Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Akazi Amathandiza Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova

Akazi Amathandiza Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova

“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—SAL. 68:11.

1, 2. (a) Kodi Mulungu anapereka mphatso ziti kwa Adamu? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu anapatsa Adamu mkazi? (Onani chithunzi pamwambapa.)

YEHOVA anali ndi cholinga polenga dziko lapansili. Iye “analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yes. 45:18) Adamu, yemwe ndi munthu woyamba kulengedwa, anali wangwiro. Mulungu anamuika m’munda wokongola kwambiri wa Edeni kuti azikhalamo. Adamu ayenera kuti ankasangalala kwambiri ndi mitengo ndiponso mitsinje yokongola komanso nyama zosiyanasiyana zochititsa chidwi. Koma sikuti Adamu anali ndi zonse zofunika. Yehova anazindikira zimenezi n’kunena kuti: “Si bwino kuti munthu akhale yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.” Kenako Mulungu anagonetsa Adamu tulo tofa nato, n’kuchotsa nthiti yake imodzi. Ndiyeno ‘anapanga mkazi kuchokera kunthitiyo.’ Adamu atadzuka anasangalala kwambiri ndipo anati: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga.”—Gen. 2:18-23.

2 Mkazi amene Mulungu anapatsa Adamu anali mphatso yapadera kwambiri chifukwa anali womuthandiza woyenerera. Mkaziyo akanathanso kubereka ana angwiro ndipo umenewu unali mwayi waukulu. M’pake kuti “Adamu anatcha mkazi wake dzina  lakuti Hava, chifukwa anali kudzakhala mayi wa munthu aliyense wamoyo.” (Gen. 3:20; mawu am’munsi) Patapita nthawi, dziko lonse likanakhala paradaiso ndipo mukanadzaza anthu angwiro. Anthuwo akanathanso kumalamulira zamoyo zina.—Gen. 1:27, 28.

3. (a) Kodi Adamu ndi Hava ankafunika kuchita chiyani kuti adalitsidwe ndi Mulungu, koma chinachitika n’chiyani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

3 Kuti Adamu ndi Hava alandire madalitso onsewa komanso kuti akwaniritse cholinga cha Mulungu, ankafunika kumvera Yehova ndi kugonjera ulamuliro wake. (Gen. 2:15-17) Koma n’zomvetsa chisoni kuti iwo anamvera “njoka yakale ija” yemwe ndi Satana, ndipo anachimwira Mulungu. (Chiv. 12:9; Gen. 3:1-6) Kodi kusamvera kumeneku kwakhudza bwanji akazi? Koma kodi akazi oopa Mulungu anachita zotani kalelo? N’chifukwa chiyani tinganene kuti akazi achikhristu masiku ano ndi “khamu lalikulu”?—Sal. 68:11.

ZOTSATIRA ZA KUSAMVERA MULUNGU

4. Adamu ndi Hava atachimwa, kodi ndi ndani amene anaimbidwa mlandu waukulu?

4 Mulungu atafunsa Adamu za kusamvera kwake, iye anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” (Gen. 3:12) Adamu sanavomereze tchimo lake. M’malomwake anaimba mlandu mkazi wake komanso Mulungu. Onse awiri Adamu ndi Hava anachimwa koma Adamu ndi amene anaimbidwa mlandu waukulu. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa kudzera mwa uchimo.”—Aroma 5:12.

5. Kodi zimene Mulungu wachita polola kuti anthu ndi angelo osamvera azidzilamulira okha zasonyeza chiyani?

5 Satana anachititsa Adamu ndi Hava kuganiza kuti sakufunikira kulamuliridwa ndi Yehova. Zimenezi zinachititsa kuti pakhale funso lakuti: Kodi woyenera kulamulira ndi ndani? Kuti funsoli liyankhidwe, Mulungu analola kuti anthu komanso angelo osamvera azidzilamulira okha. Iye ankadziwa kuti zimenezi zidzasonyeza kuti sitingathe kudzilamulira. Ulamulirowu wangobweretsa mavuto ambirimbiri. Mwachitsanzo, pa zaka 100 zapitazi anthu okwana 100,000,000 aphedwa pa nkhondo ndipo ambiri mwa iwo anali amuna, akazi ndiponso ana osalakwa. Zonsezi zikusonyeza kuti “munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” (Yer. 10:23) Chifukwa chodziwa zimenezi, timaona kuti Yehova ndi woyenera kutilamulira.—Werengani Miyambo 3:5, 6.

