsa ntchito timapepala m’njira imene takambiranayi ndiye kuti muzigwiritsa ntchito Baibulo pa ulendo woyamba komanso wobwereza. Zimenezi zingathandize kuti muziyambitsa maphunziro a Baibulo ambiri. Komanso munthu akachita sikani kachidindo kamene kali kuseri kwa kapepalaka angathe kutsegula nkhani ina pa webusaiti yathu imene ingamulimbikitse kuti aziphunzira Baibulo. Kodi pali zinanso zimene mungachite kuti muzigwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu mu utumiki?

MUZIKAMBIRANA NAWO NKHANI IMENE IKUWADETSA NKHAWA

14, 15. Kodi mungatsanzire bwanji Paulo mu utumiki wanu?

14 Pa utumiki wake, Paulo ankafunitsitsa kuthandiza “anthu ochuluka.” (Werengani 1 Akorinto 9:19-23.) Iye ananena kuti ankafunitsitsa kupindula “Ayuda . . . , anthu otsatira chilamulo . . . , anthu opanda chilamulo . . . [komanso] ofooka.” Izi zikusonyeza kuti ankalalikira ‘anthu osiyanasiyana, kuti mulimonse mmene zingakhalire apulumutseko ena.’ (Mac. 20:21) Kodi tingatsanzire bwanji Paulo pamene tikukonzekera kukalengeza uthenga wabwino kwa anthu osiyanasiyana m’gawo lathu?—1 Tim. 2:3, 4.

15 Mwezi uliwonse timapeza zitsanzo za ulaliki mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Yesani kuzigwiritsa ntchito. Koma ngati anthu m’gawo lanu akuda nkhawa ndi nkhani inayake, konzekerani ulaliki wogwira mtima wogwirizana ndi nkhaniyo. Choncho muziganizira zimene zimadetsa nkhawa anthu a m’dera lanu. Kenako ganizirani lemba limene lingawathandize. Woyang’anira dera wina ananena mmene iye ndi mkazi wake amagwiritsira ntchito Baibulo. Iye anati: “Anthu ambiri amalola kuti tiwawerengere vesi limodzi n’kulifotokoza mwachidule. Timawapatsa moni Baibulo lathu lili m’manja, kenako timawerenga lemba.” Tiyeni tione zitsanzo zina za nkhani, mafunso komanso malemba amene mungagwiritse ntchito m’gawo lanu.

Kodi mumagwiritsa ntchito bwino Baibulo komanso timapepala mu utumiki? (Onani ndime 8 mpaka 13)

16. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji lemba la Yesaya 14:7 mu utumiki?

16 Ngati kumene mukukhalako kumachitika zipolowe pafupipafupi, mungafunse kuti: “Kodi mungamve bwanji tsiku lina mutamva nkhani yakuti: ‘Dziko lonse lapansi lapuma, lilibenso chosokoneza. Anthu akusangalala ndipo akufuula mokondwera’? Izi ndi zimene Baibulo limanena pa Yesaya 14:7. Ndipotu m’Baibulo muli malonjezo ambiri a Mulungu osonyeza kuti m’tsogolo dziko lonse lidzakhala pa mtendere.” Ndiyeno pemphani kuti muwawerengere lemba limodzi m’Baibulo.

17. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji lemba la Mateyu 5:3 pokambirana ndi anthu?

17 Kodi m’dera lanu anthu ambiri amavutika kupeza zofunika pa moyo? Ngati ndi choncho, mungayambe kukambirana ndi anthu pofunsa kuti: “Kodi munthu akuyenera kumapeza ndalama zingati kuti azitha kusamalira banja lake?” Akayankha, munganene kuti: “Anthu ambiri amapeza ndalama zambiri kuposa zimenezo, koma mabanja awo sasangalalabe.  Ndiye chofunika n’chiyani?” Kenako werengani Mateyu 5:3 n’kuwapempha kuti muziphunzira nawo Baibulo.

18. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Yeremiya 29:11 polimbikitsa anthu?