6. Kodi m’mayiko ambiri anthu amaona bwanji akazi?

6 Amuna komanso akazi akumana ndi mavuto ambiri m’dziko la Satanali. (Mlal. 8:9; 1 Yoh. 5:19) Koma akazi ndi amene achitiridwa nkhanza kwambiri. Padziko lonse, akazi atatu pa akazi 10 alionse amanena kuti achitiridwa nkhanza ndi amuna. M’madera ena, anthu amakonda ana aamuna chifukwa choganiza kuti ndi amene adzakhalabe ndi dzina la abambo awo komanso kusamalira makolo ndi agogo awo. M’mayiko ena, anthu safuna kukhala ndi ana aakazi ndipo ambiri amachotsa mimba akadziwa kuti adzabereka mwana wamkazi.

7. Kodi Mulungu anasonyeza bwanji kuti amalemekezanso akazi?

7 Mulungu sasangalala akaona kuti akazi akuchitiridwa nkhanza. Iye amachita zinthu ndi akazi mwachilungamo ndipo amawalemekeza. Yehova anasonyeza zimenezi polenga Hava. Iye sanamulenge kuti akhale kapolo wa Adamu koma anali munthu wangwiro wokhala ndi makhalidwe abwino kuti azithandiza kwambiri Adamu. Chimenechi ndi chifukwa china chomwe chinachititsa Mulungu  kuona kuti “zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Gen. 1:31) Zonse zinalidi zabwino chifukwa Mulungu anapatsa amuna komanso akazi chilichonse chowathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino.

AKAZI AMENE YEHOVA ANKASANGALALA NAWO

8. (a) Kodi inuyo mungafotokoze bwanji khalidwe la anthu ambiri? (b) Kodi Yehova wakhala akusangalala ndi anthu otani?

8 Anthu atangopanduka mu Edeni, khalidwe lawo linayamba kuipa. Ndipo m’zaka 100 zapitazi, zinthu zasokonekera kwambiri. Baibulo linaneneratu kuti makhalidwe a anthu adzaipa kwambiri ‘m’masiku otsiriza’ ndipo ndi mmene zilili masiku ano moti tinganene kuti tikukhaladi ‘nthawi yovuta’ kwambiri. (2 Tim. 3:1-5) Koma Yehova, yemwe ndi “Ambuye Wamkulu Koposa,” wakhala akusangalala ndi amuna komanso akazi amene amamukhulupirira, kumvera malamulo ake komanso kulola kuti aziwalamulira.—Werengani Salimo 71:5.

9. Kodi ndi anthu angati amene anapulumuka Chigumula, ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Pamene Mulungu ankawononga anthu oipa m’masiku a Nowa, anthu ochepa anapulumuka. Ngati abale ake a Nowa anali moyo pa nthawiyo, ndiye kuti nawonso anaphedwa. (Gen. 5:30) Chiwerengero cha amuna amene anapulumuka chinali chofanana ndi cha akazi. Amene anapulumuka anali Nowa ndi mkazi wake, ndiponso ana ake atatu ndi akazi awo. Iwo anapulumutsidwa chifukwa chakuti ankaopa Mulungu n’kumachita zimene iye amafuna ndipo Yehova ankasangalala nawo. Anthu mabiliyoni onse amene ali padzikoli ndi zidzukulu za anthu 8 amenewa.—Gen. 7:7; 1 Pet. 3:20.

10. N’chifukwa chiyani Yehova ankasangalala ndi akazi ena akale?

10 Ndiyeno patapita zaka zambiri, akazi ena okhulupirika ankachitanso zinthu zosangalatsa Mulungu. Zimenezi sizikanatheka akanakhala kuti ndi anthu okonda kudandaula kapena kunyinyirika. (Yuda 16) Sara ayenera kuti sankadandaula pamene anachoka kumzinda wa Uri, womwe unali wotukuka, n’kumakakhala m’mahema kudziko lina. M’malomwake, anali “womvera kwa Abulahamu, ndipo anali kumutcha kuti ‘mbuyanga.’” (1 Pet. 3:6) Ndiye panalinso Rabeka, yemwe Yehova anamupereka kwa Isaki ndipo anakhala mkazi wabwino kwambiri. M’pake kuti Isakiyo “anam’konda kwambiri, ndipo anatonthozedwa pambuyo pa imfa ya mayi ake.” (Gen. 24:67) N’zosangalatsa kuti masiku ano pali alongo ambiri oopa Mulungu ngati mmene analili Sara ndi Rabeka.

11. Kodi akazi awiri achiheberi anasonyeza bwanji kulimba mtima?

11 Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo, ankachulukana kwambiri moti Farao analamula kuti ana onse aamuna aziphedwa akangobadwa. Ndiye taganizirani zimene Sifira ndi Puwa anachita. Akazi awiriwa ayenera kuti ankayang’anira azamba achiheberi. Iwo ankaopa Yehova ndipo analimba mtima n’kukana zopha anawo. Ndipo Yehova anawadalitsa powapatsa mabanja awoawo.—Eks. 1:15-21.

12. Fotokozani zimene Debora ndi Yaeli anachita.

12 M’masiku a oweruza, mneneri wina wamkazi dzina lake Debora, anasangalatsanso Mulungu. Iye analimbikitsa woweruza wina dzina lake Baraki ndipo anathandiza kuti Aisiraeli asamaponderezedwe ndi Akanani. Debora analoseranso kuti munthu wamkazi ndi amene adzamalizitse kugonjetsa Akanani, osati Baraki. Ananena kuti Yehova adzapereka mkulu wa asilikali a Akanani, dzina lake Sisera, “m’manja mwa munthu wamkazi.” Izi zinachitikadi. Sisera anaphedwa ndi mkazi wina, yemwe sanali Mwisiraeli, dzina lake Yaeli.—Ower. 4:4-9, 17-22.

13. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za Abigayeli?

 13 M’zaka za m’ma 1000 B.C.E., Abigayeli anasangalatsanso Mulungu. Iye anali wanzeru kwambiri koma mwamuna wake dzina lake Nabala anali wachabechabe, wankhanza komanso wopanda nzeru. (1 Sam. 25:2, 3, 25) Pa nthawi inayake, Davide ndi anthu ake ankalondera chuma cha Nabala. Koma Davideyo atapempha zinthu zina, Nabala anakana ‘n’kulalatira’ anthu amene Davide anawatuma. Ndiyeno, Davide anapsa mtima n’kukonzeka kuti akaphe Nabala ndi antchito ake. Abigayeli atamva zimenezi anatenga chakudya ndi zakumwa n’kukapereka kwa Davide ndi anthu ake. Izi zinathandiza kuti anthu asaphedwe. (1 Sam. 25:8-18) Zitatero, Davide anamuuza kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli, amene wakutumiza kudzakumana nane lero!” (1 Sam. 25:32) Ndiyeno Nabala atafa, Davide anakwatira Abigayeli.—1 Sam. 25:37-42.

14. (a) Kodi ana aakazi a Salumu anathandiza pa ntchito iti? (b) Kodi masiku ano alongo ena amafanana bwanji ndi ana aakazi a Salumu?

14 Pamene asilikali a Babulo ankawononga Yerusalemu komanso kachisi wake mu 607 B.C.E., amuna, akazi komanso ana ambiri anaphedwa. Ndiyeno mpanda wa Yerusalemu unamangidwanso mu 455 B.C.E. ndipo Nehemiya ndi amene ankayang’anira ntchitoyi. Anthu ena amene anathandizanso pa ntchitoyi anali ana aakazi a kalonga wa chigawo china cha Yerusalemu dzina lake Salumu. (Neh. 3:12) Iwo anadzipereka kuti agwire ntchito yooneka ngati yonyozeka. Masiku ano, timayamikiranso kwambiri alongo amene amathandiza pa ntchito ya zomangamanga.

AKAZI OOPA MULUNGU M’NTHAWI YA ATUMWI

15. Kodi Mulungu anapatsa Mariya mwayi uti?

15 Panalinso akazi ena amene Mulungu ankasangalala nawo n’kuwapatsa mwayi wapadera nthawi ya atumwi isanafike komanso itafika. Mmodzi mwa iwo anali Mariya. Iye ali pa chibwenzi ndi Yosefe, anapezeka kuti ndi woyembekezera mwa mphamvu ya mzimu woyera. N’chifukwa chiyani Mulungu anamusankha kuti akhale mayi wa Yesu? Ayenera kuti anamusankha chifukwa cha makhalidwe ake abwino amene akanamuthandiza kulera bwino mwana wake wangwiro mpaka atakula. Unalidi mwayi waukulu kwambiri kukhala mayi wa munthu wofunika kwambiri kuposa wina aliyense amene anakhalapo.—Mat. 1:18-25.

16. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakomera mtima akazi?

16 Yesu ankakomera mtima kwambiri akazi. Mwachitsanzo, anathandiza mkazi wina amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12. Mkaziyo analowa m’khamu la anthu n’kudzera kumbuyo kwa Yesu kuti agwire malaya ake. M’malo momudzudzula, Yesu ananena mokoma mtima kuti: “Mwanawe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere, matenda ako aakuluwo atheretu.”—Maliko 5:25-34.