18 Kodi anthu a m’dera lanu akuvutika chifukwa cha vuto linalake limene lachitika posachedwapa? Ngati ndi choncho mungayambe ndi mawu akuti: “Ndabwera kuti ndidzakulimbikitseni ndi mfundo ya palemba ili.” Ndiyeno werengani Yeremiya 29:11. (Werengani.) Kenako munganene kuti: “Kodi mwaona zinthu zitatu zimene Mulungu akufuna kutipatsa? ‘Mtendere,’ ‘chiyembekezo’ ndiponso ‘tsogolo labwino.’ N’zosangalatsa kuti akufuna kuti tikhale ndi moyo wabwino. Koma kodi zimenezi zingatheke bwanji?” Kenako musonyezeni mutu wogwirizana ndi nkhani imeneyi m’kabuku ka Uthenga Wabwino.

19. Kodi mungagwiritse ntchito bwanji lemba la Chivumbulutso 14:6, 7 pokambirana ndi anthu okonda kupemphera?

19 Kodi anthu a m’dera lanu ndi okonda kupemphera? Ngati ndi choncho, mungayambe ndi funso lakuti: “Kodi mngelo atabwera kudzalankhula nanu mungamumvere?” Kenako mungawerenge Chivumbulutso 14:6, 7. (Werengani.) Ndiyeno munganene kuti: “Palembali mngeloyu akunena kuti ‘opani Mulungu.’ Kodi akunena Mulungu wake uti? Zimene mngeloyu ananena zingatithandize kudziwa Mulunguyo. Iye anati ndi ‘amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.’ Kodi anapanga zimenezi ndi ndani?” Kenako werengani Salimo 124:8, limene limati: “Thandizo lathu lili m’dzina la Yehova, Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi.” Ndiyeno mupempheni kuti mudzakambirane mfundo zina zokhudza Yehova Mulungu.

20. (a) Kodi tingagwiritse ntchito bwanji lemba la Miyambo 30:4 pophunzitsa munthu dzina la Mulungu? (b) Kodi pali lemba lililonse limene mumakonda kuligwiritsa ntchito?

20 Pokambirana ndi wachinyamata mungayambe ndi mawu akuti: “Ndikufuna tiwerengere limodzi lemba limene lili ndi funso lofunika kwambiri.” Kenako mungawerenge Miyambo 30:4. (Werengani.) Mukatero munganene kuti: “Palibe munthu amene angachite zimene zafotokozedwa palembali. Choncho liyenera kuti likunena za Mlengi wathu. * Kodi dzina lake tingalidziwe bwanji? Ndingakonde kukusonyeza dzinali m’Baibulo.”

MUZIGWIRITSA NTCHITO BWINO MAWU A MULUNGU MU UTUMIKI

21, 22. (a) Kodi kuwerenga lemba loyenera kungasinthe bwanji moyo wa munthu? (b) Kodi inuyo tsopano muzichita zotani mu utumiki?

21 Mukhoza kudabwa kuona zimene anthu angachite mukawawerengera lemba loyenera. Mwachitsanzo, abale ena ku Australia atagogoda panyumba ya mayi wina, mmodzi anamufunsa kuti: “Kodi dzina la Mulungu mumalidziwa? Kenako anawerenga lemba la Salimo 83:18.” Pofotokoza zimene zinachitika panthawiyo, mayiyo anati: “Ndinadabwa koopsa. Atangonyamuka ndinauyamba ulendo wa makilomita 56 kupita kusitolo ya mabuku kuti ndikaone dzinalo m’Mabaibulo ena komanso mudikishonale. Nditatsimikizira kuti dzina lake ndi Yehova ndinazindikira kuti mwina pali zinthu zambiri zimene sindikuzidziwa.” Pasanapite nthawi yaitali, mayiyu ndi mwamuna amene anadzakwatirana naye anayamba kuphunzira Baibulo ndipo kenako onse anabatizidwa.

22 Baibulo limasintha anthu amene amaliwerenga n’kuyamba kukhulupirira malonjezo a Yehova. (Werengani 1 Atesalonika 2:13.) Uthenga wa m’Baibulo ndi wamphamvu ndipo umafika anthu pamtima kuposa mawu alionse amene tinganene. Choncho tiyeni nthawi zonse tizigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu chifukwa ndi amoyo.

^ ndime 20 Onani Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002, tsamba 5 ndi 6.