17. N’chiyani chinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E.?

17 Panali akazi ena amene ankatumikira Yesu ndi atumwi ake. (Luka 8:1-3) Pa Pentekosite mu 33 C.E., anthu pafupifupi 120 analandira mzimu woyera mozizwitsa ndipo m’gululi munali amuna komanso akazi. (Werengani Machitidwe 2:1-4.) Zimenezi zinali zitanenedwa kale m’mawu a Yehova akuti: “Ndidzatsanulira mzimu wanga pa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera . . . ndidzatsanuliranso mzimu wanga pa antchito anu aamuna ndi aakazi.” (Yow. 2:28, 29) Zimene Mulungu anachita pa tsikulo zinasonyeza kuti iye wasiya Aisiraeli opanduka ndipo wayamba kudalitsa amuna ndi akazi omwe anali m’gulu la “Isiraeli  wa Mulungu.” (Agal. 3:28; 6:15, 16) Akazi ena achikhristu omwe ankalalikira anali ana aakazi anayi a mlaliki Filipo.—Mac. 21:8, 9.

“KHAMU LALIKULU” LA AKAZI

18, 19. (a) Kodi Mulungu wapereka mwayi uti kwa amuna komanso akazi? (b) Kodi wamasalimo ananena chiyani za akazi amene akulengeza uthenga wabwino?

18 Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, amuna ndi akazi ena ankafunitsitsa kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Iwo ndi amene anayamba kugwira ntchito imene Yesu analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14.

19 Ophunzira Baibulowa anali ochepa koma pano padzikoli pali Mboni za Yehova pafupifupi 8,000,000. Anthu ena oposa 11,000,000 amafuna kuphunzira Baibulo ndipo anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. M’mayiko ambiri anthu ochuluka amene amafika pa Chikumbutso amakhala akazi. Pa dziko lonse pali atumiki a nthawi zonse oposa 1,000,000 ndipo ambiri mwa iwo ndi akazi. Mulungu waperekadi mwayi kwa akazi okhulupirika kuti akwaniritse mawu a wamasalimo akuti: “Yehova wapereka lamulo, ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.”—Sal. 68:11.

Pali “khamu lalikulu” la akazi amene akulengeza uthenga wabwino (Onani ndime 18 ndi 19)

AKAZI OOPA MULUNGU ADZADALITSIDWA KWAMBIRI

20. Kodi tingachite bwino kuphunzira nkhani ziti?

20 Panopa sitingathe kufotokoza za akazi onse okhulupirika amene anatchulidwa m’Baibulo. Koma tonsefe tingawerenge za akazi amenewa m’Mawu a Mulungu komanso m’mabuku athu. Mwachitsanzo, tingaganizire za kukhulupirika kwa Rute. (Rute 1:16, 17) Komanso kuwerenga nkhani ya Esitere kungalimbitse chikhulupiriro chathu. Kuphunzira za anthu ngati amenewa pa kulambira kwathu kwa pabanja kapena tikamaphunzira patokha kungatithandize kwambiri.

21. Kodi pa nthawi ya mavuto, akazi ena asonyeza bwanji kuti ndi odzipereka kwa Mulungu?

21 N’zoonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchito yolalikira imene akazi achikhristu akugwira ndipo akuwathandiza pa nthawi ya mavuto. Mwachitsanzo, iye anathandiza akazi ena kuti akhalebe okhulupirika pa nthawi ya maulamuliro ankhanza monga ulamuliro wa chipani cha Nazi. Pa nthawi imeneyo, ambiri ankazunzidwa ndipo ena anaphedwa chifukwa chomvera Yehova. (Mac. 5:29) Masiku anonso, alongo athu limodzi ndi Akhristu ena onse akusonyeza kuti ali kumbali ya ulamuliro wa Mulungu. Tinganene kuti Yehova wagwira dzanja lawo lamanja ndipo akuwauza zimene anauza Aisiraeli akale kuti: “Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.”—Yes. 41:10-13.

22. Kodi tikuyembekezera madalitso ati?

22 Posachedwapa, amuna ndi akazi oopa Mulungu adzakonza dziko lapansili kuti likhale paradaiso ndipo adzathandiza anthu ambirimbiri oukitsidwa kuti aphunzire zolinga za Yehova. Koma padakali pano, kaya ndife amuna kapena akazi, tiyeni tipitirize kutumikira Yehova “mogwirizana.”—Zef. 3:9.